You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma08/11/17

08/11/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wina mdera la Kachere ku Dedza wasamuka mderalo chifukwa cha utambwali.

08
November

Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi otchuka mderalo pochititsa lendi minda yake ndipo kwa zaka zambiri zakhala zikumuyendera. Chaka chino mwamunayo anachititsa lendi munda wina kwa mphongo ina koma chifukwa choti mphongoyo imachedwa kulima anaganiza zotsasa mundawo kwa munthu winanso ati mcholinga choti apezeretu zipangizo za ulimi. Posafuna kuchedwa mwamunayo anayamba kulima patangodutsa masiku awiri, koma tsiku lina ali mkati kulima mwamuna oyamba uja anafika pa malopo ndikukalipila mzakeyo. Winayo sanafune kukangana ndi mzakeyo ndipo m’malo mwake anauza mzakeyo kuti abisale mundamo ndikuimbila foni mwini mundayo kuti adzatenge ndalama yotsala. Mwini mundayo analunjika kumundako koma ali mkati kukambilana yemwe anabisalayo anangoti balamanthu. Apa mwini mundayo anathamanga ngati alibe mafupa mpakana kugwera ku phompho. Pamene timalandila nkhaniyi mwini mundayo wasamukiratu mderalo koma mikoko yogona komanso nyakwawa ya mderalo amema anthu kuti apitilize kufunafuna tambwaliyo.

 

Mwamuna wina akumulozelana kamba kobera gogo wina ndalama kwa Chitimbe mdera la Nkanda m’boma la Mulanje. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mkuluyo wakhala akuoneka ngati msamaliya wachifundo potumikira gogoyo. Mwa zina gogoyo wakhala akudalira mnyamatayo maka popeza zinthu zake zofunika monga kupita naye ku banki pokasiya komanso kutapa ndalama ndipo mnyamatayo amakhala ngati mwana wapakhomopo. Koma paja amati mtima wanzako ndi tsidya lina, masiku apitawa mnyamatayo wadzidzimutsa anthu ataba khadi lotengela ndalama la gogoyo. Ataba khadiyo njondayo inakatapa 500 thousand kwacha ku account ya gogoyo mpaka kugula mthuthuthu ndi ndalamazo. Ndipo gogoyo atazindikila kuti khadi lake lasowa anapita ku bankiyo komwe anamuza kuti munthu wina wakhala akutapa ndalama ku account-yo. Apo ndi pomwe anadzindikila kuti mnyamatayo ndi kapsyala. Atampanikiza ndi mafunso mnyamatayo wavomela kuti anabadi ndalamazo.Anthu a m’mudzi wina ku Mitundu mboma la Lilongwe agwidwa ndi mantha aakulu malinga ndi zomwe zachitika ku banja lina pomwe mwana wao wa mnyamata wafa nsomba itamulowa m’mimba. Nkhaniyi ikuti mnyamatayo anapita kukawedza nsomba ku damu lina m’deralo ndi anzake. Ali chiyimire mphepete mwa damulo, nsomba ina inatuluka nkumudumphira mnyamatayo kumulowa mkamwa mpaka kutsikira m’mimba. Anzake omwe anali nawo pamalopo anamutenga nzawoyo kuthamangira naye ku chipatala komwe anakamuchita opareshoni. Chodabwitsa nchoti atamuchita opareshoniyo, nsombayo inatuluka ya moyo ndipo achibale anayitenga nkukayiwotcha. Koma akuti m’mene nsombayo imapsya pamotopo nkuti mnyamatayo naye akuthatha ndi imfa moti tikunena pano watsikira kuli chete. Zimenezi zadabwitsa anthu m’deralo moti ambili akuganiza kuti zimenezi nzamuwanthu. Pakadali pano akubanja la malemuyo akuganiza zopondaponda mwa asing’anga kuti akawone chenicheni chomwe chapha mbale wawoyo.


Mtumiki wina wa Ambuye kwa Gulupu Ngwerelo ku Zomba akumulozerana chifukwa chakumva za ekha. Nkhaniyi ikuti mderalo mai wina opemphera wakhala akudwala ndipo matenda atafika pothiphwa anamwalira. Pa mwambo wake anafedwa anakadziwitsa ampingo mcholinga choti akonze ndondomeko ya malirowo ndikulangiza mpingowo kuti mwambowo usatenge masiku ochuluka chifukwa thupi la malemuyo limatupa. Koma mtumiki wa ambuyeyo sanasamale zolankhula anafedwawo ndipo m’malo mwake anawauza kuti aika zovutazo pakadutsa masiku awiri chifukwa ati amafuna kuti malemuwo atsogole mu ufumu wakumwamba mwamtendere. Mphuno salota akanadziwa sakanatero chifukwa tsiku lomwe amafuna ampingowo zinthu zinafika povuta kwambiri zomwe zinadandaulitsa anthu omwe anafika pa siwapo. Mwambo wa maliro unasokonezeka mpakana anthu ena kufuna kuphaphalitsa Mtumiki wa Mulunguyu ndi makofi ndipo anachoka chothawa. Anthu ena opemphera anayendetsa mwambowo koma mofulumila kwambiri mpakana zonse zinatha bwino lomwe. Pamene timalandila nkhaniyi gulupayo akukhalira kuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi.

 


Chipwilikiti chinabuka pa sitolo zapa Naminjiwa mdera la Kaduya ku Phalombe chidakwa china chitathetsa mkangano. Pa malopo pali mwamuna wina yemwe ngotchuka pokonza njinga za moto ndipo tsiku lina munthu wina wakabanza ya njinga ya moto anapititsa njinga yakeyo kwa katakweyo kuti amukonzere. Koma m’malo mokonza njingayo mwamunayo anayamba kugwira zinthgu zina zosagwirizana ndi zomwe anamuuza. Mwa zina makanikoyo anayamba kugulura engine mpakana kutenga piston ndikubisa. Pamene amachita izi nkuti anthu ena akumuona ndipo anakafotokozera mwini njingayo. Atafika pa malopo anthuwo anayamba kulongozana mpakana ndeu ya fumbi inababuka. Mkanganowo uli mkati chidakwa china chinafika pa malopo ndikukalipila anthuwo uku akuwadzudzula kuti sanaonetse moyo wachimuna mpakana kuwakumbutsa kuti mkangano sungawathandize. Apa anthuwo anachita manyazi mpakana mkanganowo unachepa zomwe zinachititsa kuti anthu omwe anali pa malopo ayambe kuseka anthuwo mpakana kuwakuwiza. Pamene izi zimachitika ntchito za malonda zinasokonekera pa malopo. Ngakhale zinthu zinali chomwecho anthuwo amvetsetsana pa nkhaniyi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter