10/09/17

Written by  Newsroom

Mtsikana wina ali m'manja mwa a polisi

Mtsikana wina ali mmanja mwa a polisi kwa gulupu Namalima mdera la Senior Authority Ngwerero m’boma la Zomba.

10
September

Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumene kuli mtsikana wina yemwe ngwachichepere koma samvera makolo ake. Ngakhale makolo akewo akuyetsesa kumtumiza kusukulu kuti akakonze tsogolo lake iye wakhala akuchitira mwano makolowo. Mwazina mtsikananayo wakhala akutandala mu phala za anayamata komanso kupezeka mmalo osayenera monga mmabala komanso malo otchovela mjuga. Ndipo masiku apitawo mtsikanawo anakolowera mwamuna wina ndi kumakhala naye ngati banja. Koma chifukwa ndiwachichepere anthu anakatula nkhaniyi kupolisi kuti alowererepo. Apo apolisiwo sanachedwe koma kumuchotsa mtsikanayo kubanjako ndi kumutsekera mchitokosi cha polisi pomwe akuyembekezera kuti akamusiye kumalo osamalirako ana pofuna kuti alandire uphungu kamba konyala-nyaza malangizo amakolo ake. Pakadali pano mikoko yogona mderalo yayamika makolo a mwanayo kamba kolimbikitsa kuti apitilize sukulu.

 

Mwamuna wina aganizilidwa kuti waphedwa
Mwamuna wina akumuganizila kuti waphedwa ndi anthu okwiya kamba ka zomwe wakhala akuchita ku Banana ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre. Malinga ndi amene watitumizila nkhaniyi anthu omwe amamwa mowa mdela la Banana ndi madela ena omwe ali pafupi ndipomwe pali malo ogona anthu apa ulendo ku Bangwe-ko akhala akukumana ndi zamtopola zosiyanasiyana kuchokela kwa mkuluyo yemwe sakudziwika kwao mpaka pano. Malinga ndi wotumiza nkhaniyi mkuluyo yemwe anali wachinyamata amavala ngati mkazi komanso kuphoda kumaso mochititsa kaso mpaka kufika pomavala wigi. Akatelo amapita m’malo osiyanasiyana omwela mowa komwe nthawi zambili amuna otengeka amapita naye mchipinda poona ngati njole koma mwa tsoka amawatembenukila ndikuwalanda china chilichonse nkuthawa. Pa chifukwa-chi kwa nthawi anthu akhala akumangomuwerenga kuphatikizapo atsikana oyenda yenda omwe anati amakhala akuwaipitsila mbili yao. Tsono dzulo madzulo mkuluyo anachitanso chimodzimodzi mpaka anakalowa mchipinda chogona anthu apa ulendo koma panthawiyo nkuti anthu akumuona. Kenaka kufika mchipinda mwamunayo anafunza amene amati mkaziyo kuti amasuke koma amakana ndipo apa winayo anatuluka pang’ono ngati akukataya madzi komwe anakamema anthu ena. Kufika mchipindamo akuti anagwilizana zomuvula zovala zomwe anavala mpakana kapanti ndipo zinadziwikadi kuti anali wamwamuna. Pamenepa, akuti anthu ambili anayamba kumuphika mpaka kumusiya ali thapsya. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi momwe amafika m’manja mwa achitetezo zikuonetsa kuti anali atasiya kale kupuma. Panopa, kwao kwa munthuyo sikukudziwikabe.

Anamizila mzake kuti waba

Tili mu mzinda wa Blantyre womwewo koma mtauni ya Limbe mai wina wochita malonda wogulitsa nsomba pa msika wina amudzudzula chifukwa chonamizila nzake wina kuti wamubela ndalama. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi mayi wina anapempha nzake wina kuti amuthandize kulowa gulu ndipo zinathekadi. Pa chifukwachi anatenga 3-thousand Kwacha yokapereka ku gululo. Koma mosakhalitsa anauza nzake uja kuti kugulu amusasa ndipo akuyenela kumubwezela ndalama yake. Koma m’malo mobweza nsanga ndalama ija kwa nzake uja zimakanika ndipo amangomuzemba. Mwa zina, mayiyo mpaka anakwanitsa kupeza ndalama yochuluka koma analepherabe kupereka 3-thousand kwa mai nzake uja. Tsiku lina amai aja omwe onse amagulitsa nsomba zouma anakumana mu msika ndipo apa panabuka chipwilikiti pamene mai wina auja amauza nzake uja kuti amupatse ndalama yake. Komabe zikuonetsa kuti mai yemwe adatenga ndalama nzake uja anali wachipongwe chifukwa anauza nzakeyo kuti alibe ndalama ili yonse. Amuna ena anafika kudzauza mayiyo kuti apatse nzakeyo ndalama pofuna kuthetsa mkangano koma anati alibe. Koma pokanganapo mai uja anataya nsalu yake pa chipata cha msikawo mkumapita kwao. M’mawa pobwela anadzauza akulu akulu kuti nzakeyo wamubela ndalama yokwana ten –thousand Kwacha yomwe anaimanga pa nsalu chonsecho amanena kuti alibe ndalama pokangana. Pa chifukwa-chi akulu akulu ena ataikhalilana nkhaniyi zaonetsa kuti mayiyo akunama ndikuti akufuna kuipitsa mbili ya nzakeyo kuti asabweze ndalamayo. Pakadali pano, nkhaniyi aikokela kubwalo lina.

 

Athawa pakhomo kamba ka manyazi

Bambo wina wathawa pa nyumba yake anthu atazindikira kuti anazikhweza kamba ka mavuto a m’banja ku Mtandire mdera la Njewa m’boma la Lilongwe. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli mkulu wina yemwe m’mbuyomu anali pa banja la ulemu. Banjalo Mulungu adalidalitsa ndi ana atatu ndipo limayenda bwino. Koma kamba koti mwamunayo ngwa mchiuno ndipo samakhutira ndi mkazi wakeyo iye anapalananso ubwenzi wamseli ndi mkazi wina. Koma ubwenziwo utafumbila njondayo inapilikitsa mkazi wake wakale uja ndikukwatira mkazi watsopanoyo. Koma banja latsopanolo silinakhalitse kamba koti mwamunayo wati sakukukhutila ndi zochita za mkazi watsopanoyo maka ku chipinda. Ndipo masiku apitawo njondayo inalandula mkaziyo kuti apakile katundu wake kuti azipita kwao m’boma la Karonga. Koma madzulo atsikulo pomwe njondayo inafika pakhomopo inapeza mkaziyo asanachoke. Apa mwamunayo sanachitile mwina maka atadzindikira kuti mkaziyo wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sachoka pakhomopo. Ndipo pa chifukwa-chi anatenga chingwe ndi kudzimangilila ku denga la nyumba yake. Koma mkaziyo ataona kuti mwamuna wake ali lende ku tsindwi la nyumba yakeyo anaitana anthu kudzapulumutsa. Panopa, mwamunayo ataona kuti akanafa ndikuti mwina apolisi amugwila wathawa pa khomopo ndipo komwe wapita sikukudziwika.

 

Mkulu wachipembezo alodzedwa dzala

Mkulu wina wachipembezo akumuloza-loza chala mdera la Ngokwe m’ boma la Machinga. Nkhaniyi ikuti anyamata ena okondana awiri analowa mchipinda china momwe amaontseramo kanena. Kenaka pamalopo panafikanso mkulu wachipembedzo china yemwe anakhala yekha pa mpando. Koma pa nthawi-yo nkuti anyamata awiri aja akuzizilitsa kukhosi pamene amakonkha mkalabongo. Apa mkulu wachipemebzoyo anapempha anyamatawo kuti amugawireko zakumwa zomwe amamwazo. Anyamatawo anakana kamba koti ati zinali zochepa komanso kuti zakumwa zam’botolo samayenela kugawana. Mosakhalitsa mkuluyo anayamba kukalipira anyamatawo mpaka kumenya anyamatawo makofi owonetsa nyenyezi masana. Koma anyamatawo atazindikira kuti akuchepera anathawa pamalopo poopa kuti mwina mkuluyo atha kuwachotsa mano pa mphumi. Koma chomwe chinasangalatsa anthu pamalopo nchoti m’nyamata m’modziyo anagwetsa kabudula wake kamba koti anali omanga ndi mkuzi. Pakadali pano, mikoko yogona mderalo yadandaula ndi zomwe anachita mkuluyo pomenya anyamata chifukwa chomumana mowa.

 

Get Your Newsletter