You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma11/04/15

11/04/15

Written by  Newsroom

Njonda ina iba mabelo afodya
Njonda ina ya m’mudzi mwa Bwananyambi m’boma la Mangochi yathawa anthu ataituluki kuti inaba mabelo a fodya kwa mu mlimi wina.

13
April

Nkhani ikuti poyambilira mkuluyu anadwala ndipo anapita ku chipatala china komwe anapeza bwino. Kenaka njondayo imakhala kwa mchimwene wake kutauni mpaka nthawi yonse yomwe anthu anamalima. Koma tsiku lina anayimba foni ku mudzi komwe anaudzidwa kuti m’bale wake wakolola fodya wambiri. Iye ananyamuka usiku ndikukafika ku nyumba kwa m’bale wakeyo komwe ananyamula mabelo awiri pa njinga ndi cholinga choti akatamuke mofulumira. Koma akutuluka ku mpandako anangoti gululu ndi mkazi wake waku nyumba imene amabayo, Pamenepa njondayo inaliyatsa liwiro la mtondo wadoka mkusiya njinga ndi mabelowo. Maiyop anakuwa koma mkuluyo anali atatha mtundu koma mkuti maiyo atamuzindikira kuti anali malume ake a mwamuna wakeyo. Usiku omwewo anthu atapita kuti akamugwire sanamupeze ndipo zikumveka kuti wathawira ku Mozambique. Pakadali pano nyakwawa ya m’muzimo yachenjeza kuti ithana ndi aliyense angapezeke akusowesa mtendere pa nkhani ya umbanda ndi umbava.Akwatira mkazi oyendayenda kusiya mkazi ndi ana
Anthu okhala ku Namiyasi m’boma la Mangochi ati akudabwa ndi zomwe wachita mkulu wina posiya mkazi wake yemwe anaberekerana naye ana asanu ndikukakwatila mtsikana wina woyendayenda. Nkhaniyi ikuti mkuluyo akugwira ntchito yolondela pa malo ena omwera mowa mderalo . Ndipo tsiku lina pa malopo anabwera mtsikana wina kuchokera ku Monkey-Bay kuti adzasangakltse anthu pa balapo. Koma atalezera analowa mnyumba yomwe amagona mkuluyo ndikukakamiza kuti achite naye zachiwerewere . Pamenepa mkuluyo anatengeka mpaka anachita naye zadama . Mawa kutacha anthu awiriwo anathawisana mkupita ku Monkey-Bay. Mkazi wa mwamunayo atamva nkhaniyi anamusatila koma mwamunayo anakanitsisa kuti sabwerela ku banja lake ndipo afera m’manja mwa mtsikana oyendayendayo. Ndipo mai wa anawo anakayitula nkhaniyi ku mpingo koma atamuyimbila lamya mkuluyo iye anakana kuti sasapondanso ku banja la analo. Pakadali pano nyakwawa ya m’mudzimo yayitanitsa mkuluyo chifukwa choti maiyo ndi anawo akusowa chisamaliro ngakhale anthu ena akunena kuti chosamva anachiphikira m’masamba.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter