M’mbuyomu mayiyo anatasa nkuyamba kuchita zibwenzi ndi amuna osiyanasiyana. Masiku apitawa anagwa m’chikondi ndi mphongo zina ziwiri koma sizimadziwana. Ndiye poti la 40 likakwana, Tsiku lina amuna awiriwo anakumana ku nyumba ya mayiyo. Mwamuna winayo ataona kuti patelera anayamba kuthawa ndipo apa mpamene anayamba kuthamangitsana kuzungulira mudzi onsewo koma chifukwa choti nzakeyo amanjonjola ngati nkhwali sanampeze. Nkhaniyi inachititsa manyazi abale a mkaziyo ngakhalenso akuluakulu a m’mudzimo. Nawo achibale a mwamuna wake-yo atamva, anamufotokozera mbale wawoyo za nkhaniyi yemwe wangolandula kuti basi sakumufunanso mkaziyo. Pakadali pano mayiyo akuyenda momangika kwambiri chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.
Alalatira abusa mapemphero ali mkati
Mapemphero anasokonezeka mu mpingo wina ku Soche mu mzinda wa Blantyre mai wina atalowa m’tchalitchimo nkuyamba kulalatira abusa. Nkhaniyi ikuti mayiyo anali pa banja ndi mwana wa mbusayo koma banjalo linatha pa zifukwa zina atamuberekera ana awiri. Kuyambira pa nthawiyo mayiyo wakhala akuchita businesi zosiyanasiyana ndipo tsiku lina anapita ku Ntcheu kukatenga kachewere. Pamenepa mkazi wa m’busayo anapita kukatenga zidzukuluzo ndikupita nazo ku nyumba kwake komwe anakawagulira zovala. Pa tsikulo mbusayo ndi mkazi wake ananyamula zidzukuluzo kupita nazo ku tchalitchi zitaponya zovala zatsopanozo. Mwini anawo atafika pa khomo anapeza anawo palibe ndipo atafunsa anamuuza apongozi ake ndi amene anadzatenga anawo. Popsya mtima mayiyo anatsatila komweko koma atafika anamuuza kuti anawo apita ku tchalitchi ndi agogo awo. Apa mayiyo anatsatira komweko komwe anakapeza apongozi akewo akulalikira mau a mulungu koma mayiyo anangoti lowu ndikunyamula anawo uku akulalatila m’busayo kuti alibe khalidwe ndipo anati ndi amene anatuma mwana wawo kuti athetse banja. Kenaka mayiyo akuti anavula anawo zovala zonse zomwe anawagulira agogo awo nkuwatenga ali mbulanda. Anthu ambiri anagwetsa nkhope zawo pansi pa zomwe anachita mayiyo. Pakadali pano nyakwawa ya m’mudzimo yaitanitsa maiyo ku bwalo koma iye akuti sapita kwa mfumuko chifukwa sakuona chomwe analakwitsa pokatenga ana akewo.