You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma15/05/15

15/05/15

Written by  Newsroom

Ukwati utha kamba ka chimasomaso
Mayi wina kwa Kanduku mboma la Mwanza akunong’oneza bondo mwamuna wake atamuuza kuti ukwati watha chifukwa cha khalidwe lake la chimasomaso.  Nkhaniyi ikuti mwamuna wa mayiyo anapita ku Joni kukagwira ntchito.

19
May

  M’mbuyomu mayiyo anatasa nkuyamba kuchita zibwenzi ndi amuna osiyanasiyana.  Masiku apitawa anagwa m’chikondi ndi mphongo zina ziwiri koma sizimadziwana.  Ndiye poti la 40 likakwana, Tsiku lina amuna awiriwo anakumana ku nyumba ya mayiyo.  Mwamuna winayo ataona kuti patelera anayamba kuthawa ndipo apa mpamene anayamba kuthamangitsana kuzungulira mudzi onsewo koma chifukwa choti nzakeyo amanjonjola ngati nkhwali sanampeze.  Nkhaniyi inachititsa manyazi abale a mkaziyo ngakhalenso akuluakulu a m’mudzimo.  Nawo achibale a mwamuna wake-yo atamva,  anamufotokozera mbale wawoyo za nkhaniyi yemwe wangolandula kuti basi sakumufunanso mkaziyo.  Pakadali pano mayiyo akuyenda momangika kwambiri chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

 
Alalatira abusa mapemphero ali mkati
Mapemphero anasokonezeka mu mpingo wina ku Soche mu mzinda wa  Blantyre mai wina atalowa m’tchalitchimo nkuyamba kulalatira abusa.  Nkhaniyi ikuti mayiyo anali pa banja ndi mwana wa mbusayo koma banjalo linatha pa zifukwa zina atamuberekera ana awiri.  Kuyambira pa nthawiyo mayiyo  wakhala  akuchita businesi zosiyanasiyana  ndipo tsiku lina anapita ku Ntcheu kukatenga kachewere. Pamenepa mkazi wa m’busayo anapita kukatenga zidzukuluzo ndikupita nazo ku nyumba kwake komwe anakawagulira zovala.  Pa tsikulo mbusayo ndi mkazi wake ananyamula zidzukuluzo kupita nazo ku tchalitchi zitaponya zovala zatsopanozo.   Mwini anawo atafika pa khomo anapeza anawo  palibe ndipo atafunsa anamuuza   apongozi ake ndi amene anadzatenga anawo. Popsya mtima mayiyo anatsatila komweko koma atafika anamuuza kuti anawo apita ku tchalitchi ndi agogo awo. Apa mayiyo anatsatira komweko komwe anakapeza apongozi akewo akulalikira mau a mulungu koma mayiyo anangoti lowu  ndikunyamula  anawo uku akulalatila m’busayo  kuti alibe khalidwe ndipo anati ndi amene anatuma mwana wawo kuti athetse banja. Kenaka mayiyo akuti anavula anawo zovala zonse zomwe anawagulira agogo awo nkuwatenga ali mbulanda. Anthu ambiri anagwetsa nkhope zawo pansi pa zomwe anachita mayiyo. Pakadali pano nyakwawa ya m’mudzimo yaitanitsa maiyo ku bwalo koma iye akuti sapita kwa mfumuko  chifukwa sakuona chomwe analakwitsa pokatenga ana akewo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter