You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma17/05/15

17/05/15

Written by  Newsroom

Ayenda mwamanyazi mbiri yawo itawanda
Mnyamata wina kwa Iwala ku Ntaja m’boma la Machinga akuyenda zamadulira atazindikira kuti mbiri yake yawanda yofuna kulanda katundu wa m’nyumba  ya mchemwali wake.

19
May

  Nkhaniyi ikuti  mai wina anali pa banja lomwe amakhala mwa mtendere koma pa zifukwa zosadziwika  banjalo  linayamba kusokonekera. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati mwamuna wa mayiyo amapita ku nyanja kukapikula nsomba. Tsiku lina anagwa mchikondi ndi mkazi wina oyendayenda ndipo anapangana kuti akakomane ku malo ogona alendo ku Nayuchi. Mwatsoka anangoti gululu ndi mlamu wache yemwe anagona komweko poyembekeza ma Transport opita ku Liwonde kuti akapikulitse nsomba zake. Mkangano unabuka mpaka kuyamba kumenyana. Pamenepa mkazi wakubayo anapeza mpata  nkuthawa ndipo kenaka mlamu wakeyo anamupulumukanso nkuthawa. Tsiku lina mwamunayo anayimbira foni mkazi wakeyo  kuti atenge katundu yense ndipo banja latha. Apa mnyamatayo atamva kuti mlamu wakeyo sadzafikanso pamudzipo, analamula mchemwali wakeyo kuti amupatse matchini ndi njinga zomwe anasiya mwamuna wakeyo.  Zomwe akuchita mnyamatayo zakwiyitsa anthu ambiri mderalo ponena kuti  alibe gawo ku chuma cha mchemwali wakeyo chifukwa m’banjamo muli ana asanu ndi awiri omwe anasiya mwamunayo.

Mtsikana wina akunthidwa kamba koyenda ndi mamuna wa eni
Mtsikana wina wapa sukulu ina kwa Mposa m’boma la Machinga amuswa kodetsa nkhawa atamupezelela ali mchikondi ndi mwamuna wa mwini.  Nkhaniyi ikuti mkuluyo anatsegula malo ogulitsira mpunga ku malosa ndipo masiku apitawa anagwa mchikondi ndi mtsikana wapa sukulu ina yoyendera   mpaka chibwenzi chao chinafumbila. Kwa nthawi yaitali mkuluyo amati akamaliza kugulitsa mpungawo amapita kwa makolo ake a mtsikanayo ndipo makolowo amamulandila mwa chimwemwe. Koma mbiri inawanda mpaka mwini  mwamunayo anadziwa za nkhaniyi.  Patsikulo mayiyo anapeza awiriwo ali  jijili-jijili pa malo ena ogona anthu apaulendo. Posakhalitsa  ndeu ya fumbi inabuka mpaka mwini mwamunayo anang’ambira zovala mtsikana wakubayo ndikumuvulaza mlomo. Mtsikanayo anapeza mpata wothawa anthu ena achifundo ataleretsa ndeuyo. Pakadali pano mphunzitsi wamkulu wapa sukulu yomwe akuphunzira mtsikanayo wamuitanitsa kuti akafotokoze bwino za mkanganowo pamene atsikana anzake apa sukulupo akumulozaloza chifukwa choyaluka ndi mwamuna wa mwini.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter