You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma30/10/17

30/10/17

Written by  Newsroom

Awapezelera ku malo ogona alendo

Mayi wina kwa Kamphata mboma a Lilongwe waona zakuda atamuyendetsa mbulanda pamene anamupeza ali ndi mwamuna wina ku malo ena ogona anthu apaulendo.

30
October

Nkhaniyi ikuti mayiyo ali pa banja koma mwamuna wake ali ndi ulumali wosaona. Izi zinachititsa kuti mayiyo apezerepo mwayi pa ulumali wa mwamuna wakeyo nkumazemberana ndi amuna ena. Ngakhale amachita khalidweli, koma anthu ena a m’deralo zimawakhudza kwambili ndipo anamuchalira kuti tsiku lina adzamuyalutse. Patsikulo mayiyo anagwirizana ndi chibwenzi chake kuti akakomane ku malo ena ogona anthu apaulendo. Akupita kumeneko anthu ena anamuona ndipo anakakodolana anthu angapo nkumamulondola mayiyo. Atafatsa kumaloko anthuwo anakauza mwamuna wake ndipo anamulonjeza kuti amuthandiza kumukhaulitsa mkaziyo bola angowauza chochita. Popsya mtima mwini mkaziyo analamuladi kuti akamuvumbulutse mkaziyo ku maloko ndipo akamugwira amuyendetse mbulanda. Izi zinachitikadi koma mwamuna yemwe anali ndi mayiyo anapeza mpata nkuthawa. Pakadali pano banjalo laweyeseka ndipo mayiyo akuyenda njira zachidule chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

 

Apha mwamuna pofuna kumudyesa kondaine
Mayi wina wagwidwa njakata mu mzinda wa Blantyre mwamuna wake atatsikira kuli chete pamene anakafuna mankhwala a kondaine kwa sing’anga wina. Nkhaniyi ikuti mayiyo anakwatiwa ndi mwamuna wina zaka zingapo zapitazi ndipo banjalo akuti limakhala bwino. Koma chifukwa chosakhutitsdwa mayiyo anapita kwa sing’anga kukafuna mankhwala ati ncholinga choti mwamuna wakeyo azimukonda kwambili. Mwa zina mayiyo akuti amafuna mwamuna wakeyo azimukhuthulira ndalama zonse za malipiro ake. Atapita kwa sing’angako, anamupatsadi mankhwalawo koma chizimba chake anamuuza kuti mwamuna wakeyo akakamuyitana koyamba ndi kachiwiri asakayankhe koma akayankhe akakamuyitana kachitatu. Mayiyo anakhala ngati wamva malangizowo, koma atapita kunyumbako anayiwala malangizo a ng’angayo. Mwamuna wakeyo atamuyitana, mayiyo anayankha nthawi yomweyo ndipo pamene amakafika kwa mwamuna wakeyo anamupeza atasanduka njoka ku miyendo koma ku ntunda akuoneka kuti ndi munthu. Apatu mayiyo anayamba kukuwa ndipo anthu atafika pamalopo anadabwa ndi zimenezi. Atamufunsa chomwe chinachitika analephera kufotokoza bwino koma anthu ena apafupi anati mayiyo akudziwapo kanthu. Zachisoni pasanapite nthawi mwamunayo anamwalira ndipo achibale atamva izi anenetsa kuti awona chomwe angachite kuti athane ndi mkaziyo. Pakadali pano mayiyo wagwira njakata moti sakudziwa kuti akuchimunawo athana nawo bwanji pa nkhaniyi.

 

Mayi wina akhumudwisa anthu ku Lilongwe

Zomwe wachita Mayi wina kwa Mfumu Mazengera mboma la Lilongwe zakhumudwitsa anthu. Nkhaniyi ikuti mayiyo ndi mbeta koma ali ndi ana awiri. Chaka chathachi pakhomo pake patalowa galu wakuda amapita m’makomo mwa abale ndi anansi ake kumakakongola chimanga nkumawalonjeza kuti akakolola chaka chino adzabweza chimangacho. Pomumvera chisoni, achibalewo amamupatsa chimangacho komabe amawerengera kuti inali ngongole. Tsono chaka chino mayiyo akuti pakhomo ake palowanso galu wakuda malinga nkuti sanakolole zokwanira. Atawona kuti chakudya chamuchepera, anayiwala za ngongoleyo ndipo akuti anthuwo samamukumbutsa poganiza kuti adziwa yekha. Tsono pano mayiyo zamukoka manja chifukwa choti anthu asanu omwe anawatengera chimanga chawo chaka chathachi anayamba kumukwenya nthawi imodzi ndipo mayiyo anasowa mtendere. Pachifukwachi akuti anatenga ana ake awiri nkulunjika nawo ku dziwe lina komwe anakadziponya m’madzi ati kuti afe pamodzi ndi ana akewo. Komatu mphuno salota, m’mene amadziponya padziwepo nkuti munthu wina akumuona ndipo anathamanga kukamuvuwulamo pamodzi ndi ana akewo. Atamufunsa chifukwa chomwe wachitira zimenezo anayamba kufotokoza. Pomva chisoni munthuyo anayenda naye khomo ndi khomo kwa anthu omwe anawakongola chmangawo nkukawapempha kuti angomukhululukira. Nkhaniyi yakhumudwitsa anthu ambili moti pakadali pano mayiyo akungobindikira m’nyumba chifukwa anthu akamuona akungomulozerana.

 


Anamizila kukomoka atadya ndalama za ukwati
Mwamuna wina ku Blantyre ananamizira kukomoka atadya ndalama za budget ya ukwati. Watitumizira nkhaniyi wati mwamunayo anapeza mkazi yemwe amakhala kunja. Ubwenziwo utafumbira, awiriwo anaganiza zochititsa ukwati woyera. Koma mwamunayo atauza bwenzi lakelo kuti alibe ndalama zochititsira ukwatiwo, ngengeyo inauza mwamunayo kuti asadere nkhawa kamba koti chilichonse , ipanga yokha ndipo inalonjeza budget ya 6.5-million kwacha ncholinga choti ukwatiwo udzakhale wapamwamba. Posakhalitsa, Donayo inayamba kutumizira mphongoyo ndalamayo. Koma mwamunayo amangomwera mowa ndalamazo nkumazipopa kuti yatola chikwama. Kutatsala masiku awiri kuti ukwati uchitike, Mkaziyo anafika kuno ku mudzi, ndipo mwamunayo anamufotokozera kuti chilichonse chili m’malo moti walipira zonse zofunikira kuphatikizapo hall. Kenako Donayo inadabwa ndi zochita za mwamunayo kamba koti amaoneka wosakhazikika. Ndipo usiku woti ukwati ndi mawa, atapanga zokonzekera zomaliza,, mwamunayo anaona kuti yalakwa ndipo ananamizira kukomoka. Achibale atamutengera kuchipatala, Dokotala anawauza kuti ali bwinobwino ndipo akunamazira zokomokazo. Atamutengera kunyumba, sananene chifukwa chomwe amachitira zimenezo ndipo ananenetsa kuti sapita ku ukwatiwo kamba koti sakakwanitsa kuimilira. Kenako akuchikaziwo anatulukira zoti mwamunayo sanalipire haloyo komanso panalibe akomiti. Poopa kuchita manyazi, akuchikaziwo anaganiza zokapeza hall ina yotchipa kuti bola ukwatiwo uchitike koma mwamunayo anakanitsitsabe. Malinga ndi yemwe watitumizira nkhaniyi, mkaziyo akungobindikira m’nyumba osadya komanso osalankhula ndi munthu, moti abale ake ati ali ndi nkhawa kamba koti sakudziwa chomwe mbale wawoyo akuganiza mu mtima mwake. Munthuyo watinso pakadali pano komwe kwalowera mwamunayo sikukuziwika.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter