14/11/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wina mdera la Chigalu ku Blantyre anaona ngati kutulo atagwidwa ali chino-chino kuseli kwa uvuni.

14
November

Nkhaniyi ikuti mwamunayo wakhala ali pa banja ndi mai wina yemwe anamupeza ndi ana angapo koma chifukwa chosakhutitsidwa mwamunayo anapalana ubwenzi wa ntseri ndi mai wina oyenda-yenda. Ubwenziwo utafika pofumbila anthu awiriwo akhala akukomana kuseli kwa uvuni omwe uli pafupi ndipa khomopo komanso mchimbudzi. Pamene amachita izi nkuti anthu ena akhala akudziwa za chinsinsicho ndipo potopa ndi nkhaniyi anatsina khutu mkazi wa mwamunayo. Apa mkaziyo anayamba kulondola zochita za mwamuna wake kufikira tsiku lina anapezerela anthuwo ali chinochino kuseri kwa uvuni. Apa mkaziyo sanaimve koma kuyamba kukuntha anthu awiriwo mothandiza ndi anyamata ena adzitho. Anthuwo anayesa kuchonderela koma sizinamveke mpakana anawanga pamodzi ndi zingwe ngati mtolo wa nkhuni. Chipwilikiti chinabuka pa malopo chifukwa mwa zina anthu awiriwo analira ngati makanda. Pamene timalandila nkhaniyi banja la mwamunayo laweyeseka ndipo pakadali pano akuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

 

Mtsikana wina oyendayenda mu mzinda wa Lilongwe amuna ayamba kumuthawa mkulu wina yemwe anatengana naye kupita kumalo ogona anthu apa ulendo atadandaula kuti walumidwa. Nkhaniyi ikuti mtsikanayo ali ndi mwana koma anthu akhala akumudzudzula chifukwa chowilikiza khalidwe lopita kumowa komanso kumalo ogona anthu apa ulendo ndi mwanayo ponena kuti adzavulaza mwanayo ndi tsempho. Koma masiku apitawa mayiyo anatengana ndi mphongo ina mwana wake ali kumsana, kufika mchipinda mkuluyo anakolopola zovala zonse ndipo akucheza mwanayo analuma mkuluyo kumsana mpakana bala. Pamenepa, mkuluyo analila kwambili malinga nkuti samadziwa chomwe chimachitika mpaka anakanena kwa akulu akulu apa malo ogona anthu apaulendopo. Panopa, zamveka kuti mkaziyo geni yake yalowa pansi chifukwa amuna ambili azindikila kuti mwana wake akumaluma makasitola. Anthu ena ati bola mwina mwanayo akadapeza omamusiila m’malo mopita naye kumalo ogona anthu apa ulendo. Naye mkulu yemwe adalumidwa ndi mwanayo sizikudziwika kuti kwao adakanama kuti chiyani za bala lomwe mwanayo anamusiila.

 

Mai wina akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi kwa Mpama mboma la Chiradzulu mwamuna wake atanenetsa kuti akututa katundu wake kubwelela kwao. Nkhaniyi ikuti mkulu wina adakwatila kwa Mpamako koma mbanjamo adapezamo mwana wa mwamuna. Mkuluyo amagwila ntchito ku Blantyre koma adakali ku ntchito mkazi wakeyo amalowetsa mwamuna mnyumbamo. Koma mwana wa mayiyo ataona kuti zaonjeza anawafunsa kuti mchifukwa chiyani akuchita khalidwe loipalo. Koma mayiyo anayankha m’maso muli gwaa kuti zisamukhudze, mpaka anagwilizana ndi azilongo ake kuthamangitsa mwanayo pakhomopo. Koma mnyamatayo anauza bambo ompeza aja zonse zomwe mai ake amachita ndipo mkuluyo wayamika mwanayo chifukwa cha chikondi chomwe waonetsa. Pakadali pano, mkuluyo akutita katundu wake kusonyeza kuti banja ndi mayiyo latha akaone zina. Zimenezi akuti zachititsa mayiyo aziyenda zamadulila podziwa kuti madzi achita katondo. Anthu ambili m’mudzimo adzudzula khalidwe la mchiuno la mayiyo yemwe akuti mwamuna wake amaonetsetsa kuti asamakhale wosowa.

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter