11/09/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wina manja ali kunkhongo banja litatha
Mwamuna wina ku Lunzu mu mzinda wa Blantyre manja ali ku nkhongo banja lake litakathera kubwalo la nyakwawa.

11
September

Nkhaniyi ikuti anthu ambiri mderalo akhala akukaikira mwamunayo kuti wakhala akusowetsa mtendere anthu mderalo powabera zinthu zosiyana-siyana kuphatikizapo zokolora. Mkazi wa mwamunayo akamulangiza amakhalira kulalatila mkazi wakeyo ponena kuti ngati watopa ndi banja akhoza kuchoka pakhomopo. Izi zakhala zisakusangalatsa mkaziyo komanso abale a mwamunayo. Paja pali mau oti lafote limakwana , tsiku lina mwamunayo anagwidwa ndi anyamata ena a mderalo akuthamangitsa nkhuku ya mlimi wina dzuwa likuswa mtengo. Apa anyamatawo sanachedwe koma kugwira njondayo ndikumunjata ngati nkhumba uku akumukokera ku bwalo la nyakwawa ya mderalo. Chifukwa cha mfuu mkazi wa mwamunayo anathamangira ku maloko koma zachisoni anakapeza kuti mwamuna wake atanjatidwa ngati nkhumba. Apa mkaziyo anagwadwa pabwalo la nyakwawa ndikuchonderela kuti amumasule koma sizinamveke. Pa chifukwachi maiyo anakumbusa mwamunayo pa zomwe akhala akumuuza ndipo anauza bwalolo kuti banja latha. Koma m’malo modandaula kuti wagwidwa ndi nkhani yakuba mwamunayo anachonderela mkazi wake kuti amukhululukire uku akulira ngati kwagwa maliro . Anthu omwe anasonkhana ku bwalolo anaseka chikhakhali ndipo pamene timalandila nkhaniyi banja-lo latha koma sizikudziwika kuti nkhani yokhudza kuba yatha bwanji.

Mkulu wina aseketsa anthu

Tili m’boma lomwelo la Blantyre ku Nacholi mwamuna wina anaseketsa anthu atakadandaulira apolisi kuti amuthandize kupeza zinthu zake. Nkhaniyi ikuti mwamunayo mosazindikira wakhala pa ubwenzi wa ntseri ndi mkazi okwatiwa mpakana kumugulira foni yamakono komanso computer ya m’manja. Mwa zina mwamunayo sanasiire pomwepo koma kuthandiza ana amaiyo, mai ake komanso kukhala nawo pa zinthu zofunika zokhudza maiyo. Izi zimachitika chifukwa mwamuna wa maiyo amakhalira kutandala kumaganyo. Chifukwa choti chibwenzi chao chinafumbila tsiku lina mwamunayo anapita kunyumbako dzuwa likuswa mtengo koma mwatsoka mwini mkaziyo anali ali mnyumbamo. Anthuwo polonjerana mwini mkaziyo anadziulura kuti ndiye mwini nyumba kwa mlendoyo pamene naye mwamunayo ananenetsa kuti akudabwa chifukwa anali atagwirizana ndi maiyo pa nkhani yoti amange banja. Kumapeto kwa kukambilana kwao, mwamuna uja anapepesa ndipo m’malo mwake anapita ku polisi kuti amuthandize kuti apeze zinthu zake zomwe anamuonongera mkaziyo. Apa apolisi anauuza mosabisa Chichewa kuti nzosatheka chifukwa ubwenzi wao palibe omwe amaudziwa. Koma anthu ambiri mderalo adzudzula anthu omwe amakhala moyandikana ndi banjalo kuti amadziwa za nkhaniyi koma samafuna kuchitapo kanthu. Pakadali pano mwamunayo manja ali ku nkhongo chifukwa cha nkhaniyi ndipo akukhalira kulira ati chifukwa choti mkaziyo wamutaitsa nthawi. Nyakwawa ya mderalo ndi mikoko yogona aitanitsa banjalo ku bwalo kuti akambirane za nkhaniyi ndikuona momwe angawathandizile pamodzi ndi mwamunayo.

 

Mtumiki wina atandala myumba kamba ka manyazi

Mtumiki wina wa Ambuye mdera la Malemia m’boma la Nsanje akukhalira kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi. Nkhaniyi ikuti mderalo munali mwambo olonga ufumu ndipo mkazi wa gulupayo anapatsidwa udindo oyang’anila zakudya . Ku mwamboko anthu ambiri anasonkhana kuphatikizapo mamembala omwe amawatumikira Mtumiki wa Ambuyeyo . Nthawi ya chakudya itakwana zinabadwitsa akubanja kumva kuti chakudya chinaperewera makama-maka ndiwo chikhalireni pa mwambowo panaphedwa zifuyo zambiri. Apa anyamata ena omwe anaona mkazi wa m’busayo akulongedza nyama kuphatikizapo liver analunjika pa malo ena pomwe maiyo anabisa katunduyo. Zinali zochititsa manyazi atakapeza nyama ikukha magazi mjumbo. Izi zitachitika, Mbusayo komanso maiyo anachoka mosadziwika bwino pa malopo chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi. Pakadali pano banjalo likukhalira kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi. Malinga ndi yemwe watitumizila nkhaniyi zisikudziwika kuti nkhaniyi yatha bwanji pakati pa mtumiki wa Mulunguyo ndi maiyo koma mamembala a mpingowo akhumudwa ndi nkhaniyi.

 

Mai wina ayimitsa mikoko yogona

Mai wina mdera la Kalolo mboma la Lilongwe waimitsa mitu mikoko yogona ponena kuti akasumila mwamuna wina chifukwa chomugwiritsa fuwa la moto. Maiyo yemwe sanakwatiwepo anachiona chinthu cha mtengo wapatali mwamuna yemwe anali naye pa ubwenzi kwa nthawi yayitali atamutsimikizila nkhani yabanja. Koma chodabwitsa ubwenziwo watha zaka zingapo tsopano ndipo akamufunsa za nkhaniyi njondayo imangoyankha kuti chaka cha mawa. Chomwe chaseketsa anthu mderalo mchakuti pakadali pano maiyo wapempha nyakwawa ya mderalo kuti imulondolere kwa mabungwe omwe amathandiza amai pa nkhani za mtunduwu. Koma anthu ena otsatila bwino mau a Mulungu ati nzosadabwitsa kuti zomwe akufuna maiyo nkupherezera mau oti m’masiku otsiliza amai ambiri adzalakalaka kukhala pa banja mcholinga choti adzipatsidwa ulemu wa banja ngakhale asathandizidwe.

 

Mnyamata wina adabwa ndi zoyankhula za agogo ake

Mnyamata wina ku Edingeni m’boma la Mzimba sakumvetsa ndi zomwe alankhula agogo ake. Nkhaniyi ikuti mnyamatayo zaka zingapo zapitazo anapita ku Joni kokagwira ntchito mcholinga choti athe kupeza zosowa zake. Koma kwa zaka zingapo tsopano mnyamatayo wakhala akudwaladwala ndipo moyo wake sumayenda bwino ku Joni-ko. Tsiku lina ali mtulo mdziko la South Africa-lo anayamba kulankhula mokweza amvekere ndikubwera. Izi zinadabwitsa amzake omwe amagona nawo limodzi ndipo pomufunsa sanabise chichewa koma kuuza amzakewo kuti agogo ake akumuitana m’maloto. Nkhaniyi inachititsa mantha amzakewo ndipo anamulangiza kuti ayambe abwerela kuno kumudzi. Atafika kumudzi kwao mnyamatayo anali odabwa agogo akewo atamutsimikizila kuti asadandaule ndi kudwaladwala kwake koma chofunika angoonjezera za thandilo lake kwa gogoyo. Mnyamatayo anagwira pakamwa chifukwa mwa zina ngati panali munthu yemwe amamuthandiza kwambiri ndie gogoyo. Anthu ambiri mderalo ati sakukaika kuti gogoyo ndi okhulupilira zamatsenga. Pakadali pano anthu ambiri mderalo kuphatikizapo anthu opemphera atsimikizila myamatayo kuti angokhulupilira Mulungu m’malo mochita mantha ndi zochitika za mdziko. Malipoti ati mnyamatayo akukonzekeranso zobwerewla ku Joni ndipo gogoyo akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi.

 

Get Your Newsletter