17/11/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wina kwa Gulupu Kalungwe mdera la Likoswe m’boma la Chiradzulu wanenetsa kuti wachimina atamugwiritsa ntchito yonse yapa mwambo osesa.

17
November

Nkhaniyi ikuti mderalo munachitika maliro ndipo tsiku lotsatila anafedwa kuphatikizapo nyakwawa ya mderalo anakonza zoti pakhomopo pachitike mwambo osesa. Mwambowo utangoyamba kumene mwamunayo yemwe ndi m’modzi wa abale aku banjalo anakautunga mowa ndikuyamba kulalatila anthuwo pamodzi ndi nyakwawayo uku ali dzandi-dzandi. Apa mwambowo unasokonezeka zomwe zinachititsa kuti nyakwawayo alipitse mkuluyo nkhuku zisanu ndi imodzi ngati chindapusa komanso kumulamula kuti agwire yekha ntchito yonse yosesa. Mwamunayo amachita izi uku akupitilirabe kulankhula zosamveka koma anthu omwe anasonkhana pa siwapo anati mkuluyo anali asanaledzere koma amachitila dala mcholinga chofuna kukhaulitsa nyakwawayo ati pa zifukwa zina. Mwambowo unachedwa kwambiri mpakana chaku masana. Pamene timalandila nkhaniyi anthu ena ati nkutheka kuti mwamunayo mutu wake sumayenda bwino . Tsiku lotsatila chidakwacho chinakapepesa nyakwawayo ndipo ananenetsa kuti wachimina.

 

Mai wina ku Chigumula m’boma la Blantyre wagwira njakata. Nkhaniyi ikuti maiyo wakhala ali pa ubwenzi wa ntseri ndi amuna awiri kwa zaka zinai koma anthuwo samadziwana. Kuphatikiza apo amunawo aberekera mkaziyo ana m’modzi aliyense. Paja pali mau oti tikatamba-tamba tidziyang’ana ku m’mawa , masiku apitawa amunawo anakomana kunyumbako ndipo aliyense mwa iwo amamudabwa mzake. Pomufunsa maiyo zinadziwika kuti mkaziyo wakhala akuwayenda njomba koma chifukwa chothamanga magazi kwa m’modzi mwa mphongozo ndeu ya fumbi inabuka mpakana kusambitsana ndi zibagera. Pa chifukwachi anthu ambiri anakhamukira ku nyumbako ndikuyamba kuleletsa ndeuyo koma sizinaphule kanthu chifukwa m’modzi mwa amunawo anamenyedwa mpakana kukodzedwa. Anthu omwe anafika pakhomopo anaseka chikhakhali chifukwa mwa zina anadzudzula amunawo kuti ndi ombwambwana. Mikoko yogona komanso anthu ena anagwirizana ndi amunawo kuti athetse ubwenzi ndi maiyo ndipo zinachitikadi. Pamene timalemba nkhaniyi mkaziyo manja ali ku nkhongo chifukwa akudandaula kwambiri ponena kuti ana ake asowa owathandiza. Mkaziyo pakadali pano amuthatsekulira mlandu onyazitsa mudzi.

 


Mwambo wa maliro unasokonezeka mdera la Juma m’boma la Mulanje. Nkhaniyi ikuti mderalo munthu wina wakhala akudwala ndipo matenda atakula anamwalira. Pa chifukwachi nyakwawa ya mderalo kuphatikizapo anafedwa anayamba kuyendetsa mwambo wa maliro. Tsiku loika maliro litakwana akuluakulu ena komanso anafedwa anapatsidwa mwai okaona nkhope kuphatikizapo mtumiki wina wa Mulungu yemwe anayandikira chitandacho uku akudandaula kwambiri chifukwa cha imfayo. Ali chigwadile chithumwa chinagwa kuchokera m’buluku lake mpakana kugwera chitanda. Anafedwa komanso anthu ena omwe anakuta chitandacho anadzuma pamene ena akulozerana mkuluyo kuti ndi nthakati. Apa mwamunayo yemwenso ndi otchula pa nkhani zolangiza anthu mau a Chauta zinamukoka manja ndipo anayesera kuti athawe koma anyamata ena adzitho anamugwira. Anthu ena amafuna kuti mkuluyo amulange pomumenya koma nyakwawa ya mderalo inalangiza anthuwo kuti asatero ndipo m’malo mwake amuitanitsa ku bwalo la milandu kuti akayankhe. Anafedwa achenjeza nyakwawayo kuti mpofunika kukhaulitsa mwamunayo chifukwa malinga ndi yemwe watitumizila nkhaniyi anafedwea ati sakukaika kuti munthuyo akudziwapo kanthu paza imfayo.Mayi wina pa mudzi wa Mdzeka kwa T/A Mazengera mboma la Lilongwe amuthidzimula koopsya chifukwa chodyetsa njomba mwamuna wake. Nkhaniyi ikuti mayiyo anapempha mwamuna wake kuti akalowe mgulu la Banki nkhonde komwe anthu amasungitsa ndi kubwereka ndalama. Nkhaniyi inakondweretsa mwamunayo malinga nkuti nayenso amachita bizinesi yogulitsa nsomba ndi mbeu zaku dimba. Sabata iliyonse mwamunayo amampatsa ndalama mkazi wakeyo zokapereka ku gululo ndipo masiku apitawa anagulitsa mtedza ncholinga choti akasungitse ku guluko ndalama zambili. Tsono chomwe chinavuta nchoti mayiyo amatenga ngongole ku guluko koma osamuuza mwamuna wakeyo ndipo akuti amangodya ngati tomato ndalamazo . Itakwana nthawi yogawana, anamuuza mwamunayo kuti ali ndi ngongole ya 8 thousand kwacha ndipo anamutsimikizira kuti akabweza ngongoleyo akalandira ndalama zake zonse. Koma zinali zokhumudwitsa akubwera ku guluko, mayiyo atafika pakhomo ndi 2 , 200 kwacha yokha. Atamufunsa analephera kufotokoza momwe amayendetsera ndalamazo. Apatu mwamunayo anakwiya kwambili ndipo nthawi yomweyo anamugwira nkuyamba kumuthidzimula mpaka anamutchola mkono. Mayiyo anatengera nkhaniyi ku bwalo koma akuti atamiyitanitsa mwamuna wakeyo sanapiteko. Pakadali pano banjalo lasokonekera ndipo mayiyo akungokhalira kulira usana ndi usiku polingalira zomwe zamuchitikirazo.


Tili m’dera lomwelo la Mfumu Mazengera koma m’mudzi mwa Geleta, Imfa ya mayi wina yaziziritsa anthu nkhongono. Nkhaniyi ikuti mayiyo anakwatiwa zaka zingapo zapitazo ndipo amakhala ku Area 25 ku Lilongweko ndi mwamuna wake. Banjalo akuti limakhala mosangalala ku chithandoko ndipo lmakhala bwino ndi anthu pa lainipo. Koma masiku apitawa,tambala wa mikolongwe anatera mayiyo pa mutu ndipo kenaka anayamba kuphupha nkugwa pansi. Nthawi yomweyo mayiyo anayamba kudwala ndipo anthu oyandikana naye nyumba anamutengera ku chipatala. Kumeneko anagonako masiku angapo koma osasintha ndipo achibale atamva zachiyambi cha matendawo, anatuluka m’chipatalamo nkupita kumudzi kwawo komwe amakafunitsa mankhwala a chikuda. Koma akuti izi sizinathandizebe mpaka mayiyo kutsikira kuli chete. Imfayi yakhumudwitsa anthu ambili moti ena akuganiza kuti nkhukuyo inali yamatsenga. Pakadali pano mwamuna wa malemuyo wanenetsa kuti sabwereranso ku maloko pochita mantha ndi zomwe wazionazo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter