Error
  • JUser: :_load: Unable to load user with ID: 43
You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma23/05/17

23/05/17

Written by 

Panja lina lisekedwa
Banja lina akuliseka pa sitolo za kwa Nkanda m’boma la Mchinji. Nkhaniyi ikuti masiku apita mkulu wina yemwe ndi wochita malonda pamalopo anapezerela mkazi wake akutchaya lamya kwa mwamumuna wachibwenzi.

23
May

Apo mwamunayo mtima sanaupeze ndipo adafuna kulanda mkazio wakeyo lamyayo. Koma mkaziyo sanalole ndipo motero ndeu yafumbi inabuka pakati pao. Ndeuyo inachema mpaka kung’ambirana zovala ndikusala za mkati mokha. Panthawiyo palibe yemwe analeletsa anthu awiriwo ati kamba mkaziyo wakhala akuchita thamo kwa a mzake kuti banja lake silingathe kamba iye adapita patali pofuna kuti mwamuna wakeuyo adzimukonda. Pakadali pano mwamunayo wati nkhaniy saitsiira pafupi.

 

Wakabaza ayenda usiku okhaokha kamba ka kamanyazi

Tili kwa Mkanda komweko wakabanza wina akuyenda usiku wokha kamba ka manyazi. Yemwe watumiza nkhaniyi wati masiku apita mkuluyo adanyamula mai wina pa njinga yake kuti akamusiye komwEa maiyo amapita. Koma ali pakati pa ulendowo mkaziyo adauza mwamunayo kuti alibe ndalama zolipira hayalayo. Mai-yo adamuuzanso wakabanzayo kuti aone chochita popeza wakula watha. Mosakhalitsa awiliwo anagwirizana zongothana patchire lina lomwe lili m’mbali mwa mseu womwe awiriwo amadutsamo panth. Ndipo pomwe awiriwo amalowa patchirepo mkuti ana ena akuwaona. Awiriwo atalowa ptchirepo anavula zovala zao nkuyamba kugawana chikondi ngati banja. Mosakhalitsa ana aja anatulukira pamalopo ndi kuyamba kupilikitsa anthuwo mpaka wakabanzayo kuiwala njinga yake pamalopo. Anthu amidzi yoyandikira pamalowo anadabwa kuona mkuluyo akukokera tharauza wake kwinaku akuthanga. Ndipo ana atalephera kugwira anthuwo adakaulula kwa mikoko yogona ya mderalo. Mikoko yogona itakokera awiriwo kubwalo wakabanzayo waululu kuti mkaziyo analephera kulupira ndalama za hayala ndipo anangoganiza zoti athane ndi mkaziyo. Pakadali pano wakabanzayo akuyenda usiku wokha-wokha kamba ka manyazi koma anthu ena ali ndi nkhawa kuti mwina awiriwo sanaziteteze panthawiyo zomwe zingaike miyoyo yawo pachiopsyezo kamba ka mlili wa HIV womwe uli kunjaku.

 

Chidakwa china chikunthidwa

Chidakwa china achitsambitsa kumowa komwe chimakonda kupapila bibida ku Chinangwa mtauni ya Mbayani mu mzinda wa Blantyre. Mderalo muli mwamuna wina yemwe kwake nkudzikhuthulira mowa pomwe nkazi wake amataktaka kuti apezere banjalo zosowa. Ndipo nthawi zambiri mkaziyo akapezako kandalama mwamunayo amanka nakatengeko zina ndikumwera mowa. Poyamba mkaziyo anakadandaula zankhaniyi kwa ankhoswe komanso akumpingo kwa mkuluyo kuti achepese mkhalidwe lake lakumwa mowa mwa uchidakhwa zomwe ati zimamubweretsera mavuto m’banja lake. Koma izi, sizinaphule kanthu. Ndipo mkaziyo atatopa ndi mkhalidwe la mwamuna wakeyo anakatula nkhaniyi kwa anzake a mwamuna wake omwe amamwa nao mowa limodzi. Apo anthuwo anachita upo kuti amlange pomsambisa mkuluyo akafika kumowako. Ndipo mwachizolowezi njondayo inafika pamalopo. Apo anzakewo anailandira mwamsangala poipatsa matoti a mowa wachilendo ndipo itamwa anzakewo anaitengera kubafa komwe anaikasambita komanso ndikuipatsa mwambo kuti izitsamala banja lake. Pakadali pano njondayo yati yasiya kumwa mowa mwaichidakwa ndipo iyamba kusamalira banja lake.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter