You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma18/05/15

18/05/15

Written by  Newsroom

Akumba dzenje mnyumba kuti ayikemo mwana

Anthu a kwa  Mfumu yayikulu Nkhumba mboma la Phalombe atengera bambo wina ku bwalo pa zomwe anachitila mwana wake womupeza.

19
May

Nkhaniyi ikuti bamboyo wamakhala pa chikamwini mu’mudzimo kwa nthawi yayitali ndipo mkazi yemwe anamukwatirayo anamupeza ndi mwana. Tsiku lina mwana uja anadwala mwadzidzi ndipo mkuluyo m’malo mopititsa mwanayo ku chipatala anagwirizana ndi mayi ake kuti atsatile zomwe mpingo wao umanena pokumba dzenje mnyumbamo ndikumuika mwanayo uku akumupempherela mokweza kwa Namalenga kuti apeze bwino. Izi zinachitika masiku awiri otsatana, koma mayi wa mnyumbamo zinamuopysa apa anatsina khutu abale ache. Abalewo atamufunsa bamboyo cholinga chake iye anayankha m’maso muli gwa kuti akuchita zomwe zili m’malemba pofuna kuti munthu achiritsidwe ku matenda. Anthuwo anamutengera ku bwalo kwa Mfumu komwe anthu mudzimo anauza mfumuyo kuti mkuluyo amusamutse mudzimo komanso alipile chindapusa. Pakadali pano bamboyo amuthamangitsa m’mudzimo komanso amulipitsa chindapusa cha mbuzi zinayi, komabe anthu ena ndiwokwiya ponena kuti chilangocho chachepa kwambiri kamba koti anachita mkuluyo mkulaula mudzi komanso zachilendo.

 

Abindikila ku resthouse kamba ka chisembwere

Mayi wina kwa Nsakambewa mboma la Dowa waona zakuda pobindikira kwa tsiku la thunthu ku nyumba ina yolandila alendo pa sitolo zapa Nsakambewa mboma la Dowa chifukwa cha khalidwe lake lachimasomaso. Nkhaniyi ikuti mayi wina mderalo sakana amuna ndipo wakhala akuyenda ndi azibambo osiyanasiyana posalabadila za banja lake. Kwa nthawi yayitali mayiyo akhala akumudzudzula chifukwa cha khalidwe lake lothetsa mabanja a weni, koma iye zonsezo samazilabadila konse. Mayiyo masiku apitawa anapalana ubwenzi ndi njonda ina yomwe imagwira ntchito za mabungwe omwe siya boma mderalo, ndipo ubwenzi wao wakhala ukuyenda bwino. Anthu omwe amadziwa bwino za mayendedwe a mayiyo, anamuona mayiyo ndi bamboyo akulowa mchipinda cholandilira alendo ndipo anakafotokozera mwamuna wa mkaziyo. Eni malo atazindikira kuti mayiyo akumufuna anathawitsa bamboyo ndikubisa mayiyo. Anthuwo atafika pa malopo ananenetsa kuti sachoka pa malopo mpaka atamupeza mayiyo ndipo mayiyo zinamukoka manja mpaka anakhala ndi njala ku malo omwe amamusunga aja. Apa ataona kuti zinthu zavuta anangozipereka kwa anthuwo. Koma chodabwitsa mwamuna wa mayiyo anangonena kuti ndi mkazi wakebe, ndipo anthu mderalo ndi zomwe anachita bamboyo kuti mwina anamudyetsa mankhwala.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter