01/09/17

Written by  Newsroom

Alandidwa maliro
Ana a banja lina m’boma la Thyolo anagwira njakata atawalanda maliro a atate awo pa chipatala china m’boma la Blantyre.

01
September

Chomwe chinachitika nchoti bambo wa anawo anakwatira ku Thyolo komwe amakhala ku chikamwini. Mwatsoka anayamba kudwala ndipo matenda atakula anamugoneka pa chipatala china mu mzinda wa Blantyre koma uthenga utapita kwa abale ake ku Ntcheu palibe ndi m’modzi yemwe anakazonda matendawo. Mwatsoka bamboyo anamwalira. Pamenepa anawo anatumiza uthenga wa imfayo kumudzi kwawo ku Thyolo ndipo anthu anali tcheru kumudziko pofuna kulandila malirowo. Koma mwadzidzidzi ku chipatalako kunatulukila achibale a mwamunayo omwe anauza anawo kuti Malemuwo apita nao kwawo ku Ntcheu. Apatu chipwilikiti chinabuka ndipo anthuwo sanagwirizane mpaka akuchimunawo ananyengerela dalaivala wina yemwe ananyamula thupi la malemuyo kukabisala kwa Kameza. M’modzi mwa anawo anayesera kufufuza komwe inayima galimotoyo koma sanaipeze. Kenaka anangoganiza zotsatira ku Ntcheu komweko ndipo anakapezadi malirowo atafika kale. Pakadali pano ana a malemu-yo ati ndi okhumudwa kwambili ndi zomwe anachita achibalewo kamba koti nthawi yomwe malemuwo amadwala sanapite kukazonda matendawo.

Anyanyalilidwa maliro

Tili pa nkhani ngati yomweyi Nyakwawa ina ayinyanyalila maliro ku Soche m’boma la Blantyre. Chomwe chinachitika nchoti mwamuna wina amadwala ndipo kenaka anamwalira. Malemu-yu anamanga nyumba yake m’mudzimo ndipo wakhala zaka makumi atatu. Mkuluyu anawuza ana ake, akulu akulu a mpingo komanso nyakwawa ya m’mudzimo kuti akadzagonela mkono adzamuyike mdera lomwelo. Koma chokhumudwitsa nchoti mkuluyu atamwalira, achibale anafika kuchokera ku Mulanje kuti adzanyamule thupi la malemuwo. Pamenepa anthu pasiwapo anamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti anthuwo awona zakuda ngati angapitilize maganizo oterewo. Izi zinachititsa kuti achibalewo anyanyale pasiwapo ndikusiya mwambo onse m’manja mwa nyakwawayo. Mwambowo unachitika bwino lomwe motsogozedwa ndi nyakwawayo koma anthu ambili ati ndi okhumudwa ndi zomwe achita achibalewo pokana kuyendetsa nao mwambo wa malirowo, chonsecho anthu m’mudzimo amafuna kulemekeza zofuna za malemu mbale wawoyo zomwe ananeneratu ali moyo.

 

Banja litha kamba komenya mamuna
Mai wina ku Zalewa manja ali ku nkhongo banja lake latha chifukwa chomenya mwamuna wake ku malo obisika. Nkhaniyi ikuti mai-yo wakhala pa banja ndi mwamunayo kwa zaka zambiri mpaka kukhala ndi ana anai . Koma chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga nchoti mwamunayo amagwira ntchito ku kampani ina mderalo ndipo pa zifukwa zina ntchito-yo idatha. Pamenepa mai-yo anayamba kulalatila mwamunayo kuti akungokhala manja lende. Kenaka mai-yo anapempha mwamuna wake-yo kuti adzichita bizinesi yogulitsa mondokwa. Poyambilira zinthu zimayenda bwino koma kenaka mkaziyo analowerela mpaka kumabwera mochedwa pakhomopo. Zikumveka kuti nthawi zina amakagona komwe anapita kukatenga katunduyo zomwe zinachititsa mwamunayo kukayikila khalidwe la mkaziyo. Tsiku lina mkaziyo anatengana ndi mwamuna wina nkukagona ku malo ena ogona anthu apaulendo ndipo m’mene amachita izi nkuti anthu ena akuwaona. Anthuwo anakatsina khutu mwamuna wake ndipo atafika kumaloko sanakhulupilire atamupeza mkazi wakeyo atakolekana miyendo ndi mwamuna wakubayo. Pamenepa mwamuna wakeyo anangofikila kumenya mwamuna wakubayo ndipo mkaziyo anathawa . Koma atafika ku nyumba mkaziyo anayamba kulalata ndipo kenaka anagwira mwamuna wakeyo nkumucheka ku malo obisika. Anthu ena achifundo anatengela mwamunayo ku chipatala china komwe akulandila thandizo. Pakadali pano mwamunayo walamula mkaziyo kuti achoke pa khomopo ndipo anthu ambiri akumuseka kamba kopasula banja lake chifukwa chokonda ndalama.

 

Akunthidwa kamba kokuba ku maliro

Mkulu wina kwa Kalolo m’boma la Lilongwe amuthibula mpaka thapsya kamba kakuba nyama ku Maliro. Chomwe chinachitika nchoti m’modzi mwa mai wina yemwe amachita malonda pa sitolo za m’deralo anamwalira. Mwa mwambo pasiwapo anaphika zakudya koma anthu amayenera kudya akachoka ku manda. Apa Mkuluyo yemwe ndi otchuka m’deralo anatuluka msanga ku mandako ndikukalowa mnyumba yomwe munali chakudya ndikukhutula ndiwo zonse mu mphika ndikuthira mu jumbo. Koma akutuluka mnyumbamo anangoti gululu ndi m’modzi mwa anamfedwa yemwe anaphaphalitsa mafunso mkuluyu mpaka kusowa choyankha. Apa namfedwayo anakuwa ndipo anthu onse omwe amachokera ku mandako anakhamukira ku nyumbako komwe anapeza mkulu wakubayo. Anthuwo anamuthibula mkuluyo mpaka magazi kukamwa uku akupepesa kuti analibe ndiwo ku nyumba kwake. Pakadali pano nyakwawa ya m’mudzimo yalamula kuti mkuluyo alipire chindapusa cha mbuzi ziwiri kamba kakhalidwe lake loipalo.

 

Get Your Newsletter