31/10/17

Written by  Newsroom

Ndeu ibuka pakati pa mwini mkazi ndi wa chibwenzi

Ndeu ya fumbi inabuka mdera la KACHECHE ku Mzimba pakati pa mwini mkazi ndi mwamuna wachibwenzi.

31
October

Nkhaniyi ikuti mkaziyo akhala akumudzudzula paza khalidwe lake lachimasomaso ndi amuna a weni koma mkaziyo wakhala akubweza moto pa nkhaniyi. Izi zakhala zisakusangalatsa mwamuna wake ndipo pa chifukwachi anayamba kulondola zochita za mkazi wakeyo. Chifukwa chokhala bwino ndi anthu mwini mkaziyo tsiku lina anthu ena mderalo anamutsina khutu pa komwe kunali mkazi wakeyo ndi njondayo. Apa mwamunayo mogwirizana ndi achibale analunjika kupita ku maloko ndipo sanamvetse atapezerela mkazi wake ndi njondayo atakolekerana khosi. Mkaziyo ataona mwamuna wake analiyatsa liwiri losayang’ana mbuyo ndikusiya ndeu ya fumbi pakati pa mbali ziwilizo. Koma chifukwa choti mwamuna wachibwenziyo ndi katakwe pa zibagera za khufuu monga zija tidziwila zaku China anaphaphalitsa anthu onsewo mpakana mwini mkaziyo kukodzedwa. Apa kunali mwana agwilitse ndipo anthu omwe amathandiza mwini mkaziyo anayamba kulalatila mwini mkaziyo kuti awavulazitsa. Mwini mkaziyo komanso anzakewo sakupezekanso mderalo pothawa njonda ya khufuuyo. Mikoko yogona komanso anthu ena ati akokera ku bwalo maiyo pamodzi ndi chibwenzi chake apo bi awasamutsa mderalo.

 

Athawa sing'anga wadzitsamba

Anthu ena amakomo angapo ku Mitundu ku Lilongwe asowa mnyumba zao pothawa Sing’anga wina wadzitsamba ochokera ku Mozambique. Nkhaniyi ikuti mderalo nyakwawa mogwirizana ndi mikoko yogona anaitanitsa Sing’anga kuti adzasilike deralo malinga ndi nkhani zaufiti zomwe ati zakula mderalo. Koma Sing’angayo atafika tsiku lotsatila chinthu china choneka ngati ndege yaufiti chomwe chinakutidwa ndi mphinjili, mikanda komanso nthenga za mbalame chinagwa . Tsiku lotsatila anthu anaona ngati kutulo anthu angapo ochokera m’mabanja ena anasowa mderalo zomwe zikupereka chithunzithunzi kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyi.

Mtumiki wina ayenda mwamanyazi
Mtumiki wina wa Ambuye kwa Gulupu Ngwerelo ku Zomba akuyenda zoli zoli chifukwa cha manyazi zitadziwika kuti ndi wa nzelu zayekha. Nkhaniyi ikuti mderalo mai wina opemphera wakhala akudwala ndipo matenda atafika pothiphwa anamwalira. Pa mwambo wamalilo ake anafedwa anakadziwitsa ampingo mcholinga choti akonze ndondomeko ya malirowo ndikulangiza mpingowo kuti mwambowo usatenge nthawi yaitali polingalila ndi momwe anadwalila. Koma mtumiki wa ambuyeyo sanasamale zolankhula anafedwawo ndipo m’malo mwake anawauza kuti aika zovutazo pakadutsa masiku awiri chifukwa ati amafuna kuti malemuwo atsogole mu ufumu wakumwamba mwa mtendere. Mphuno salota akanadziwa sakanatero chifukwa tsiku lomwe amafuna ampingowo zinthu zinafika povuta kwambiri zomwe zinadandaulitsa anthu omwe anafika pa siwapo. Mwambo wa maliro unasokonezeka mpakana anthu ena kufuna kuphaphalitsa Mtumiki wa Mulunguyu ndi makofi ndipo anachoka chothawa. Anthu ena opemphera anayendetsa mwambowo koma mofulumila kwambiri mpakana zonse zinatha bwino lomwe. Pamene timalandila nkhaniyi gulupayo akukhalira kuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi.

 

Anong'oneza bono kamba kokuba
Mwamuna wina Ku Lingazi ku Lilongwe akunong’oneza bondo mchitolokosi cha apolisi atamupeza olakwa pa mlandu wakuba. Khoti lina mu mzindawo lalamula mwamunayo kuti akagwire ukaidi wa miyezi isanu ndi inayi atalephera kufotokoza bwino paza mankhwala osiyana-siyana omwe anapezeka nawo pa chipatala china chamu mzindawo a ndalama pafupifupi 80 thousand kwacha. Mwa zina apolisi ati alonda apachipatapo ndiwo anagwira mwamunayo pamene anamuchita chipikisheni m’chikwama chake atamukayikira, ndipo atamufunsa analephera kufotokoza bwino komwe anatenga mankhwalawo. Ku bwalo la milandu mwamunayo anapempha khothilo kuti limuchepetsere chilangocho pomwe anati nkoyamba kupalamula mlandu komanso ali ndi banja lalikulu lomwe amalisamalira kuphatikizapo mayi ake omwe ndi achikulire koma sizinamveke. Koma bwalolo lati lapereka chilangocho chifukwa choti mchitidweu ukupitilirapitilirabe mdziko muno. Mwamunayo amachokera m’mudzi mwa Chitsotso m’dera la Kayembe mboma la Dowa.

 


Anthu a mdela lina mboma la Chiradzulu anakhamukila pakhomo la mkulu wina. Nkhaniyi ikuti munthu wina adasowa m’mudzimo zaka ziwili zapitazo koma zinamveka kuti tsopano mkuluyo watuluka mnyumba ina pamudzi wina kumeneko. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi mkulu wina anadana ndi mkazi wake ndi alongo ake ndipo anamuuza kuti ayaluka. Tsono lelo m’mawa anachokapo kupita koyenda mbuyo muno mkazi wake anasiya ku khomo kotsekula ndipo anthu maka ana omwe amasewela pafupi ndi nyumba ya mkulu wina kumeneko anadabwa chimunthu chooneka modabwitsa chikuwakodola. Ndipo anthu omwe anasonkhana pamalowo anadzidzimuka atadziwa kuti ndi mkulu yemwe adasowa m’mudzimo zaka ziwili zapitazo. Malinga ndi amene aona munthu-yo akuti tsitsi lake ndi lalikulu kwambili komanso ndenvu zikufikila mchiuno. Panopa sizikudziwika kuti zatha bwanji kumeneko.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter