14/09/17

Written by  Newsroom

Banja lithela ku malo ogonela alendo

Mai wina ku Malimba pa boma la Salima manja ali ku nkhongo banja lake litathera ku malo ogona alendo.

14
September

Nkhaniyi ikuti maiyo wakhala akuyenda njomba mwamuna wake pochita ubwenzi wa ntseri ndi amuna ena ku malo ake a ntchito pa sitolo zina m’bonmalo. Kwa nthawi yayitali mwamuna wa maiyo wakhala akuuzidwa za mayendedwe a mkazi wakeyo ndipo mwamunayo wakhala akuvomereza za nkhaniyi koma wakhala akuuza anthuwo kuti amusiye adzagwira yekha. Masiku apitawa mzake wa mwamunayo anakatsina khutu mwamunayo kuti mkazi wake ali pa malo ena ogona alendo ndi njonda yomwe yakhala ikumveka kuti ili pa ubwenzi wa ntseri ndi mkazi wake . Apa mwamunayo sanachedwe koma kuthamangira ku maloko ndi anthu ena kuti akadzionere okha. Koma atangofika pa malopo mwamunayo anaona ngati kutulu ataona mkazi wake akuyenda mwachikondi ndi njondayo uku atagwirana manja. Mwa phuma mwamunayo anadzidzimutsa anthuwo ndi zikwapu ndipo analira ngati kwachitika maliro ndikumuuza mkaziyo kuti banja latha. Chifukwa cha makani naye njonda yakubayo inayamba kubweza moto koma ikanadziwa sikanatero chifukwa gulu lonse inamuunjikira ndikumumenya mpakana thaphya mpaka kukodzedwa ndipo anakatsitsimukira kwa nyakwawa. Ku bwalo la milandu njondayo inangoti kukamwa yasa kusowa choyankhula komanso zinadziwika kuti amalephera kuyankhula chifukwa cha ululu.

 

Athawa munthu wamisala
Mnyamata wina pa sitolo zapa Kachama mdera la Kasumbu m’boma la Dedza anaseketsa anthu atayamba kuthamanga ngati alibe mafupa kuthawa munthu wina wamisala. Nkhnaiyi ikuti mwamunayo yemwe ngotchuka ndi nkhani zamaganyu pa malopo amakhalira kulankhula mwa thamo kuti iye anabadwa masiku okwana komanso palibe yemwe angaime ndi iye pa nkhani yazibagera ndipo anthu anamupatsa dzina loti KAMATAMA. Nkhaniyi yakhala ikuipila anthu ambiri apa sitolopo koma amasowa poyambila chifukwa mwa zina mwamunayo amaopedwa chifukwa chozama ndi nkhani yazitsamba. Koma m’modzi mwa anthu omwe amachita maganyu pa malopo ndi mwamuna wina wamisala koma owoneka kuti ndi ofatsa. Mwamuna wolalatila amzakeyo nthawi zambiri samagona tulo ati ponena kuti wamisala uja akumulanda mgodi wake ndipo pa chifukwachi amakhaliranso kulalatila wamisalayo ncholinga choti zikamunyasa asiye ntchito yonyamula maganyu koma zinakanika. Masiku apitawa mwamuna wamatama uja anauza wamisala uja kuti adzamumeta tsitsi ndi chibagera zomwe sizinasangalatse wamisalayo. Apa ndeu ya fumbi inabuka pakati pao koma chifukwa chochepa mphamvu kwa mwamuna wamatamayo, wamisalayo anamukuntha mwamunayo mpakana kumukwakwazila ku dzala. Mwamunayo analira ngati mwana uku akupepesa wamisalayo. Kumapeto kwake mwamunayo anayankhula mau omwe anthu apa sitolopo sadzaiwala kuti wamisala adaona nkhondo uku akuthamanga liwiro la mtondo wodooka ngati amapalasa njinga. Pakadali pano mwamunayo akukhalira kutandala mnyumba ndipo wayamba wasowa pa malopo.

 

Anthu akhala mwa mantha ku Mulanje

Anthu akwa Naphungo m’dera la Juma m’boma la Mulanje akukhala mwa mantha ndi zomwe akuchita mkoko wina wogona m’deralo. Nkhaniyi ikuti mkoko wogonawo unapereka munda kwa mdzukulu wake kuti asamavutike pa nkhani yolima ndipo zinachitikadi. Chodabwitsa patadutsa maiyezi yochepa mkokowo unalangiza mdzukulu wakeyo kuti amubwezerenso mundawo mcholinga choti adzigwilirapo ntchito zina zomwe wauzidwa ndi mizimu. Chifukwa cha mantha ndi nkhaniyi mdzukuluyo anaperekadi mundawo koma akudandaulira anthu aja apa banjapo kuti amuthandize. Achibale ena atamva za izi anakokera ku bwalo la milndu mkokowo koma chodabwitsa nthawi zonse akati amufunse mkokowo za nkhaniyi amasanduka kadzidzidzi zomwe zakhala zikupereka mantha kwa nduna za mfumu komanso anthu ambiri a mderalo. Ngakhale izi zili chomwechi anthu ena ati sasiila pomwepa ndipo apondaponda kuti akhaulitse mwamunayo. Pakadali pano mwamunayo apindilana ndevu mkamwa ndi anthu a mderalo ndipo akukhalira kulozana zala. Pamene timalandila nkhaniyi anthu ena mogwirizana ndi mikoko ina yogona yaitanitsa sing’anga yemwe wafika kale mderalo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter