Awapezelera nchimbudzi ali mchikondi
Banja lina kwa Chinyama mboma la Kasungu linatsala pangono kutha mwamuna atapezelela mkazi wake mchimbudzi ali mchikondi ndi chibwenzi.
Abeledwa K160,000 kwa mkazi waku Mozambique
Mwamuna wina ku Tsangano mboma la Ntcheu akulila usiku ndi usana mkazi waku Mozambique yemwe anakwatila atamukwangwanula pafupifupi K160,000 mkuthawila kwao.
Akunthidwa ataba mbewu ya tsabola
Anyamata awiri a mdera la Kalumba m’boma la Lilongwe achilapa atamenyedwa kolapitsa chifukwa cha kuba mbeu ya tsabola wa paplika kwa mlimi wina wa mderalo.
Njoka ituluka mu ntondo wa chigayo
Anthu ena ogwira ntchito yagaitsa pa ntchini ku Mtunthama m’boma la Kasungu aona malodza njoka itatuluka mu mtondo wa chigayocho, iwo ali mkati ndi ntchito yao yothandiza anthu.