19/09/17

Written by  Newsroom

Banja lina lidabwisa anthu ku Nsanje

Anthu ena mdera la Malemia m’boma la Nsanje ati sakumvetsa ndi zomwe lachita banja lina mderalo.

19
September

Nkhaniyi ikuti banjalo liri ndi munda wa chimanga ku madimba ena mphepete mwa ntsinje wa shire omwe anthu amakwanitsa kulima kangapo pa chaka . Banjalo lomwe limaoneka kuti ndila manja lende limakhalira kulimitsa anthu mundawo koma kumapeto kwake lakhala likuyambana ndi anthu ambiri chifukwa chosawapatsa malipiro. Mosazindikira bwino za khalidwe la banjalo mnyamata wina anakalima m’mundamo mcholinga choti kumapeto kwake apeze ndalama. Atamaliza kulima mnyamatayo anagwira pakwamwa banjalo litagwirizana kuti maiyo akhalire limodzi ndi mnyamatayo ati ngati njira imodzi ya malipiro ake. Koyambilira mnyamatayo anakanitsitsa kwa ntuwagalu koma kutengera zomwe amachita maiyo ku dimbako mnyamatayo anatengeka komanso zinamukoka manja mpaka kuchita zachisembwere ndi maiyo. Choseketsa mchakuti mwamuna wa maiyo anthu ena atamufotokozera za nkhaniyi anazazila anthuwo ponena kuti chikuwakhudza mchiani ndipo mnyamatayo akapapila mowa wa nkarabongo amakhalira kuyamikira maiyo. Pakadali pano anthu ambiri mderalo kuphatikizapo abale a banjalo ati sakumvetsa ndi zomwe lachita banjalo. Nyakwawa ya mderalo pamodzi ndi mikoko yogona ati akokera ku bwalo banjalo.

Nyakwawa idzudzulidwa
Nyakwawa ina mdera la Kaduya m’boma la Phalombe ayidzudzula chifukwa cholekerela makhalidwe ena oipa. Nkhaniyi ikuti banja lina mderalo limakanitsitsa kupita m’maliro pa zifukwa zodwiwa okha. Masiku apitawa munthu wina wapa banjapo anamwalira ndipo nyakwawayo sinachedwe koma kulengeza za zovutazo kuphatikizapo kuuza adzukulu . Tsiku loika maliro litakwana adzukulu sananyalanyaze koma kupita kumanda kukagwira ntchito . Nthawi ya chakudya itakwana adzukuluwo anakanitsitsa kudya ndipo m’malo mwake anatumiza uthenga kunyumba ya siwayo kuti anafedwe akamalize okha ntchito yokumba manda. Nkhaniyi itafika kunyumba kuja anafedwa anaona ngati ali kutulo ndipo pa chifukwachi anakadandaulira nyakwawa ya mderalo. Izi zinapangitsa kuti mwambo wa maliro uchedwe komabe kumapeto kwa zonse zinayenda bwino koma nthawi inali itatha. Pa tsiku losesa nyakwawa inayamba kuloza chala adzukulu koma akanadziwa sakanatero chifukwa anthu onse anayiwowoza nyakwawayo ponena kuti imakonda kuikira kumbuyo anthu ena omwe salabadila zokhala ndi anzawo. Apa nyakwawayo zinamukoka manja chifukwa choti aliyense pa bwalolo anaikira kumbuyo adzukulu. Anthu ena atafufuza za nkhaniyi zadziwika kuti nyakwawayo imakonda kulandila zinthu kuchokera kwa anthu ena kuti adziwaikira kumbuyo. Pakadali pano nyakwawayo komanso anafedwawo akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi.

 

Ayenda zamadulira kamba ka manyazi 
Mlembi wa mpingo wina mdera la Mkanda m’boma la Mulanje akuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi. Kwa nthawi yayitali mamembala a mpingowo akhala akudzudzula gulupayo paza khaklidwe lake la nchuuno ndi amai okwatiwa apa mpingo omwewo. Mwamunayo zadziwika kuti mpingo wake oyamba omwe amatumikira unamuchotsa pa mpingo chifukwa cha nkhani ngati za mtunduwu koma zikuoneka kuti sakufuna kulapa. Chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga, masiku apitawa amai amu mpingowo anali ndi masankho ofuna kusankha mkulu wa gulu la amai koma chodabwitsa mlembiyo anauza gulu la amaiwo kuti munthu wapezeka kale ndipo anatsindika kuti mzimu oyera wamuonetsera kale m’masomphenya zomwe zinadabwitsa anthu onse apa mpingopo. Akuluakulu ena apa mpingopo atafufuza za nkhaniyi anapeza kuti mai yemwe amafuna gulupayo anali naye pa chibwenzi chikhalireni anthu awiriwo ngapa banja. Mkulu wapa mpingopo chifukwa chosakondwa ndi nkhaniyi anaitanitsa maiyo komanso gulupayo ndipo ku bwalo la mpingo zinali zomvetsa chisoni chifukwa mwa zina maiyo anaulura kuti gulupayo anachita kukonza mapulaniwo mcholinga choti alimbitse ubwenzi wao. Pakadali pano mlembiyo akuyenda ngati mbalame yogwera mvuwo chifukwa cha nkhaniyo ndipo mabanja a anthu awiriwo aweyeseka.

Mkulu wina asokoneza mwambo wa paper Sunday
Tili m’dera lomwelo la Mkanda m’boma la Mulanje mkulu wina wa mpingo anasokoneza mwambo ofuna kupeza ndalama mu mpingo omwe umadziwika kuti paper Sunday. Nkhaniyi ikuti nthambi ina ya mpingowo inali ndi mwambowo koma chifukwa choti wamkulu wa mpingowo mdera lonselo sagwirizana ndi mkulu wa nthambiyo anapita ku kachisiyo mwambo uli mkati ndikuyamba kulalatila mzakeyo kuti amamupinga komanso kuti akufuna kumulanda udindo chikhalireni ndi bodza la nkunkhuniza. Apa pofuna kupewa za mtopola mkulu wa nthambiyo anangochoka pa malopo ndikusiya mwambo uli mkati. Pofufuza za nkhaniyi zadziwika kuti m’modzi wa iwo amakhalira kudzudzula wina kuti m’malo mogwira ntchito ya Chauta amatanganidwa kugwira ntchito zakudziko. Mamembala ambiri mu mpingowo akukhalira kuloza chala mkulu wa mpingowo ndipo aophyeza kuti akapitilira ndi khalidwe lakelo onse atuluka mu mpingowo chifukwa ati zomwe zikuchitikazo zaonetsa poyera kuti ndi zizindikiro za m’masiku otsiliza.


Chule agwa mthumba la jekete

Mkulu wina kwa Mkalo mboma la Chiradzulu akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi chule atagwa mthumba la jekete yake. Nkhaniyi ikuti mkuluyo akukonzekela kumuveka unyakwawa ndipo mogwilizana ndi abale ake anakonza phwando pokonzekela tsiku lomuveka unyakwawalo. Tsono masiku apitawa anaitanitsa gulu la achinyamata ambiri omwe anali anzake kuti adzakhale limodzi kusangalala kuti tsopano akukhala mdindo. Koma madyelelo ali mkati anthu anadabwa kuti mzaoyo amangoti fulukutufulukutu osakhala momasuka. Mosakhalitsa anthu anadabwa kuona chule kapena kuti THESI akudumphadumpha kutuluka mu thumba la jekete lomwe mkuluyo anavala. Pa chifukwachi, anangoti zoli kusowa choyankhula koma anthu omwe akudziwa bwino za m’nyamatayo ati ndi katundu pa nkhani ya zitsamba kotelo kuti chuleyo ndi mbali imodzi ya zizimba zake ndikuti sangamusunthe chisawawa munthu wina aliyense. Panopa mwambowo ukumbekezeka kuchitika tsika lina lili lonse pomuvomereza kuti ndiye nyakwawa mdelalo ngakhale akuti akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi yomwe ili mkamwamkamwa mdelalo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter