You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma01/11/17

01/11/17

Written by  Newsroom

Mfumu ina igulisa mitengo ya kumanda

Anthu a kwa kalimanjira one kwa sub TA mkutumula, mboma la Ntcheu ati ndi okhumudwa ndi zomwe mfumu yawo ikuchita podula ndi kugulitsa mitengo ya kumanda mwa chisawawa.

01
November

Yemwe watumiza nkhaniyi yemwenso ndi mmodzi mwa adzukulu mmudzimo wati mmudzimo munachitika Maliro ndipo itafika nthawi yoti adzukulu akakumbe manda, anadabwa kuona munthu wina akudula mitengo m’mandamo, mitumbira ili pa mbalambanda chifukwa chakuonongeka kwa mitengoyo. Atamufunsa, munthuyo anawulura kuti mitengoyo anakagula kwa mfumu ya m’mudzimo kuti awotchele uvuni . Apa adzukuluwo analamula munthuyo kuti asiye kudula mtengowo ndipo anamuchenjeza kuti ngati achite makani awona zakuda. Adzukuluwo awopyseza kuti ngati mfumuyo sisintha mchitidwe owononga zachilengedwezo, asiya kukumba manda komanso sadzithandiza nawo pa ntchito yobyala mitengo.

 

Athawitsa nyama ya mbuzi

Mkulu wina m’mudzi mwa Mlele mfumu yaikulu chikowi mboma la zomba wadabwitsa anthu atathawitsa nyama ya mbuzi imene analandira pa mwambo wa chikondwelero cha eid-al adhuha. Chomwe chinachitika nchakuti m’mudzimo munabwera anthu ena amene amagawa nyama ya mbuzi malinga ndi chikondwererocho ndipo mkuluyo analandila mbuzi yomwe amayenera kuti agawane ndi amzake. Koma m’malo mogawana ndi anzakewo, mkuluyo anathawa nayo nyamayo ndikupita kunyumba kwake kuti akadye yekha. Apatu anthu ena sanalole ndipo anamutsatira komweko komwe anakamupeza akugagada nyamayo ku nyumba kwake. Apa mkuluyo anachita manyazi kwambili ndipo monyowa chifukwa cha manyazi anapereka nyamayo kwa anthuwo kuti agawane. Pakadali pano nkhaniyi yawanda mdera lonselo moti mkuluyo akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi.

 

Aphaphalitsidwa makofi kamba ka ngongole

Anyamata ena atatu ogwira ntchito pa kampani ina kwa Ngomani ku Lilongwe awaonetsa nyenyezi usana atawaphaphalitsa makofi chifukwa chozemba kupereka ngongole . Yemwe watitumizira nkhaniyi wati anyamatawo nthawi zambili amagula nsima ndi mbatata yootcha pa nthawi ya nkhomaliro ndipo anali makasitomala a mayi wina pamalopo. Ataona kuti chikasitomala chamera mizu, mayiyo anayamba kuwakongoza ndipo poyamba anyamatawo amakhulupilika kubweza ngonglezo. Koma kenaka atakongola nsima ndi mbatata yoootcha anayamba kuzemba zemba mpaka mayiyo kufika pothodwa. Ataona kuti sakumupatsabe ndalama zake, anapita kukamang’ala ku polisi ndipo apolisi anayitanitsa anyamatawo. Kumeneko anyamatawo anawaphaphalitsa makofi atayamba kukana mlanduwo. Kenaka akuti anavomera mlanduwo koma anati ndalama za mwezi wathau awononga kale. Pachifukwacho anyamatawo alonjeza kuti abweza ngongoleyo kumapeto kwa mwezi uno ndipo awachenjeza kuti ngati sabweza awoa chomwe chidameta nkhanga mpala. Pakadali pano mayiyo ndi anyamatawo akuonana ndi diso la nkhwezule chifukwa cha nkhaniyi.

Achoka chothawa ku dimba

Kwa T/A Chikho mboma la Ntchisi Mlimi wina anachoka chothawa ku dimba komwe amakathilira khofi. Nkhaniyi ikuti m’deralo muli mkulu wina yemwe ndi wolimbika pa ntchito zakumunda. Masiku apitawa anabyala khofi ku dimba ndipo anayilowa ntchito yothilira tsiku liri lonse m’mawa ndi madzulo. Pachifukwachi khofiyo amakula mochititsa kaso moti anthu ena anayamba kumuchitira Nsanje. Tsiku lina atapita kudimbako kukathilira, anatunga watercane yoyamba kukayika pamtunda ndipo anatsikira m’madzi kuti akatenge watercane ina. Koma atafika pa malo omwe anaika watercane yoyambayo, anachita mantha kupeza watercaneyo ikusuntha pang’nopang’no. Apatu mlimiyo anayamba kugogoma kuthamangira kumudzi kukauza anthu za malodzazo. Anthu ambili anasonkhana ku dimbako koma akuti sanaone zomwe amanena mlimiyo. Pakadali pano anthu ambili m’mudzimo ati akuganiza kuti alipo yemwe akumuyenda pansi mkuluyo kuti asiye kuthilira khofi wakeyo. Koma naye mlimiyo wanenetsa kuti apondaponda kuti akaone yemwe akumuchita zachipongwezo.

Mayi wina athidzimulidwa kamba kodyesa njomba mwamuna

Mayi wina pa mudzi wa Mdzeka kwa T/A Mazengera mboma la Lilongwe amuthidzimula koopsya chifukwa chodyetsa njomba mwamuna wake. Nkhaniyi ikuti mayiyo anapempha mwamuna wake kuti akalowe mgulu la Banki nkhonde komwe anthu amasungitsa ndi kubwereka ndalama. Nkhaniyi inakondweretsa mwamunayo malinga nkuti nayenso amachita bizinesi yogulitsa nsomba ndi mbeu zaku dimba. Sabata iliyonse mwamunayo amampatsa ndalama mkazi wakeyo zokapereka ku gululo ndipo masiku apitawa anagulitsa mtedza ncholinga choti akasungitse ku guluko ndalama zambili. Tsono chomwe chinavuta nchoti mayiyo amatenga ngongole ku guluko koma osamuuza mwamuna wakeyo ndipo akuti amangodya ngati tomato ndalamazo . Itakwana nthawi yogawana, anamuuza mwamunayo kuti ali ndi ngongole ya 8 thousand kwacha ndipo anamutsimikizira kuti akabweza ngongoleyo akalandira ndalama zake zonse. Koma zinali zokhumudwitsa akubwera ku guluko, mayiyo atafika pakhomo ndi 2 , 200 kwacha yokha. Atamufunsa analephera kufotokoza momwe amayendetsera ndalamazo. Apatu mwamunayo anakwiya kwambili ndipo nthawi yomweyo anamugwira nkuyamba kumuthidzimula mpaka anamutchola mkono. Mayiyo anatengera nkhaniyi ku bwalo koma akuti atamiyitanitsa mwamuna wakeyo sanapiteko. Pakadali pano banjalo lasokonekera ndipo mayiyo akungokhalira kulira usana ndi usiku polingalira zomwe zamuchitikirazo.


Tili m’dera lomwelo la Mfumu Mazengera koma m’mudzi mwa Geleta, Imfa ya mayi wina yaziziritsa anthu nkhongono. Nkhaniyi ikuti mayiyo anakwatiwa zaka zingapo zapitazo ndipo amakhala ku Area 25 ku Lilongweko ndi mwamuna wake. Banjalo akuti limakhala mosangalala ku chithandoko ndipo lmakhala bwino ndi anthu pa lainipo. Koma masiku apitawa,tambala wa mikolongwe anatera mayiyo pa mutu ndipo kenaka anayamba kuphupha nkugwa pansi. Nthawi yomweyo mayiyo anayamba kudwala ndipo anthu oyandikana naye nyumba anamutengera ku chipatala. Kumeneko anagonako masiku angapo koma osasintha ndipo achibale atamva zachiyambi cha matendawo, anatuluka m’chipatalamo nkupita kumudzi kwawo komwe amakafunitsa mankhwala a chikuda. Koma akuti izi sizinathandizebe mpaka mayiyo kutsikira kuli chete. Imfayi yakhumudwitsa anthu ambili moti ena akuganiza kuti nkhukuyo inali yamatsenga. Pakadali pano mwamuna wa malemuyo wanenetsa kuti sabwereranso ku maloko pochita mantha ndi zomwe wazionazo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter