You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma09/10/17

09/10/17

Written by  Newsroom

Mai wina adabwisa anthu ndi khalidwe lake

Mai wapa mudzi wina kwa Chikowi m’boma la Zomba akudabwitsa anthu kamba ka khalidwe lake.

09
October

Maiyo wakhala pa banja kwa zaka zambiri koma chifukwa cha khalidwe lake losaugwira mtima banja lake latha dzuwa likuswa mtengo. Izi zachitika kamba koti mwamuna wa maiyo anamulandula mkaziyo pa banja chifukwa chotopa ndi khalidwe lake lachimaso-maso. Banjalo litatha amuna ambiri omwe anali pa ubwenzi wa nseri ndi maiyo naonso anayamba kumusala maiyo. Pakadalipano maiyo wawirikiza khalidwe lofunsira amuna a weni. Nkhaniyi yakhumudwitsa anthu ambiri mderalo kuphatikizapo amai apa banja poda nkhawa kuti akhoza kuwasokonezera mabanja. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti maiyo akusowa mtendere chifukwa mwa zina anthu akukhalira kumulozerana kamba ka nkhaniyi.

 

Athawidwa kamba kolalata

Mtengwa wina wapa mudzi wa Makunje kwa Nankumba m’boma la Mangochi akulilira ku utsi mwamuna wake atamuthawa kamba ka khalidwe lake lolalata. Nkhaniyi ikuti mkazi wina m’bomalo yemwe kwao ndi pa mudzi wina anapeza banja ndipo amakhala kwao kwa mwamunayo. Zaka zomwe mwamuna ndi mkaziyo akhala pa banja Chauta wadalitso banjalo ndi ana atatu. Koma chodabwitsa nchakuti masiku apitawa mwamunayo anatsazika makolo ake komanso achibale kuti akuchoka pakhomopo potopa ndi khalidwe lolalata la mkazi wake. Pakadalipano komwe mwamunayo walowera sikukudziwika. Nawo makolo komanso achibale a mwamunayo akungomuyang’ana mkaziyo osamuuza kuti azipita kwao poganizira kuti ali ndi ana omwe ndi wofunika chisamaliro. Koma anthu ena adzudzula mwamunayo kuti zomwe wachitazo ndi zosavomerezeka kamba koti achikhala kuti samammfuna mkaziyo akanamutumiza kwao. Pakadalipano mkaziyo maso ali kunjira poganizira kuti mwamunayo tsiku lina afika pakhomopo, kamba koti walephera kumuimbira foni yake ya m’manja kangapo konse koma sikugwira.

 

Mkulu wina ayenda zamadulira kamba ka manyazi

Mkulu wina yemwe amatsogolera pa ntchito zachitukuko m’dera lomwelo la Mfumu Mkanda, akuyenda zamadulira atamutulukira kuti akuvutitsa mayi wina osowa yemwe amalandira thandizo kuchokera ku bungwe lina mbomalo. Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko kuli mai wina yemwe amasunga ana amasiye. Ndipo masiku apitawo mderalo munafika bungwe lina lothandiza anthu osowa. Mwa zina bungwelo likupereka zakudya monga nyemba, ufa, mafuta ophikira komanso kumangira nyumba anthu omwe alibe pogwira kamba ka umphawi. Ndipo atsogoleri a deralo atawafunsa kuti asankhe anthu oyenera kupindula ndi ntchito za chifundozo, iwo anasankha maiyo kamba koti makolo ake anamwalira ndipo akusamalira ana amasiye. Atapereka dzina la maiyo kwa akulu akulu a bungwelo iwo sanachedwe koma kuyamba kuthandiza maiyo ndi zithu zosiyana-siyana kuphatikizapo kumpatsa maiyo zipangizo zomangira nyumba. Koma masiku apitawo maiyo anadabwa pomwe mkuluyo anayamba kumuvutitsa kuti amugawireko matumba awiri a cement yemwe bungwelo lamupatsa ati kamba koti mai-yo akupindula chifukwa cha iyeyo. Apo maiyo atadandaula kwa anthu ena, anamulangiza kuti akatule nkhaniyi kwa nyakwawa ya deralo komanso bungwe lomwe likupereka thandizolo. Pakadali pano njonda ya ziphuphuyo ikuganiza zosamuka mderalo zitamveka kuti mai-yo akufuna kupititsa nkhaniyi patali.

 

Mnyamata wina aimitsa mitu mikoko yogona 

Mnyamata wina m’dera la MFumu Msakambewa mboma la Dowa waimitsa mitu mikoko yogona chifukwa cha khalidwe lake lokonda kukwatira amayi achikulire. Nkhaniyi ikuti m’nyamatayo yemwe ali ndi zaka 32 ndi okonda kukwatirakwatira koma vuto lalikulu ndi loti amayi omwe amakwatirawo ndi achikulire osayerekeza ndi msinkhu wake. Poyamba mnyamatayo akuti anakwatira mayi wina wa zaka makumi asanu ndi ziwiri ndipo banjalo litatha anakwatira wina wa zaka 55 koma banjalo linathanso patangotha zaka zochepa. Anthu akamufunsa cholinga chake pokwatira amayi achikulire akumayankha kuti akufuna kuti anthu achikulire nawo azidya zonona zomwe amadya achinyamata komanso akuti chikuni chakale nchimene chimasunga moto. Masiku apitawa mnyamatayo akuti wakwatiranso mkazi wina wachitatu, ameneyo ndiye akuti zanyanya chifukwa choti ali ndi zaka zopitilira makumi asanu ndi limodzi. Pakadali pano anthu ambili m’mudzimo ati sakumvetsa cholinga chenicheni cha mnyamatayo pokwatira amayi achikulire pamene m’deralo muli amai ambili amsinkhu wake omwe akusowa mabanja. Anthu ambili m’deralo ati nkutheka kuti mnyamatayo ali ndi vuto ndiye akuopa kuyaluka akakwatira mtsikana.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter