NJUCHI ZISOKONEZA MWAMBO WA MALIRO Featured

Written by  Zam'maboma

Mwambo wa maliro unasokonekera m’dera la Mfumu Kwataine mboma la Ntcheu chifukwa cha njuchi zomwe zinabalalitsa anthu ku manda. Nkhaniyi ikuti m’mudzimo munachitka maliro a munthu wina odziwika bwino ndipo monga mwa mwambo anthu anasonkhana pa nyumba ya siwa. Pa tsiku loika malirowo, adzukulu analawira kokumba manda ndipo atamaliza ntchitoyo anatumiza uthenga kumudzi. Mwambo wakukhomo unayenda bwino lomwe mpaka anthu kunyamula zovutazo ulendo wakumanda. Koma mwambo uli mkati kumandako, njuchi zomwe sizinaoneke komwe zachokera, zinayamba kubalalitsa anthuwo ndipo akuti ambili mwa iwo anavulala pothawa komanso ena kulumidwa ndi njuchizo. Yemwe watumiza nkhaniyi wati panatenga nthawi yaitali njuchizo zikuulukabe kumandako ndipo apa mikoko yogona itagundana mitu, inangoganiza zokaika malirowo pakhomo pa mkuluyo. Pamenepa amuna ena olimba mtima anavala zodziteteza mnthupi kuti asalumidwe ndi njuchizo, nkukatenga bokosi la malirowo kubwelera nalo kumudzi. Kunyumbako, mwambo woika m‘mada malemuyo unayenda bwino lomwe popanda chovuta zomwe zachititsa kuti anthu ena aganizire malemuyo kuti anali wokhwima.

Get Your Newsletter