12/10/17

Written by  Newsroom

Mikoko yogona iima mitu ku Machinga

Mikoko yogona yaima mitu kwa mfumu yaikulu Ngokwe m’boma la Machinga. Nkhaniyi kumeneko kunali mkulu wina yemwe wakhala akudwala kwa nthawi yaitali.

12
October

Achibale ake anayetsetsa kumtengera wodwalayo mzipatalata zosiyana-siyana kuti mwina mkupulumutsa moyo wake. Koma matenda anamanga ntchenje pa mkuluyo mpaka kutsikila kuli chete miyezi ingapo yapitayo. Eni mbumba anayendetsa mwambo wamaliro ndipo zonse zinayenda bwino. Ndipo patadutsa nthawi yokwanira, malinga ndi chipembezo chomwe malemuwo anakapemphera ali moyo, achibale a malemuwo anachititsa mwambo wachikumbutso. Anthu osiyana-siyana anafika kudzachita nao mwambo wachikumbutso. Pamwambowo anthu anakondwa kamba ka chakudya chokwanira chomwe analandira pa mwambowo. Koma mai wina yemwe anafika pamalopo anadabwitsa anthu atasowetsa mbale zomwe analandiliramo chakudya pa mwambowo. Mikoko yogona itamfutsa maiyo za mbalezo iye wayankha mmaso muli gwa! kuti ankagwilizana kwambiri ndi malemuwo ndipo watenga mbalezo kuti azikakumbukira za ubale wake ndi malemuwo. Anthu ena mderalo akuganiza kuti mwina maiyo akufuna zizimba. Pakadali pano, mikoko yogona yati ittengera nkhaniyi patali mpa aone chenicheni.

 

Anjatidwa kamba kogwilira mwana

Mkulu wina kwa Nkando mdera la TA Juma m’boma la Mulanje alimmanja mwapolisi pomuganizira kuti wagwilira mwana wa mkazi wa zaka khumi. Nkhaniyo ikuti mkuluyo amapanga business pa msika wa Nkando ndipo ndiwazaka zoposa makui asanu ndi limodzi. Ndipo malonda ake amamuyendera bwino kwambiri. Moti analemba anthu ena omuthandizira kugulitsa katundu wake pofuna kukweza bizinesi yake. Koma tsiku lina mmodzi mwa anthu ake sanafike kudzagwira ntchitoyo. Ndipo mwadzidzidzi kunafika kamtsikana ka zaka khumi komwe kamafuna ganyu. Apo bamboyo adapatsa mwanayo ganyu yotunga madzi. Koma mtsikana atagwila ntchitoyo bamboyo analephera kupereka malipiro kwa mwanayo mpaka panadutsa tsabata zitatu. Koma masiku apitawo mtsikanayo analawilira kwa mkuluyo kukafunsa ndalama yakeyo. Atafika kunyumbako, bamboyo adauza mwanayo kuti adikile . Apo wanayo anadikila mpaka mdima umagwa moti sanathenso kubwerela kwawo. Kutada anampatsa mwanayo malo ogona kamba kunali kutada. Ndipo mkati mwa usiku mkulu wopanda manyaziyo anagwilira mwanayo. Ngakhale mwanayo adayetsera kukuwa palibe yemwe anamumva kamba panali pakati pa usiku. Komanso bamboyo yemwe makzi wake anali atachoka pakhomopo adaopsyeza mwanayo kuti asaulule zankhanzazo. Koma mmawa kutacha mwanayo anathamangira kwao komwe anakauza achibale ake za zachipongwezo. Mosakhalitsa achibale anakatula nkhaniyo kwa apolisi omwe sanadeweze koma kugwira njondayo ndikuiponya mchitokotsi. Pakdali pano, mkuluyo akukuta mano mchitokotsi chapolisi ndipo ntchito zake zamalonda zaima.

 

 

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter