You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma09/04/15

09/04/15

Written by  Newsroom

Nkhandwe likolowola maso amkulu wina
Mwamuna wapa mudzi wina kwa Mazengera m’boma la Lilongwe ali mu ululu woopsya nkhandwe itamukolowola maso usiku ataledzera.

13
April

Nkhaniyi ikuti tsiku lina mwamunayo anakapapila bibida pa mudzi woyandikana ndipo amabwelera ku nyumba kwake ndi mdima. Ndipo atafika pa nyumba pake mkuluyo anangofikira kudziponya pakhonde la nyumba yake kuti khuuu!!!! tolo tinali tomweto osadzukanso. Ali mtulo pa khomopo panafika nkhandwe zomwe zimafuna-funa nkhuku. Nkhandwezo zikununkhiza zinafika pomwe panali mkuluyo ndikumukolowola maso. Apo mkuluyo anakuwa mpaka mowa wonse kukungunuka kamba ka ululu. Anthu ambiri anathamangira ku malowo atamva mfuu ndipo anampeza mkuluyo ali kwalaa!!! magazi akuyendelera monga mtsinje. Anthuwo anathandizana ndikutengera mkuluyo ku chipatala komwe amugoneka. Pakadali pano mwamunayo akadali mchipatala ndipo sakupeza koma wanenetsa kuti sadzamwanso mowa mwa uchidakwa.Agwilira mtsikana ozerezeka
Mwamuna wina wapa banja kwa Kaluzi m’boma la Lilongwe wathawa pamudzipo mbiri itawanda kuti wakhala akugwilira mtsikana wina wozelezeka. Nkhani ikuti mwamunayo yemwe ali pa banja komanso ali ndi ana wakhala akugwilira mtsikana wozelezekayo yemwe amakhala ndi agogo ake pomunyengelera ndi ndalama. Tsiku lina anthu anapezelera mkuluyo akuchita za dama ndi mtsikana wozelezekayo pamene anali ku dimba la agogo ake lomwe lachita malire ndi munda wafodya wa mkuluyo. Pa tsikulo mkuluyo akuti anayengelera mtsikana wozelezekayo ndi 1-thousand Kwacha. Anthu atawapezelera m’dimbalo mkuluyo anathawa liwiro la ndege losayang’ana nalo m’buyo buluku liri ku manja. Pamene anthu amathandiza mtsikana wozelezekayo m’pamene anampeza ndi 1-thousand kwacha ya pepala m’manja. Anthu kuphatikizapo mikoko yogona yaima mitu ndi nkhaniyi ndipo nyakwawa ikudikilira tsiku lomwe mwamunayo adzatulukire pa mudzipo kuti akamuphe ndi mafunse pa nkhaniyi ku bwalo. Pakadali pano mkazi wa mwamunayo akupempha thandizo kwa anthu ena pa mudzipo chifukwa choti fodya wa wa njondayo akuonongeka m’munda. Anthu ena pa mudzipo ali kali-liki kufuna-funa mkuluyo, koma ena akuti adamuona mu msika waku Dowa .

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter