You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma15/11/17

15/11/17

Written by  Newsroom


Anthu ena atatu akuwaloza chala powaganizira kuti akuphunzitsa ana zinthu zachilendo kwa Nankumba ku Monkay Bay, m’boma la Mangochi.

15
November

Mtolankhani wa nkhani zammaboma kumeneko wati masiku ambuyomu ana ena akhala akudandaula kuti amakhala wotopa kwambiri mamawa akadzuka kamba kuti agogo ena atatu mderalo amawatenga kotamba. Apo mikoko yogona mderalo inakokera agogo atatuwo omwe ndi amai awiri kuzanso bambo mmodzi mkanyumba komata ku ayankhepo pankhaniyo. Agogowo akana nkhaniyi. Koma ngakhale agogowo akana za nkhaniyo, anawo anenetsa kuti agogo akhala akuwatengera kumalo osiyana-siyana. Mwa zina anawo ati agogowo, akhala akupita ndi anawo ku maiko maiko ena monga Tanzania, Zimbabwe komanso ku America. Mwachitsanzo mmodzi wa anayo masiku apitawo anagwa pa ndege ya ufiti yomwe anakwera paulendo wopita kotamba. Ndipo anawo atinso nthawi zina amasewera pansi pa mtengo mpira wa mutu wa munthu yemwe amusankha kuti amuzunze mderalo. Pakadali pano anthu mderalo ati apilitiza kufufuza bwino za nkhaniyi.

 

 

Anthu aima mitu ndi zomwe zachita njonda zachilendo kwa gulupu Kalilima mdera lomwelo la Nkanda m’boma la Mulanje. Yemwe watumiza nkhaniyi wati masiku apitawo mderalo munafika njonda zachilendo zitatu pagalimoto ya pick up kwinaku zikumwaza mipukutu ya ndalama. Njondazo zomwe zinatchena kwambiri zimaitanila ana kuti atenge ndalamazo ndikugulira zomwe akusowa pamoyo wawo. Koma mikoko yogona kuzanso makolo awanawo anachita jenkha ndi zomwe njondazo zinkachita. Mwa zina njondazo zimangoponya ndalamazo osaima ndi sizinafototokoza komwe zinachokera komanso cholinga chawo pomwaza ndalamazo. Apo makolo analanda anawao ndalamazo ndikuzitentha. Pakadali pano, anthu mderalo aima mitu kamba ka zinthu zachilendozo.


M’busa wina wasokoneza nkhosa zake zomwe amazitsogolera pa mpingo wina kwa Chigalu m’boma la Blantyre. Nkhaniyi ikuti kumeneko kuli m’busa wina yemwe wakhala akutsogolera mpingo wake mwa luntha. Anthu ambiri akhala akuyamika m’busayo kamba ka mau ake achikoka komanso ulaliki wabwino. Mwa zina m’busayo wakhala akusala chakudya komanso kupita kuphiri kukachita mapemphero apadera. Monga mwa chizolowezi tsiku lina anatengana ndi mmodzi mwa amai ampingo wake ndikupita kuphiri kuti akamupemphelera maiyo. Koma ali makti mwamapemphero kuphiriko anthuwo anagwa mchikondi mpaka kuchita za dama. Koma ali mkati mogawana chikondi kumalownso kunatulukira anthu enanso kudzachita mapemphero omwe anapezerela awiriwo ali mbulanda. Koma atazindikira kuti pamalopo pafika anthu ena m’busayo analiyatsa liwiro la mtondo wadooka kusiya mkaziyo pamalopo. Koma pothawa mk’busayo anatola chitenje cha maiyo mmalo mwa buluku lake. Ndipo atadzindikira kuti wavala chitenje anabwerera pamalopo nkuyamba kuchonderela anthuwo kuti asafalitse nkhaniyo kwa anthu ena. Ndipo anthuwo adalamula m’busayo kuti awaptse chindaputsa cha ten thousand kwacha kamba koyalutsa mpingo wake. Pakadali pano m’bussayo akuyenda ngati nkhuku yonyowa kamba koti anthu adziwa kuti m’busayo ngwa mumchuno.


Mnyamata wina m’dera la MFumu Msakambewa mboma la Dowa waimitsa mitu mikoko yogona chifukwa cha khalidwe lake lokonda kukwatira amayi achikulire. Nkhaniyi ikuti m’nyamatayo yemwe ali ndi zaka 32 ndi okonda kukwatirakwatira koma vuto lalikulu ndi loti amayi omwe amakwatirawo ndi achikulire osayerekeza ndi msinkhu wake. Poyamba mnyamatayo akuti anakwatira mayi wina wa zaka makumi asanu ndi ziwiri ndipo banjalo litatha anakwatira wina wa zaka 55 koma banjalo linathanso patangotha zaka zochepa. Anthu akamufunsa cholinga chake pokwatira amayi achikulire akumayankha kuti akufuna kuti anthu achikulire nawo azidya zonona zomwe amadya achinyamata komanso akuti chikuni chakale nchimene chimasunga moto. Masiku apitawa mnyamatayo akuti wakwatiranso mkazi wina wachitatu, ameneyo ndiye akuti zanyanya chifukwa choti ali ndi zaka zopitilira makumi asanu ndi limodzi. Pakadali pano anthu ambili m’mudzimo ati sakumvetsa cholinga chenicheni cha mnyamatayo pokwatira amayi achikulire pamene m’deralo muli amai ambili amsinkhu wake omwe akusowa mabanja. Anthu ambili m’deralo ati nkutheka kuti mnyamatayo ali ndi vuto ndiye akuopa kuyaluka akakwatira mtsikana.

 

Mwamuna wina wayaluka mdera la Kadewere m’boma la Chiradzulo. Nkhaniyi ikuti mderalo muli mwini mbumba wina yemwe wakhala akuchitira zamatsenga mbumba yake yomwe koma osamudziwa. Mwachitsanzo mmodzi wa zizukulu zake wakhala akudwa kwa nthawi yaitali ndithu. Ndipo iye amalodza chala mkamwini wina yemwe ndi khumutcha pakhomopo akuchitira zamatsenga mbumbayo. Koma masiku apita mwana wa baja lina pakhomopo anadwala mwadzidzidzi. Makolo a mwanayo atathamangira kwa katakwe wina wazisamba yemwe adawapatsa mtela kuti akawaze pakhomopo. Atawadza makhalawo usiku wosatira anaona chinthu chachilendo chili pakhonde la nyumba yomwe munali mwana wodwalayo. Apo bambo wabanjalo anawaza chinthucho mankhwla ena omwe anatenga kwa ng’anga ija monga adamuudzira. Mkamwiniyo anadabwa kuona kuti chinthucho ndi mwini mbumba yemwe wakhala akuloza chala banja lina kuti ndilo likutha anthu pakhomopo. Panthawiyo mwini mbumbayo ati anali ndi maoneke achilendo monga kusololoka zala komanso milomo ndipo anali mbulanda. Pakadali pano mwini mbumbayo akuyenda zamadulira.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter