11/11/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wina mdera la Kachere ku Dedza wasamuka mderalo chifukwa cha utambwali.

11
November

Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi otchuka mderalo pochititsa lendi minda yake ndipo kwa zaka zambiri zakhala zikumuyendera. Chaka chino mwamunayo anachititsa lendi munda wina kwa mphongo ina koma chifukwa choti mphongoyo imachedwa kulima anaganiza zosasa mundawo kwa munthu winanso ati mcholinga choti apezeretu zipangizo za ulimi. Posafuna kuchedwa mwamunayo anayamba kulima patangodutsa masiku awiri koma tsiku lina ali mkati kulima mwamuna oyamba uja anafika pa malopo ndikuzazila mzakeyo. Winayo sanafune kukangana ndi mzakeyo ndipo m’malo mwake anauza mzakeyo kuti abisale mundamo ndikuimbila foni mwini mundayo kuti adzatenge ndalama yotsala. Mwini mundayo analunjika kumundako koma ali mkati kukambilana yemwe anabisalayo anangoti balamanthu. Apa mwini mundayo anathamanga ngati alibe mafupa mpakana kulephera kumugwira. Pamene timalandila nkhaniyi mwini mundayo wasamukiratu mderalo koma mikoko yogona komanso nyakwawa ya mderalo amema anthu kuti apitilize kufunafuna tambwaliyo.

 


Mwamuna wina akumuloza chala kamba kobera gogo wina ndalama kwa Chitimbe mdera la Nkanda m’boma la Mulanje. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mkuluyo wakhala akuoneka ngati msamaliya wachifundo potumikira gogoyo. Mwa zina gogoyo wakhala akudalira mnyamatayo maka popeza zinthu zake zofunika monga kupita naye ku banki pokasiya komanso kuteapa ndalama ndipo mnyamatayo amakhala ngati mwana wapakhomopo. Koma paja amati mtima wanzako ndi tsidya lina, masiku apitawa mnyamatayo wadzidzimutsa anthu ataba khadi lotengela ndalama la maiyo. Itaba bakhadi njondayo inakatapa 500 thousand kwacha ku account ya gogoyo mpaka kugula mthuthu ndi ndalamazo. Ndipo gogoyo atadzindikila kuti khadi lake lasowa anapita ku bankiyo komwe anamuza kuti munthu wina wakhala akutapa ndalama ku account-yo. Apo ndi pomwe anadzindikila kuti mnyamatayo ndi kapsyala. Atampanikiza ndi mafunso mnyamatayo wavomela kuti anabadi ndalamazo.

 


Anyamata ena awiri mdera la Malili ku Lilongwe anenetsa kuti sadzayambilanso kuseka munthu wadazi atakagwera mchitsime chouya. Nkhaniyi ikuti anyamatawo cha m’ma six koloko madzulo anapangana kuti akayende mdera la Kalolo mcholinga choti ati akasangalale. Koma pa njira anakoma ndi mwamuna wa dazi ndipo anyamatawo anaseka chikhakhali koma mwamunayo anatsimikizila anyamatawo kuti aona chomwe chidameta nkhanga mpara. Atayenda pang’ono chabe anali odabwa kuti samaona komwe amapita chifukwa cha mdima osaona nawo nyenyezi. Apa anyamatawo zinawakoka manja komabe anadziumiliza kuyenda mpakana mtunda wama kilometer 15. Koma asanamalize mtundawo anagwera mchitsime mpakana m’modzi mwa anyamatawo kuvulala. Pa chifukwachi anakuwa kosalekeza zomwe zinachititsa anthu mderalo kuganiza kuti anyamatawo anali akuba. Ataachotsa, anyamatawo anayesetsa kufotokoza za nkhani yao koma anthu ena anawakaikira kuti anali mbava mpakana kuwakokera kwa nyakwawa ya mderalo. Chifukwa chotopa komanso njala anyamatawo anatsimikiza nyakwawayo kuti awasungire foni za manja ngati chikole kenako anawagawira chakudya. Apa nyakwawayo inatsimikizadi kuti anthuwo sanali akuba . Ku nyumba ya nyakwawa anyamatawo anenetsa kuti sadzayambilanso kuseka munthu wina aliyense kuphatikizapo wadazi ndipo pamene timalandila nkhaniyi abwerela kumudzi kwao.


Mai wina ku Chimbiya ku Dedza wanenetsa m’maso muli gwa kuti akwanitsa kuyendetsa chiwili. Nkhaniyi ikuti maiyo anamangitsa ukwati oyera zaka zingapo zapitazo koma pa zifukwa zodziwa yekha anapalana ubwenzi wa ntseri ndi njonda ina mpakana ubwenziwo kufika pofumbila. Chifukwa chosakondwa ndi nkhaniyi anthu ena anatsina khutu mwamuna wa maiyo ndipo apa mwamunayo anayamba kulondola zochita za mkazi wakeyo. Tsiku lina anapezerela mkazi wake ndi mwamuna mzakeyo anagonekerana khosi pa tchire, koma anachoka chothawa atazindikira za kupezeka kwa mwini mkaziyo pa malopo. Usiku atakomana maiyo sanapite patali koma kuyankhula m’maso muli gwa kuti mwamuna wake sakumukwanitsa choncho pa chifukwachi amulore kuyendetsa chiwiri. Mwamunayo anaona ngati zamalodza ndipo apa anatengera nkhaniyi ku bwalo la nyakwawa mogwirizana ndi ankhoswe a mbali zonse. Ku bwalolo anthu anaseka chikhakhali maiyo atabwerezanso za maganizo ake pa nkhaniyi. Nyakwawayo nayo komanso mikoko yogona anaima mitu mpakana nkhaniyi inathera panjira. Koma anthu mderalo adzudzula mwamuna yemwe ali pa chibwenzi ndi maiyo kuti mwina anadyetsa mankhwala oipa mkaziyo pamene ena ati nkutheka kuti mwini mkaziyo ali ndi mavutu ena omwe mkaziyo analephera kufotokozera bwalolo.


Mtumiki wina wa Ambuye kwa Gulupu Ngwerelo ku Zomba akumulozerana chifukwa chakumva za ekha. Nkhaniyi ikuti mderalo mai wina opemphera wakhala akudwala ndipo matenda atafika pothiphwa anamwalira. Pa mwambo wake anafedwa anakadziwitsa ampingo mcholinga choti akonze ndondomeko ya malirowo ndikulangiza mpingowo kuti mwambowo usatenge masiku ochuluka chifukwa thupi la malemuyo limatupa. Koma mtumiki wa ambuyeyo sanasamale zolankhula anafedwawo ndipo m’malo mwake anawauza kuti aika zovutazo pakadutsa masiku awiri chifukwa ati amafuna kuti malemuwo atsogole mu ufumu wakumwamba mwamtendere. Mphuno salota akanadziwa sakanatero chifukwa tsiku lomwe amafuna ampingowo zinthu zinafika povuta kwambiri zomwe zinadandaulitsa anthu omwe anafika pa siwapo. Mwambo wa maliro unasokonezeka mpakana anthu ena kufuna kuphaphalitsa Mtumiki wa Mulunguyu ndi makofi ndipo anachoka chothawa. Anthu ena opemphera anayendetsa mwambowo koma mofulumila kwambiri mpakana zonse zinatha bwino lomwe. Pamene timalandila nkhaniyi gulupayo akukhalira kuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter