You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma16/05/15

16/05/15

Written by  Newsroom

Mbava itupa mimba kamba kokuba mbuzi
Mbava ina kwa Mbera m’boma la Balaka ili pa ululu woopsya itatupa mimba chifukwa chakuba mbuzi ya mai wina mderalo.

19
May

Nkhaniyi  ikuti mai wina  anamangilira  mbuzi zake ku tchire komwe  zimadya.   Kenako mbavayo inazemba ndikuba mbuzi  imodzi ndikukayimangirira ku mtsinje. Usiku mkuluyu anakatenga mbuziyo ndikuika mdengu kuti akagulitse koma atanyamuka anakhumudwa kuona kuti mdengumo munali chinjoka chachikulu chili  fulukutu fulukutu, nthawi yomweyo  mbavayo inagwa pansi nkukomoka. Usiku omwewo anthu ena anatengera mkuluyo kuchipatala china komwe anakaulula kuti anaba mbuzi ya mai wina . Anthu ena anakapempha maiyo kuti apite ku chapatalako kuti akaone odwalayo kuti mwina apeza bwino koma maiyo  anakana ponenetsa kuti mbuzi zake zonse zikadali mkhola. Pakadali pano mbavayo siyinachre kwenikweni komabe yanenetsa kuti siyidzabanso.

 
Akuntha atate ake omupeza kamba ka nsanje
Mnyamata wina kwa Chiluzi m’boma la Dedza wathawa m’deralo  atamenya atate ake omupeza chifukwa cha Nsanje. Nkhaniyi ikuti bambo wina anakwatila mai wina ndipo m’banjamo anapeza mwana wa mwamuna. Mnyamatayo wakhala akukhala ndi atate akewo kwa zaka zisanu popanda chovuta . Koma masiku apitawa mnyamatayo anakapapila bibida ndipo anayamba kulalatila atate akewo kuti achoke pakhomopo pomwe anati asiye ukwati  mai akewo awasamala yekha. Bambowo akuti sanazitengere poganiza kuti mnyamatayo analedzera. Koma zinthu zinafika poyipa kwambiri pamene mnyamatayo anayimbila foni atate akewo  ndikuwawuza kuti asamuke pa khomo-po chifukwa akusokoneza chikondi chomwe mai akewo amamupatsa komanso business yake ya grocery yasokonezeka. Kenaka atafika ku nyumba anangofikira kukuntha  atate  akewo mpaka thapsya. Pamenepa mnyamatayo atazindikira kuti atate akewo akomoka anathawa osabweleranso. Pakadali pano anthu ambiri  mderalo akuganiza  kuti mwina  mai-yo anakhwimirana  ndi mwana wakeyo ncholinga choti bizinesi ya golosaleyo idziyenda bwino.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter