08/09/17

Written by  Newsroom

Mai wina achimina ku Mulanje

Mai wina wachimina ku Mwanamulanje mdera la Chambe m’boma la Mulanje.

08
September

Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko kuli banja lina lomwe mkazi wapabanjalo amakhalira mphanthi kamba koti mwamuna wake amakhalira kugona mmabala ndi amai komanso kupapira bibida. Ndipo mkaziyo wakhala akumusaka mwamuna wakeyo. Ndipo tsiku lina mkaziyo adamvetsedwa kuti mwamuna wake walowa ku mchipinda china ndi mmodzi wa amai omwe amagulitsa mowa pam malo ena. Apo mtima uli mmwamba anathamangira ku malowo kuti akagwire mwamuna wakeyo. Atafika ku balako anayamba kusunzumira mzipinda zogona kuti aone komwe mwamuna wake anali pantahwiyo. Koma mwangozi anagwera mchimbuzi china chomwe anakumba kuseli kwa zipinda zogona amai ogulitsa mowayo. Mai-yo anayamba kufula ngati mwana kamba ka ululu atathyola mwendo. Koma zomwe zimachitika izi nkuti mwamunayo sanali nchipinda chogona ndi mkazi wina aliyense. Mwamunayo ndi anzake omwe amamwa nao mowa anathamangira kukapulumutsa maiyo. Pakadali pano maiyo wati sadzasatiranso mwamuna wake kumowa. Koma anth uena adzuzulka mwamunayo chifukwa chomwa mowa mpaka pakati pausiku.

 

Mkulu wa mpingo amuzungulitsa nkachisi
Mkulu wapingo wina amuzungulitsa nkachisi yomwe amapempheramo kwa Kalolo m’boma la Lilongwe. Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko kuli abambo awiri ochezera limodzi ndipo winayo ndi mkulu wampingo pomwe winayo amagfulitsa mbeu pamalopo. Ndipo masiku apitawo mkulu wampingo anapangana ndi mkazi wamzakeyo kuti kagawane chikondi ku malo ena. Koma momwe amafika kumalowo anthu ena adawawona ndipo adatsina khuthu mwini mkaziyo. Mosakhalitsa mwini mkaziyo anafika pamalopo koma mozemba. Ndipo adangogwira kukamwa atapezelera mkazi wakeyo ali nchikondi ndi mzake weni-weni yemwenso ndi mkulu wa mpingo pa tchalichi lina mderalo. Atafuula anthu ena pamudzipo anafika kudzaona malozawo. Anthuwo anagwira mwamuna wakubayo pamodzi ndi mkaziyo onse ali mbulanda ndikukawazungulitsa tchalichi chomwe mwamunayo amatsogolera. Pakadali pano mabanja awiriwo aweyezeka komanso kuti mwamunayo amuimitsa kutumikila mu mpingo wake kamba ka nkhaniyo.

 

Bambo wina akhala mwa mantha

Bambo wina akukhala mwa mantha kwa a gulupu a Muwotcha mdera la Katchenga m’boma la Balaka. Nkhaniyi ikuti kumeneko kuli bambo wina yemwe anakwatira pa mudzi wina ndipo ali ndi ana asanu ndi awiri. Iye ndi mkazi wake amakhala bwino maka polimbikitsa ana awo pankhani yamaphunziro. Koma miyezi yapiyo banjalo linadabwa kumva kuti mwini mbumba yemwe njondayo yakwatira wakhomera unkhoswe mmodzi wa ana asikana abanjalo. Koma pamene bamboyo anakafunsa mwini mbumbayo za nkhaniyo maka poona kuti mwana ngwazaka khumi ndi zinayi zokha komanso amalimbikira sukulu ndipo anali form thu. Apo mwini mbumbayo analalatira bamboyo ndikumuudza kuti iye kwa kwake ndi kubereka basi ndipo asalowelere mbumba ya weni. Mwini mbumbayo wachenjezanso njondayo kuti ikapitilira kufunsa za ukwati wa mwana wake iwona polekela. Pakadali pano njondayo ikukhala mwa mantha komanso yati itengera nkhaniyi kumabungwe omenyera ufulu waana mm’bomalo kuti akamuthandize.

 

Amai ena asaka amuna kuti awapasile matenda

Amai ena alusa kwa Nasiyaya m’boma la Phalombe. Mtolankhani wathu wati kumeneko kuli amai ena akusakasaka amuna omwe ali ndi kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi kuti awaptsire. Amai ati akhala akudandaula maka chifukwa choti anzao omwe ali ndi ka chilombo ka HIV- ka akulandira thandizo la zinthu zosiyana-siyana monga nyemba, ufa, mafuta komanso ndalama zomwe mabungwe akupereka kwa anthuwo kuti ziziwathandiza pamoyo wawo. Izi zachititsa kuti amuna omwe alibe kachilombo aziwakana zibwenzi komanso mabanja kamba koti ati akaziwo samapindula kali konse akawalola amunawo. Mikoko yogona mderali yaima mitu chifukwa ambiri mwa amai mderalo akumapita mmalo omwera mowa ndi kumagonana ndi amuna omwe awapeza mosadziteteza ndi cholinga choti atenge kachilombo ka HIV. Koma amai omwe sakuwafunsira ati aponda ponda kuti apeze mtela wokopera amuna kuti mpaka awafunsire ndikuwapatsa kahilomboko. Pakadali pano, mikoko yogona yati ipemphja mabungwe omwe akulimbana ndi kufala kwa kachilombo ka HIV mdziko muno kuti adziwitse anthu mderalo zakuopsya kwa kachilombo ka HIV.

 

Alandidwa njinga ndi lamya

Mphunzitsi wina waona mbonaona atamulanda njinga komanso lamya ya mmanja kwa Chigalu m’boma la Blantyre. Nkhaniyi ikuti mphunzitsiyo anapalana ubwenzi ndi mai wina mderalo yemwenso ali ndi mwana wamkazi yemwenso ndi wophunzira wa standard 8 pa sukulu ina kumeneko. Apo mphunzitsiyo adanyengerela mwanayo kuti achite naye zachisembwere ndipo amuthandiza kuti akhonze mayeso ndikupita ku sekondale yapamwamba kamba mphunzitsiyo ndi amene amachonga mayesowo. Apo ubwenzi ndi mwanayo unayamba ndipo anayamba kumasukilana ndi bamboo akewo. Ndipo tsiku lina awiriwo anagwirizana zokumana pa tchire lina kumeneko. Koma pomwe amalowa patchirepo anthu ena adawawona ndipo adatsina khuthu mai amwanayo omwenso ndi ndi chibwenzi cha njondayo. Apo maiyo anamema gulu la mmudzi kuti likamuonetse malodzawo. Ndipo atafika patchirepo anthuwo adapeza mphunzitsi ndi mwanayo ali bwamuswe kugawana chikondi. Atampanikiza ndi mafunso mtsikanayo adaulula kuti mphunzitsiyo adamunmyengerera kuti amuthandiza kuti akhonze mayeso. Apo anthu okwiyawo sanachitire mwina koma kuloanda mphunzitsiyo njinga komanso lamya ya mmanja. Pakadali pano mphunzitsiyo akuyenda zamadulira.

Get Your Newsletter