18/05/19

Written by  Zam'maboma Desk

Mayi wina kwa Khongoni ku Lilongwe wadabwitsa mikoko yogona atalanda chofunda agogo ake omwe akudwala kwambiri. Nkhaniyi yati mayiyu yemwe agogo ake apunthika kwamiyezi ingapo tsopano, anapita kunyumba kwa agogo akewo kuti akatenge bulangete lomwe agogo akewo akhala akufunda chiyambireni kudwala.Iyeyo akuti wachita izi ati kuchitira kuti agogo akewo asafe akufunda bulangetelo lomwe akuti amalifuna kwambiri.Mayi wodabwitsayi atalowa mnyumba momwe agogo ake akuganomoyo anauza amayi omwe amadwazika matendawo kuti akufuna atengepo chofundacho chifukwa ndichamtengo wapatali.Amayi ena anamkokera kukhonde kuti amudzudzule koma iyeyo anakanitsitsa kuti sangaimve chifukwa gombezalo ndi la Joni.

Get Your Newsletter