29/08/17

Written by  Newsroom

Katswili oyimba za uzimu achita manyazi
M’modzi mwa akatswili oimba nyimbo za uzimu ku Blantyre akuyenda wela-wela ngati nkhuku yogwela mvuwo chifukwa cha manyazi.

29
August

Nkhaniyi ikuti lero chaku masanaku oimbayo analowa m’sitolo ina pafupi ndipa Nandos mu mzindawo ngati m’modzi mwa anthu ofuna kugula zinthu zomwe akuzisowa. Koma ali msitoloyo iye anapakila zinthu zina mkati mwa zovala zake. Zinthu zina zomwe anatenga nkuphatikizapo juice. Koma pomwe amati adzituluka ogwila ntchito anadabwa kuona momwe amayendela. Ndipo mkulu woyang’anira ogulitsa msitoloyo anapempha achitetezo pa malopo kuti amuchite chipikisheni maiyo. Apo maiyo anadziwiratu kuti madzi achita katondo. Pa chifukwa-chi anayamba kuchondelera anthuwo kuti amusiye ndipo akasiya pa lumali zinthu zomwe anabazo. Koma achitetezo sanaimve ndipo adamuchitadi chipikisheni ndipo anali odabwa kuona kuti ndi munthu otchuka koma waonetsa mtima wakuba zomwe anati aliyense sadamvetse. Pa chifukwachi, anthu anayamba kumukuwiza atamva kuti angomuuza kuti alipile juice yekha yemwe anabayo azipita ngakhale ena amati amukhaulitse pomuthila makofi awili okha. Pakadali pano, anthu ena ati zomwe wachita katsiwiri woimbayo mkunyozetsa akubanja lakwao ndipo zikupereka chiopsyezo kuti anthu ambili akamva za nkhaniyi ataya naye chikhulupililo.

Akhumudwitsa mamuna
M’boma la Mulanje kwa Gulupu Mkwaila mdera la Mfumu Mkanda tsikana wina wakhumudwitsa mwanuna. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli mtsikana wina yemwe ali ndi mwana m’modzi ndipo amakhala ndi abale ake ena pamudzipo. Koma ngakhale kuti sagwiritsa ntchito bwino malo olima aakulu omwe makolo ake adamusiila, chaka chino iye wakolola chimanga chokwana matumba asanu ndi limodzi. Panthawi yomwe amakolola chimangacho nkuti ali mbeta. Koma kamba koti ndiwodziwa kusamba anachita mwawi kupeza mwamuna omanga naye banja. Koma pomwe mwamunayo amafika pakhomopo mtsikanayo anabisa matumba a chimanga aja pansi pa malata owe anali m’nyumbamo. Ngakhale adabisa chotere matumbawo mwamunayo nkuti atawaona kale. Pa chifukwa-chi nthawi yonse mwamunayo amakhala pakhomopo, amadalila kuti savutika ndi njala. Koma patapita miyezi iwiri ali pa banjapo, mwamunayo anadabwa kuona kuti matumbawo pamalopo asowa mnyumbamo. Koma mwamunayo atafunso m’modzi wa ana pakhomopo, waulula kuti mkaziyo wagulitsa mozembela mwamuna wakeyo kuti nayenso aonetse chamuna pakhomopo. Pakadali pano banjalo laweyeseka chifukwa cha nkhaniyi.


Auka kwakufa

Anthu okhala mdela la Matale kwa Mphambala mboma la Ntcheu akukhala mwa mantha zitadziwika kuti mnyamata wina yemwe adamwalila mchaka cha 2012 watulukilanso m’mudzimo. Nkhaniyi ikuti m’nyamata wina adamwalila pa ngozi yapa msewu kumeneko galimoto itamuomba pamene adali akuthamangitsa kalulu ku thengo lina mbomalo. Pa nthawiyo makolo pamodzi ndi eni mbumba adayendetsa mwambo wonse wamaliro ndipo zonse zinatha bwino mpaka kusesa. Komabe ngakhale achibale sankamvetsa momwe zidakhalila malilowo adakaika kumanda mpaka kufika poiwala ndipo amalimbikila kupemphela. Koma chodabwitsa mchkauti Lamulungu lapitali m’nyamatayo wapezeka mderalo ali moyo koma ali ndi zikhadabo zitali zitali komanso tsitsi lambiri losapesa. Achibale amunthu-yo yemwe akungoti waukayo panopa zamveka kuti atsimikiza kuti ndi m’bale waodi yemwe adamwalila galimoto itamuomba. Ngakhale achibale ayesera kumufunsa zakomwe anapita kuchokera mchaka cha 2012, akuti akulephera kufotokoza zomveka. Koma akuti walankhula mau ena omvekapo omwe akutsimikiza kuti komwe wachokako kwatsala mnyamata m’modzi yemwe akuvutika ndi njala ndipo walephela kuchoka kumalowo chifukwa adavulala mwendo kokusa ng’ombe. Padakali pano, makolo amnyamatayo ati apitiliza kupemphera pofuna kuyamika Mulungu chifukwa chobweretsa mwana wawo ndi moyo.

 

Mpingo usokonekela
Mpingo wina wapasuka ku Mlomba mdera la mfumu Juma , m’boma la Mulanje. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli mipingo yambiri yomwe imaziimilira pa yokha pa nkhani za chuma. Koma watumiza nkhaniyi wati ampingo umodzi mwa mipingoyo kumeneko akhala akuchita matama polankhula mwathamo kuti iwo amayendetsa bwino mpingo wawo kuphatikizapo chuma cha mpingowo. Ngakhale nthumwi zaku likulu la mpingowo zakhala zikuyamika atsogoleriwo kuti amakwanilitsa ma target omwe amawapatsa pa chaka. Izi zinapereka mangolomela kwa atsogoleriwo kukweza mtulo womwe mamembala ake amapereka kuchokera pa 1-thousanda Kwacha kufika pa 2000 kwacha. Ngakhale akhrisitu pa mpingowo-po anadandaula zakukwera kwa mtulowo atsogoleriwo anakanitsitsa kuti nkofunika kuti anthu pa kachisipo azipereka zokwanira. Koma akhirisituwo ati atopa kwambiri ndi zomwe zikuchitika pa mpingowo ndipo pakadali pano, anthu ambiri atuluka mu mpingo ndipo alowa mipingo ina yomwe siinakweze mtulo omwe akhiristu ake amapereka.

Get Your Newsletter