13/10/17

Written by  Newsroom

Anamizila kuledzera
Mwamuna wina mdera la Malemia m’boma la Nsanje anaseketsa anthu chifukwa chonamizila kuti waledzera.

13
October

Nkhaniyi ikuti mbuyomu mwamunayo wakhala ali pa banja koma pa zifukwa zina mkazi wake anachoka pa banjapo ndikukakhala kwao ati ponena kuti akapitidwe mphepo. Pa chifukwachi mwamunayo anapalana ubwenzi wa ntseri ndi mai wina mderalo mcholinga choti adziona omusesera mnyumba . Mphekesera inamupeza mwini mkaziyo zinamuipila kwambiri kufikira mwezi watha anakambirana ndi mwamuna wakeyo kuti abwererane koma mwamunayo samayankha zomveka. Poona kuti nthawi ikupita tsiku lina mkaziyo anapita kunyumbako usiku koma mwatsoka anapeza mwamunayo atapita kotentha njerwa. Apa maiyo sanachite chilendo koma kulunjika kuchipinda ndikukagoga podikirila mphongoyo. Posakhalitsa mkazi wachibwenziyo naye anafikira kulowa mnyumbamo uku ali buno buno akuitana chibwenzi chake kut ADALINGI muli kuti NDAFIKA. Mwini mwamunayo ngakhale anali mtulo anadzambatuka ndikugwira pakhosi mkazi wakubayo koma onse ali buno buno ndipo apa ndeu ya fumbi inabuka mpakana kugwetserana mu ndowa ya madzi zomwe zinachititsa kuti anthu ambiri adzuke ndikuthamangira kunyumbako. Mphepo itamupeza mwamunayo anafika pa khomopo ngati oledzera chonsecho kunali kuchita manyazi ndi nkhaniyi. Anthu ambiri mderalo adzudzula mwini mwamunayo chifukwa mwa zina anachoka yekha pakhomopo pamene ena adzudzula njondayo ndi mkazi wakubayo. Pakadali pano nyakwawa ya mderalo yanenetsa kuti ikukokera anthu onsewo ku bwalo kuti akayankhe mlandu onyazitsa mudzi.

 

Nyakwawa ina ibindikila kamba ka manyazi

Nyakwawa ina mdera la Chakhaza ku Dowa ikukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi. Nkhaniyi ikuti mderalo mpingo wina unapeza malo kudzera kwa nyakwawayo koma chifukwa chosagwirizana pa zinthu zina nyakwawayo inasintha manga ponena kuti malowo ndi asukulu. Apa mamembala a mpingowo sanaimve koma kukasuma kwa anthu ena owona nkhani za mtunduwu. Ku bwalolo nyakwawayo inangoti kukamwa yasa kusowa choyankhula. Apa bwalolo sinabise Chichewa koma kuyamba kuimitsa nyakwawayo pa udindo. Anthu ambiri mderalo kuphatikizapo mikoko yogona adzudzula kwambiri nyakwawayo chifukwa cha moyo wake osakhulupilika. Pamene timalandila nkhaniyi nyakwawayo ikukhalira kuyenda njira zodula pochita manyazi ndi nkhaniyi.

 

Anyamata ena adana kamba ka mkazi

Anyamata ena awiri omwe mbuyomu anali pa chimzache cha ponda apa nane mpondepo mdera la Mkanda ku Mulanje akuonana ndi diso la mkhwezure. Nkhaniyi ikuti m’modzi mwa anyamatawo anapeza chibwenzi pafupi ndi komwe amakhala mzakeyo mcholinga choti adzamange oyera. Koma mzake wa mnyamatayo yemwe amaoneka kuti sashota chifukwa cha bizinesi yake ya golosale anayamba kuchitila nsanje mzakeyo pomuuza kuti mkazi yemwe akumufunayo akhala naye pa ubwenzi kwa zaka zambiri ndipo ndi njinga yotheratu zomwe zili bodza la nkunkhu niza. Pofufuza za nkhaniyi zadziwika kuti mpondamatikiyo akuchita izi ati pofuna kuti afanane chifukwa mwa zina wakhala akukanidwa ndi akazi ambiri mderalo chifukwa cha mbiri zake zokhulupilira nyanga. Tsiku lina amunawo atakumana anapindilana ndeu mkamwa mpakna kumenyana ndipo mwamuna wa golosaleyo anagwetsedwa pansi ngati thumba la nandolo. Pokwiya ndi nkhaniyi mpondamatikiyo waophseza kuti athana ndi mzakeyo koma anthu mderalo abwezera mau mkuluyo kuti iye ndi yemwe aone chomwe chidameta nkhanga mpala kuphatikizapo kukagona ku polisi. Pakadali pano katakwe wazitsambayo sakupezekanso pa malo ake a bizinesi poopa kuti nthawi ina ili yonse amukwidzinga.


Mtsikana wina aulura zoipa zomwe amachita

Kodi akati munthu wabadwanso mwatsopano nkuthanthauza chani? Tili mchikhulupiliro kuti zimasocheza kuti kusiya za makhalidwe onse oipa omwe munthu wakhala akuchita. Koma izi sizili chomwechi ndi mtsikana wina yemwe wasowa mdera la gulupu Mkwate mboma la Mulanje ataulura zoipa zonse wakhala akuchita kwa zaka zambiri. Nkhaniyi ikuti mderalo muli mtumiki wa Mulungu yemwe akayamba kupemphera anthu ambiri amagwa pansi nkuyamba kuulura zonse akhala akuchita. Tsiku lina pa mwambo wa mapemphero mtsikanayo naye anayamba kuulura zoti wakhala ali pa ubwenzi wa ntseri ndi amuna ambiri apa banja mpakana kuwatchula maina zomwe zinakwiitsa eni amunawo omwe anali pa malopo pa nthawiyo. Pa chifukwachi eni amunawo anatsimikizila mtsikanayo kuti athana naye. Patadutsa masiku ochepa mtsikanayo sanaonekenso mderalo pothawa pochita mantha ndi zomwe anayankhula amaiwo. Anthu ambiri mderalo kuphatikizapo opemphera adzudzula amaiwo chifukwa chophseza mtsikanayo. Mwa zina anthu-wo alangiza amaiwo kuti thanthauzo la kulapa kuulura zoipa pamene ena ati mwina nkutheka kuti mtsikanayo amangodziyankhulira koma osati motsokhozedwa ndi mzimu wa Ambuye.

 

Mnyamata wina alodzedwa zala kamba ka zomwe wachita

Mnyamata wina ku Luwerezi ku Mzima akumulozerana pa zomwe zamuchitikira. Nkhaniyi ikuti anthu ambiri mderalo akhala akulangiza mnyamatayo kuti asiye khalidwe lake lokhalira kupapira mowa wa mkarabongo ndi kusuta fodya kosalekeza koma iye wakhala akuponyera ku nkhongo malangizowo. Mwa zina akayamba kuledzera mowa ogulitsa mowa-wo nthawi zambiri amachita kumukwakwazila kunyumba kwake koma akukodzedwa njira yonseyo chifukwa chophatikiza mowa ndi fodya. Pamene timalandila nkhaniyi mnyamatayo akukhalira kulankhula yekha mu njira komanso wasiya kuzisamalira ndikutupa Masaya . Anthu mderalo ati sakudabwa ponena kuti mwina mnymatayo mutu wake wasokonekera chifukwa cha fodya. Mwa zina mnyamatayo akukhalira kupemphapempha anthu ndalama ndi zinthu zina mcholinga choti ati akamwere mowa wa midoli ndikugula fodya. Mikoko yogona komanso anthu ena mderalo akulangiza achinyamata ena kuti mpofunika atengere phunzilo mzaoyo koma ena mwa achinyamatawo ati nzosamveka ati ponena kuti mzaoyo ndi ziwanda chabe ati ponena kuti iwo amamwa ndi kusuta mosamala .

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter