24/08/17

Written by  Newsroom

Anthu aku Lilongwe akhala mwa mantha
Anthu a mdera la Senior Group Malembe kwa Chitukula mboma la Lilongwe akukhala mwa mantha.

24
August

Nkhaniyi ikuti tsiku lina anthu a mderalo anaona ngati malodza mwana wa chaka chimodzi ndi miyezi isanu ndi iwiri atasowa mosadziwika bwino. Pa tsikulo kamvuluvulu anaomba mwadzidzi mderalo ndipo kumapeto kwa mphepoyo mwana wapa banja lina anasowa mosadziwika bwino. Apa anthu a mderalo komanso omwe anaona izi zikuchitika anazindikira msanga kuti kamvuluvuluyo ndi amene anasowetsa mwanayo m’matsenga. Pa chifukwachi anthu mderalo kudzera mwa Senior Gulupu wao anakanena nkhaniyi ku polisi. Komabe ngakhale izi zili chomwechi, anthu ena komanso mikoko yogona yalangiza a Gulupuwo kuti mpofunika kupondaponda mwa Sing’anga kuti athane ndi yemwe wachita zaupanduzo. Pakadali pano a Gulupu a deralo anenetsa kuti achita china chili chonse chotheka kuti apeze zoona za nkhaniyi ndipo pali malipoti woti sing’anga wina wafika kale mderalo kuti agwire ntchito yake yofuna-funa mwanayo. Pamene timalandila nkhaniyi anthu ambiri mderalo makamaka amai ndi ana akukhala mwa mantha kwambiri chifukwa cha nkhaniyi.

 

Mwamuna wina atandala ku tchire
Mwamuna wina mdera la Chimwala ku Mangochi akukhalira kutandala ku tchire mphekesera itamupeza kuti akumufuna-funa. Nkhaniyi ikuti mwamunayo anakakwatila mdera lina mbomalo ndipo mkazi wakeyo amakhala ngati mtengwa pa khomopo. Miyezi ingapo yapitayi banjalo linali ndi chimwemwe chifukwa choti mkaziyo anapeza pathupi zomwe zinabweretsa chisangalalo chachikulu pa banjapo. Pa chifukwachi maiyo anayamba sikelo koma masiku ochira atakwana pathupi pa maiyo panasowa pamodzi ndi mafailo omwe akuchipatala zomwe zinadabwitsa anamwino komanso maiyo. Maiyo anabwerela kunyumba akulira koma anagwira pakamwa atakazindikiranso kuti ngodwala ali kunyumba. Apa banjalo linagwira pakamwa ndipo posakhalitsa linabwerelanso ku chipatala kuja koma chomvetsa chisoni manesi anauza anthuwo kuti pathupi sipakuoneka komanso ngakhale mafile awo amapitilirabe kusowa. Ali mnjira mwamunayo analira ngati kwagwa maliro mpakana anthu ena anakhamukira pa malopo. Koma atafika kunyumba pathupipo panapezekanso ndipo apa zachititsa kuti banjalo lisowe mtengo ogwira komanso kuti ligwidwe ndi mantha aakulu. Koma chodabwitsa anthu apa banjapo sakuonetsa kukhudzika ndi nkhaniyi zomwe zachititsa kuti akuchikazi ayambe kukaikira anthuwo kuti mwina nkutheka kuti izi zikuchitika m’matsenga. Akuchikazi m’malo mwake aophyeza mwamunayo kuti athana naye ngakhale zikuonetsa kuti mwamunayo sakukhudzidwa ndi zaupandu zili zonse. Pakadali pano mwamunayo akukhalira kutandala ku tchire poopa akuchikazi pamene ena ati mwamunayo wapita mdziko la Mozambique kukafunafuna singanga oti awathandize.

 

Awona polekela
Mwamuna wina mdera la Chilooko mboma la Ntchisi waona polekera. Nkhaniyi ikuti mwamunayo wakhala akuba mbeu za anthu ambiri mderalo m’matsenga koma palibe munthu ndi m’modzi yemwe anakwanitsa kugwira mwamunayo. Paja pali mau oti lafote limakwana masiku apitawo mwamunayo anakalowa munda mwa banja lina ndikuyamba kuba chimanga. Ali mkati mosakaza chimangacho eni mundawo anafika mwadzidzi ndipo mwamunayo atamva kulankhula komanso mtswatswa wa anthu anasanduka chinjoka cha mamba. Koma eni mundawo pokhala kuti nawonso ndi akatakwe pa zitsamba sanachite mantha ndipo m’malo mwake anayamba kukhapa njokayo koma njokayo inayankhula kuti musandiphe ndine munthu mpakana kuitembenuzanso kukhala munthu. Apa ndeu ya fumbi inabuka pakati pao uku akuitana anthu a mderalo ndipo posakhalitsa anthu ambiri anakhamukira kumundako. Anthuwo mogwirizana ndi eni mundawo anamenya kolapitsa mwamunayo mpakana kumukwakwazila kwa nyakwawa ya mderalo aku akulira ngati kwachitika maliro. Ku bwalo la nyakwawa mwamunayo anaulura za sing’anga yemwe wakhala akumupatsa zitsamba komanso kupepesa ponena kuti wakhala akubera anthu a mderalo kwa zaka zambiri. Pamene timalandila nkhaniyi mwamunayo amulipitsa chindapusa cha mbuzi zisanu ndipo amuchenjeza kuti akadzayambilanso adzaona chomwe chidameta nkhanga mpara. Pakadali pano mwamunayo wanenetsa pa gulu la anthu kuti akufuna kuti mzimu wa Ambuye umukhudze ndipo wachimina ponena kuti sadzayambilanso ndi khalidwe lake lobera anthu m’matsenga.

 

Ayenda zamadulira kamba ka manyazi
Tili m’boma lomwelo la Lilongwe anyamata ena atatu ku Area 25 akukhalira kuyenda njira zodula komanso kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi. Anyamatawo amagwira ntchito pa kampani ina yotchuka ndipo amalipidwa ndalama zabwino ndithu m’ma dollar. Anyamatawo omwe amayendera limodzi komanso kumwera limodzi mowa wa midoli dzana laliwisili atalandila malipilo awo anakapapira mowawo ngati kulibe mawa. Anyamatawo analedzebwa kwambiri mpaka kunawachera ndipo onsewo anadziipisila. Anthu ena owadziwa omwe anali atalawira ku ntchito zao anapeza anyamatawo ndipo anakauza abale komanso akazi awo. Abale awowo anakwanitsa kukwakwaza anyamatawo mpakana kukawasambitsa ndipo mowawo utawakungunuka anawafotokozera za nkhaniyi. Anyamatawo panopa ayamba asiya kupita ku ntchito komanso ku malo omwela mowa pochita manyazi ndi nkhaniyi. Pakadali pano zikumveka kuti banja la m’modzi mwa anyamatawo latha mkazi atalusa kuti wamuchititsa manyazi.

 

Get Your Newsletter