You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma29/11/17

29/11/17

Written by  Newsroom

Agogo awili okalamba kwambili akunthana kwambili kwa Mchinguza mboma la Machinga mpaka kutsala pang’ono kusokoneza mwambo wachinamwali cha jando.

29
November

Watitumizila nkhaniyi wati mdelalo anthu ambili akutulutsa zinali za jando. Zimenezi zinachitika mafumu akulu akulu atalamula kuti ana onse omwe ali ku samba atuluke pamene sukulu yayandikila. Mafumuwo anati kuchedwetsa ana ku ndagala kumasokoneza maphunzilo. Pa chifukwa angaliba ambili anatulutsa anamwali ao omwe amawasunga kuchinamwali. Tsono monga mwa dongosolo amai anaphika thobwa komanso chakudya chosiyanasiyana chomwe anakonzela anthu kumeneko. Koma amai ataika thobwa kuti anthu amwe ndu yafumbi inabuka pakati pa agogo awili oyendela ndondo. Agogo awiliwo amalozana zala kuti wina akumwa kwambili thobwalo ati chifukwa choti alibe mano. Pamenepa, winayo anauza nzake kuti nayenso akumwa kwambili chifukwa ali ndi abathwa omwe amawamwetsa. Pamenepa, agogo awiliwa anayamba kuphikana mpaka kuunjikana pansi. Anthu ena ati nkutheka kuti agogo awiliwo samalimbilana thobwa-lo koma kuti mwina za uthakati.

 

 

Mai wina kwa Chumachitsala mdela la mfumu Kachere mboma la Dedza waimitsa mitu ya mikoko yogona atalankhula m’maso muli gwaa kuti akufuna mitala. Watitumizila nkhaniyi wati mai wina wakhala akuzembera mwamuna wake kumachita chibwenzi. Kenaka mwamuna wachibwenzi uja anagwilizana ndi mai uja kuti azikakhala pa msika wina mdelalo. Koma mai ake amwamuna wa chibwenziyo anakasokolotsa mayiyo ponena kuti akusokoneza banja la mwana wao yemwe analinso pa banja. Pa chifukwa-chi anabwelela kwa mwamuna wake wakale uja koma nakonso anamusasa kotelo kuti manja ali kunkhongo chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi. Maiyo akuyesela kupepesa kuti amangonena za mitala koma zonse sizikuphulabe kanthu. Mboma lomwelo la Dedza kwa Kachere ukwati wina omwe umayembekezeka kuchitika sabata ino wasokonezeka mwamuna atathawa m’mudzimo. Watitumizila nkhani-yi wati mwamuna wina anakonza zoti amange ukwati koma zonse zokonzekela zitatha. Kunamveka kuti mwamunayo analinso ndi chibwenzi ndi mkazi wina ndipo achibale anabwela naye kudzamutula malinga nkuti anapezeka ndi pathupi. Pa chifukwa-chi podziwa kuti madzi achita katondo mwamunayo wathawa m’mudzimo ndipo komwe walowela sikukudziwika. Pakadali pano, anthu akudandaula malinga nkuti zinthu zambili anali atagula kale.


Kondakitala wina amukuntha kodetsa nkhawa mpaka kumuchotsa mano atatu pamphumi ku area 23 mu mzinda wa Lilongwe. Nkhaniyi ikuti pali kondakitala wina wa minibasi ina yomwe imayenda pakati pa Area 25 ndi 23 koma vuto ndi lakuti amakonda kuyambana ndi anzake chifukwa chosaugwila mtima akapapila bibida. Tsono dzulo laliwisili anachitanso chimodzimodzi mpaka kumangolimbana ndi aliyense pa chifukwa-chi, anyamata ena anamupanilila kumuphika mpaka kumuchotsa mano atatu pa mphumi ndipo panopa zamveka kuti wanenetsa kuti asiya kupapila bibida mwauchidakwa akapeza ndalama. Ku Lilongwe komweko kwa Masula mkamwini wina amusamutsa pa mudzi atadyetsa anthu kalongonda yemwe akuganiza kuti anachita kukaba m’munda mwa mkulu wina. Nkhaniyi ikuti mkamwini wina yemwe kwao mkwa Chisauka anakaba kalongonda m’munda wina momwe eni ake adatsilika ndipo kufika pakhomo anamukonza bwino lomwe. Koma chodabwitsa mchakuti aliyense yemwe anadya nao kalongondayo amangotsekula m’mimba mpaka ena kukawagoneka mchipatala. Pa chifukwa-chi eni mbumba amvana zosamutsilatu mkuluyo pakhomopo ati ponena kuti tsiku lina adzathetsa mtundu wao.

 

 

Mwambo oveka nyakwawa ina kwa Kalumbu mboma la Lilongwe lomwelo unasokonezeka gule wa gologolo atalephela kutsika mu mtengo omwe anakwela. Watitumizila nkhaniyi wati mwambo woveka unyakwawa kunafika gule wamkulu osiyanasiyanasiyana ndipo mwambo onse unayamba bwino bwino. Koma malinga ndi amene watumiza nkhaniyi panali kusiyana maganizo pakati pa akulu akulu awili adambwe malinga nkuti aliyense amafuna kuti gule wake ndiye ayambe kusangalatsa anthu pa mwambowo. Kenaka gule wamkulu wa gologolo anakwela mu mtengo wautali ndipo atamaliza kusangalatsa anthu amati azitsika koma kuti zimakanika. Amai oimbila nyimbo nao kuti golo golo tsika mpaka ena mau kuchita kusasa ndipo anayamba kunyinyilika kuti saombanso m’manja chifukwa atopa. Anthuwo akuti amaona ngati akuchitila dala gologoloyo kusatsikako. Koma kenaka anadziwa kuti chilipo chavuta mpaka zamveka kuti anachita kutewetsa mtengowo mpaka anamutsitsa. Pakadali panopa atsabwalo akuonana ndi diso lofiila chifukwa cha nkhaniyi podziwa kuti alipo wina yemwe anamuchesula guleyo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter