18/05/19

Written by  Zam'maboma Desk

Mkulu wina kwa Simon ku Dedza wadabwitsa wanthu atakaniza chakudya amfumu am’mudzimo paukwati wa mwana wake.Yemwe watumiza nkhaniyi wati, bambo wina yemwe mwana wake anapeza mwayi wabanja anachititsa ukwati ndipo monga mwa mwambo anthu ammudzimo anabwera kuti adzasangalale ndikukhwasula. Koma akuti zinadabwitsa wanthu bambo wa namwaliyo atatulukira kunyumba yomwe kumachitikira mwambo mwamavuvu kwinaku akuyankhula moopseza kuti amfumu ammudzimo asapatsidwe chakudya ati poti adamumana mowa tsiku lomwe iye adalibe ndalama.Anthu ena amaona ngati mkuluyu akuchita macheza poti inali nthawi yachisangalalo,ndipo palibe yemwe anamumvera. Koma anthuwo anadabwa poona bambo uja akulanda zakudya zomwe amayiwo anakonzera mfumu ya mmudzimo diso lili pamtunda.Posafuna kukangana naye,amayi aja anamulekera mbalezo zomwe zinachititsa anthu ena,kuphatikizapo mfumuyo kufutuka pamalopo. Anthu ena akuganiza kuti bamboyu anachitita izi kaamba kolodzera ndipo ena akumumvera chisoni kuti mwina mfumuyo,ikhoza kumuchotsa mmudzi mwake.

Get Your Newsletter