Error
  • JUser: :_load: Unable to load user with ID: 43
You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma25/05/17

25/05/17

Written by 

Agwilira gogo

Mikoko yogona m’boma la Kasungu yati yakhumudwa ndi zomwe wachita mnyamata wina wa zaka 17 pogwirira gogo wina mderalo.

24
May

Nkhaniyi ikuti gogoyo ndi wa zaka 72 ndipo amazisamalira kwambiri. Koma mphuno salota pa tsikulo gogoyo anapita ku mtsinje wa Kamvunguti komwe amachapa zovala ndipo mwadzidzidzi mnyamatayo anangoti gululu, ndipo mosachedwetsa mnyamatayo anachera ndale gogoyo mkugwa pansi kenaka mnyamatayo anavula gogoyo chitenje ndipo pofuna kulanditsa chitenje chake , mnyamatayo anamugwirilira gogoyo. Gogoyo atakaneka ku polisi , apa pamene anagwira mnyamatayo ndipo zotsatila za chipatala zaonetsa kuti gogoyo amugwiliradi. Pakadali pano mnyamatayo akukuta mano mchitolokosi cha polisi m’bomalo poyembekeza kuti akawonekere ku khothi kuti akayankhe mlandu ogwilirila.

 

Mayi wina adabwisa anthu ku ndirande

Mai wina ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre yemwe akuoneka kuti anavulala nkono ndipo anamumanga chikhakha wadabwitsa anthu ponena kuti akufuna kutsikira panjira minibus yomwe anakwera chifukwa choti kondakitala wa busiyo anakana kulandila ndalama yake ya ulendo wo. Chomwe chinachitika ndi nchoti mai-yo anakwera bus ku ndirande kupita ku chilobwe kusera ku Chipatala . Kenaka mai-yo anatulutsa ndala yoti alipile pa ulendowu koma Dalaivala ndi kondakitala anagwirizana kuti asalandile ndalamayo kuchokera kwa mai-yo . Koma atayenda ka ulendo pang’ono mai-yo ananena kuti akufuna kutsika pa basi-yo ndipo anasikadi. Anthu omwe anakwera basi-yo anakhumudwa kwambiri atamva kuti mai yemwe anatsikayo ndi katakwe wa Chitaka pa ndalama za eni. Ichi akuti nchifukwa chake kondakitala wa basiyo anakana kulandila ndalama ya mai-yo. Ndipo atakana kulandira ndalamayo mai-yo anadziwa kuti Game yagona ndipo chomwe akanachita nkungotsika basi-yo kamba ka manyazi. Pakadali pano ma dalaivala onse ku Ndirande apangana kuti amukhutha koopsya mtakatiyo ngati angapitilize ndi khalidwe lokawa ndalama-lo.

 

Wamisala aba chimanga

Alimi ena kwa Chimwala akukhala mwa mantha chifukwa cha munthu wa misala wina yemwe akumaba chimanga mderalo. Nkhaniyi ikuti wamisalayo akumayendayenda m’minda mwa alimiwo atatenga poto machesi ndi nkhuni pa mutu. Kenaka akafika pa munda omwe wamusangalatsa wa misalayo akumamanga chisakasa chake ndikuyamba kumphika chimanga m’mundamo madzulo mpaka kutcha akutafuna chimangacho. Ndipo eni mundawo akapita akumakhumudwa kupeza kuti wamisalayo wadya chimanga chambiri. Anthu ambiri akamufunsa wamisalayo akumaopsyeza kuti avulaza eni mindawo ndipo akulalata kuti mindayo ndi ya malemu makolo ake. Pakadali pano nyakwawa ya m’mudzimo yalamula alimiwo kuti amugwira kuti apite naye ku chipatala cha ku zomba kuti mwina eni chimangacho apume ku mchitidwe oyipa wa wamisalayo.

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter