12/09/17

Written by  Newsroom

Mai wina alodzedwa dzala

Mai wina yemwe amatsogolera ntchito za kumpingo wina akumuloza chala pa zomwe wachita kwa gulupu Likhomo mdera la  mfumu M’biza m’boma la Zomba.

12
September

Yemwe watumiza nkhaniyi wati maiyo ali ndi mwana wake wamkazi yemwe anapeza mwamuna woti nkumanga naye banja. Ndipo ataonekera kwa makolo a mtsikanayo mwamunayo anachoka mderalo nkupita kukafuna ntchito mu mzinda wa Lilongwe. Izi zinachitsa kuti mwamunayo ayambe kupereka thandizo kwa mkazi wakeyo. Ngakhale mwamunayo amatumizira mtsikanayo chithandizocho iye  anapalana ubwenzi wa mseli  mwamuna wina mpaka kutenga pakati. Mai amtsikanayo atazindikira kuti mwana wawo ali ndi pakati pa mwamuna wina  adampatsa zitsamba kuti achotse pakatipo. Koma zitsambazo sizinagwire ntchito bwino mpaka mtsikanayo kuyamba matenda akaya-kaya. Atampanikiza ndi mafunso ndipomwe mtsikanayo anaululu kuti mai ake ampatsa mankhwala ochotsera pakati pomwe ali napo. Pakadali pano mai-yo waleka kutumikira ku mpingowo ndipo m’busa wake wati akuganiza zomuchotsa mu mpingowo.

 

Mwamuna opephera amulipilitsa K7000

Tili m’boma la Zomba lomwelo koma mdera la sub traditional Authority Gwelero  mwamuna wina wopemphera amulipilitsa seven thousand kwacha. Malinga ndi mtolankhani wathu kumeneko wati mderalo  muli mkulu wina yemwe ngozidziwka bwino kumpingo wake. Mkuluyo yemwe ali ndi luso losiyana-siyana monga kuimba kumpingowo, ulamuliro wabwino komanso amaoneka wozilemekeza masiku apitawo wapezekeka masana  akuba phwetekele mdimba la m’busa wake. Patsikulo anthu mmudzimo anali otanganika ndi kutumikira alendo omwe anafika kudzayendera mpingo womwe mkuluyo amapempherako. Koma kasmba anali ndi maganizo okhota iye sanakhale nao kumwambo wa mapempherowo  ati poti amadwala. Koma atawendera kuti mapemphero ali mkati iye anapita kumunda kwa m’busa wake ndikuyamba kupulula phwetekere. Koma munthu mai wina anapezelera  njondayo mmundamo, atamufunsa iye adayankha kuti mwini mundawo ndiye wamutumutuma kuti akapulule phwetekereyo. Apo maiyo adapita kutchalichi komwe kunali mwambo wamapemphero ndikufunsa mwini mundayo za nkhanizo. Mwambo wamapemhero utatha anthu anakatengera mwamuna wakubayo ku bwalo la Nyakwawa ya deralo  komwe adaipeza njondayo kuti njolakwa. Ndipo popereka chigamulo kwea njondayo  nyakwawa ya deralo inati mkuluyo alipire K100.00 pa phwetekere aliyense yemwe antchola. Apo anthu anawerrenga phwetekele yense mpaka anakwan seven thousand kwacha.  Pakadali pano anthu mderlo akumuseka mkuluyo kuti wabesa kamba phwetekere wina ndi wamng’ono waosayenera  pa mtengo wa K100.00.

 

Azimayi oyendayenda akokelana kubwalo

Mai wina oyenda-yenda m’dera la Sangazi mu mzinda wa Mzuzu wakokera ku bwalo la milandu mai mzake oyenda-yendanso.  Nkhaniyi ikuti mwamuna wina wapa banja m’deralo wakhala akudzudzulidwa  chifukwa chosokoneza mabanja a weni kuphatikizapo amai awiriwo. Anthu akamulangiza mwamunayo wakhala akuyankha kuti sicholinga chake koma akazi ambiri mderalo kuphatikizapo apabanja akhala akumufunsila kuti akhale naye pa ubwenzi wa ntseri. Masiku apitawo amai oyenda-yendawo atazindikira kuti ali pa ubwenzi ndi mphongoyo anayamba kulalatilana pa njira mpakana ndeu ya fumbi inabuka pakati pao.    Anthu ambiri anakhamukira kudzaonerela ndeuyo koma winayo anakolopola madred a mzakeyo ndipo apa analira ngati kwachitika maliro. Anthu omwe anali pa malopo m’malo moleletsa anayamba kuchemerela mpakana uja anachotsedwa madrediyo analiyatsa liwiro ndikukamang’ala kwa mikoko yogona ya mderalo. Ku bwaloko anamutsimikizila kuti akokera ku bwalo mzakeyo pokhapokha nayenso ayankhe mlandu osokoneza banja la weni. Apa maiyo anachoka chokhumudwa koma akulalatila akuluakuluwo. Pamene izi zimachitika anthu omwe anasonkhana pa bwalolo anaseka chikhakhali kuphatikizapo mikoko yogonayo. Pakadali pano zamveka kuti maiyo wapiti kwa atumiki opemphera kuti amuthandize.

 

Athamanga bunobuno

Mwamuna wina m’dera la Mazengera m’boma la Lilongwe zinamukoka manja atathamanga mtunda wa 1-kilometer ali buno-buno kuthawa kuthidzimulidwa. Nkhaniyi ikuti mai wina mderalo yemwe ndi mtsogoleri wa amai pa mpingo wina wakhala akuyenda njomba mwamuna wake yemwe ndi nyakwawa ya mderalo. Kwa nthawi yayitali anthu ambiri akhala akumutsina khutu nyakwawayo paza ubwenzi wa ntseriwo koma nyakwawayo yakhala ikutsutsa za mphekeserayo ponena kuti mkazi wake ndi mtumiki wa Ambuye. Pa chifukwachi anthu ambiri kuphatikizapo nduna za nyakwawayo anagwirizana kuti asamalankhuleponso paza nkhaniyi. Paja pali mau oti lafote limakwana, Nyakwawayo ikuchokera ku ntchito zina inakhotera kumunda mcholinga choti akaone zakumunda. Koma ali m’mundamo anamva kunong’ona kwa anthu zomwe nyakwawayo sanakhulupilire. Atafika pafupi ndipa malopo anazindikira za mau a mkazi wake ndipo apa nyakwawayo sanafune kupupuluma ndipo inagwira pakamwa ataona mkazi wake ali buno-buno ndi njonda ina. Apa nyakwawayo mopwetekedwa mtima inatola chimwala mcholinga choti akhapile anthuwo, koma asanatero anthuwo anazindikira mwansanga ndipo kunali kuthamanga liwiro la mtondo wodooka. Njonda ya nchuunoyo  inadzambatuka buluku ili manja kusiya maiyo ali bunobuno. Choseketsa mwamunayo anathamanga pa mtunda wa 1-Kilometer uku ali maliseche. Pamene timalandila nkhaniyi banja la nyakwawayo laweyeseka ndipo njondayo ikukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi.

 

Akwanganulidwa ndi sing'anga wina

Mpondamatiki wina kwa Mwambo m’boma la Zomba manja ali ku nkhongo sing’anga wina atamukwangwanula ndalama za nkhani-nkhani. Nkhaniyi ikuti mpondamatikiyo yemwe ndi otchuka kwambiri mderalo pa nkhani zopemphera, mamembala a mpingo wake amumudalira chifukwa cha mau ake odalira Mulungu nthawi zonse koma osadziwa kuti mwamunayo amakhulupiliranso zinthu zina. Masiku apitawo telala wina mderalo anatsimikizila   mpondamatikiyo kuti pali  Sing’anga wina yemwe ndi katakwe pa ntchito  yochulukitsa ndalama ndipo pa chifukwachi mpondamatikiyo anavomerezadi ndikupereka ndalama zake za nkhani-nkhani mcholinga choti zikayenda telalayo adzapeze kangachepe. Koma mphuno salota izi sizinatheke koma m’malo mwake ndalama yonse ya mwamunayo inapita ndipo pomufunsa sing’angayo anatsimikizila anthuwo kuti asade nkhawa chifukwa zimatenga masiku. Nkhaniyi itakafika kwa mkazi wa mwamunayo, mkaziyo anayamba kuzazila mwamunayo pamodzi ndi telalayo ndipo pakadali pano banja la mwamunayo latha. Pamene timalandila nkhaniyi mpondamatikiyo akukhalira kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi ndi anthu ambiri omwe akhala akulangiza mwamunayo pa nkhaniyi kuphatikizapo mamembala a mpingo wake.

Get Your Newsletter