You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma10/04/15

10/04/15

Written by  Newsroom

Apasula banja kamba kachimasomaso
Mayi wapa mudzi wina m’dera la mfumu Symon m’boma la Neno wapasula banja ndi manja ake kamba ka khalidwe lake lachimaso-maso.

13
April

Mayiyo akuti wakhala akulira ndi umbeta kwa zaka zambiri ndipo akamberembere ena anamupatsa ana awiri koma osamukwatira. Zaka zapitazi mwamuna wina wa ntchito ya zomanga manga anakwatira mayiyo mpaka kubereka naye ana atatu. Koma paja akulu adati madzi saiwala m’khwawa, mayiyo anayambanso kuzemberana ndi mphongo ina yomwe imagwira ntchito ku Kampani ina yomwe imakonza njanji m’deralo mpaka mwamuna wake kumugwira yekha katatu konse. Pa tsikulo mwamunayo anauza mkaziyo alongedze katundu wake ndi kumulozera msana wanjira ya kwao kutanthauza kutha kwa banja. Mayiyo anakadandaula nkhaniyi kwa nyakwawa ya m’mudzimo koma nyakwawayo itamunika nkhaniyo inapeza maiyo wolakwa. Panopa maiyo wapita kwao koma iye pamodzi ndi mai ake akuponda ponda mwa asing’anga a mankhwala a zitsamba kuti mwamunayo asinthe maganizo ake n’cholinga choti abwelerane banja. Koma ankhoswe aku chimuna pamodzi ndi mwamunayo atemetsa nkhwangwa pa mwala kuti zivute zitani salola kuti maiyo abwelere ku banjako. Anthu ambiri m’deralo akuseka maiyo akamayenda kuti wapasula banja ndi manja ake.

 

Aika pa lilime ndalama zampingo
Mlembi wa mpingo wina kwa Mbela m’boma la Balaka akuyenda zoli zoli ngati wataya singano atamutulukira kuti amaika pa lilime ndalama za chitukuko chapa tchalichi-po. Nkhaniyi ikuti akhristu apa chalichi china mderalo akhala akupereka ndalama moolowa manja n’cholinga chogwilira ntchito zachitukuko pamalowo. Zikumveka kuti mlembi wapa mpingowo amathyolera m’nthumba ndalama zogwilira ntchito zachitukukozo pomagawa ndi mbusa wapa mpingopo. Koma Mbusayo atachoka pa tchalichi-po, panafika mbusa wina amene anachita kauni-uni paza ndalama zapa mpingowo. Pofuna kulondoloza zinthu, mbusayo anafunsa mulembiyo kuti atulutse dongosolo la ndalama za mpingowo. Koma mkuluyo ataona kuti pavuta anasiya kukapemphera ku tchalitchi ndipo m’malo mwake anayamba kumakapemphera ku nthambi ya mpingowo mtauni ya Balaka. Koma mbusayo atamva kuti mlembiyo akupemphera ku nthambi ya mpingowo anamulondola komweko ndipo anauza akhristu mu mpingowo kuti achoke mtchalichimo ndi kuti si membalanso wa mpingowo. Pakadalipano , mkuluyo akuyenda momangika kwambiri kamba koti wadziwa kuti mbiri yake yawanda kuti anthu ambiri adziwa zoti amuthothola ku mpingo chifukwa amathyolera mthumba ndalama zachopereka.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter