07
September

AMUNA AATIDZIMULANA

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 4588 times

Amuna ena kwa Nkalo m’boma la Chiradzulu aatidzimulana kwambiri m’modzi mwa iwo atadzudzula mzake kuti wamupininga kuti njerwa zake zomwe anatentha zisapsye bwino.

Nkhaniyi ikuti amunawo ndipa chinzawo ndipo onse amaumba ndikugulitsa njerwa. M’modziyo ndiye anayambilira kutentha uvuni wake ndipo zinaoneka kuti zinamuyendera kaamba koti njerwa zakezo zinapsya bwino kwambiri ndipo zinayendanso malonda. Koma mzakeyo amafuna kuti aumbe njerwa zambiri kuti akagulitsa agule mthuthumula kuti adzichitanso bizinezi ya kabaza.  

Ngakhale anali ndi maganizo amenewa, analibe nkhuni zokwanila ndipo mzake uja anamuchenjeza kuti akachita masewera njerwazo sizipsya.

Koma iye anamutsimikizira mzakeyo kuti awonjezera nkhuni ndipo anaguladi nkhunizo, koma atatentha uvuniwo kunapezeka kuti zambiri mwa njerwazo sizinapsye.

Mzake uja ataona izi, mocheza anamuuza kuti achikhala adamvera malangizo ake, zimenezo sizikadachitika. Chifukwa cha mkwiyo mzakeyo adaona ngati akumunyoza ndipo adayamba kusinthana mau a mnyozo mpaka kukwiyitsana nayamba kutikitana.

Amzawo ena omwe amachita nao bizinezi ya njerwayo ndiwo anawaleletsa. Pakadali pano amunawo akuti ayanjana ndipo winayo wamuuza mzakeyo kuti amuthandiza kumanganso uvuni watsopano kuti atenthenso njerwa zosapsyazo.

07
September

Mai wina ku Chilinde mu mzinda wa Lilongwe amuthamangitsa pa lendi chifukwa chosintha amuna ngati Malaya.

Malinga ndi mtolankhani wathu kumeneko, maiyo yemwe ndi wosakwatiwa koma amagwira ntchito pa kampani ina, anafika m’deralo kumayambiliro kwa chaka chino.

Pa pulotipo pali nyumba zingapo ndipo mwini malowo amakhalanso pomwepo.

Poyamba mwini nyumbazo analibe vuto lirilonse ndi maiyo koma patapita miyezi ingapo adayamba kuonetsa mawanga ake.

Nthawi zambiri makamaka kumapeto kwa sabata, maiyo yemwe amakhala ndi mtsikana wa ntchito komanso ana ake awiri, amafika ku nyumbako ndi mwamuna komanso ataledzera.

Koma chakhumudwitsa kwambiri landlord nchakuti amasinthasintha amunga ngati malaya. Pa mwezi akuti amatha kusintha amuna atatu.

Chifukwa cha ichi, mwini malowo anamuyitana namulangiza kuti pa malo pakepo sipochitila uhule kaamba koti akuopa kuti tsiku lina amunawo akadzakumana ku nyumbako kungadzachitike nkhondo.

Ngakhale analonjeza kuti sadzibweretsanso amuna ku nyumbako, maiyo akuti pano ndiye wangomasuliratu mabuleki. Chifukwa cha ichi, mwini nyumbayo wamuuzilatu kuti afune kwina kokhala kaamba koti mwezi uno ndi omaliza kukhala pa puloti pakepo.

07
September

Mwambo wodalitsa ukwati walepheleka pa tchalichi china ku Chigumula mu mzinda wa Blantyre zitadziwika kuti mkwati ali kale pa banja ndi mkazi wina.


Nkhaniyi ikuti mwamunayo amakhala ndi banja lake kwa Kuntaja ku Blantyre komweko. Tsono masiku angapo apitawa njondayo inatsanzika mkazi wake kuti ikupita ku mudzi ku Mwanza kukaona mai ake adwala.


Koma pa nthawiyo nkuti maiyo atatsinidwa kale khutu kuti mwamuna wakeyo akukadalitsa ukwati ndi mkazi wina ku Chigumula kotero kuti anagwirizana ndi abale ena kuti amuleke mkuluyo apite ndikuti adzakavundule madzi tsiku la ukwatilo.

Tsikulo litafika, mkazi uja anatengana ndi mwana wake, abale komanso amzake ulendo waku Chigumula. Atafika ku tchalichiko anakhala nawo mgulu la anthu omwe anafika kukaonelera mwambowo.


Pa nthawiyo mwamuna uja atakhala kutsogolo ndi mkazi watsopanoyo kudikila kuti abusa ayambe ntchito yao yodalitsa ukwati monga zikhalira.  

Posakhalitsa mkazi wake uja anangodzambatuka pamene anakhala nalunjika kutsogolo akuuza abusa kuti asadalitse ukwatiwo kaamba koti mwamunayo ndi wake ndipo kuti ali naye ana angapo.


Apatu njonda ija inangoti zolii kulakalaka pansi patatseguka kuti alowepo. Mai uja atapeleka umboni wake, abusa ndi akulu a mpingo anatsimikiza kuti mkuluyo ali kale pa banja ndipo anauza anthu kuti sadalitsa ukwatiwo kotero kuti anthu onse omwe anali mkachisimo anayamba kubalalika, ena akumvera chisoni akwatiwo pamene ena amati zachitika bwino kuti atambwali ena aphunzirepo.


Pakadali pano mkuluyo akuti sanafikebe ku nyumba kwake kwa Kuntaja.

01
September

Mayi wina ku Nguludi Turn-off, amuvumbulutsa pathengo, akuchita zadama ndi mlonda wina.

 Nkhaniyi ikuti mayiyo tsiku ndi tsiku, amatsanzika mwamuna wake chakumbandakucha kuti akupita ku madzi ndipo pozindikira vuto lamadzi m’deralo, mwamunayo samawiringula koma kulolera kuti akatunge madziwo.   

Izitu zakhala zikuchitika kwa nthawi yaitali koma mwamunayo samadziwa kuti nthawi zina mkazi wakeyo amakhala akukakumana ndi chibwenzi chake chomwe chimalondera thanki ya madzi m’phiri lina kumeneko.

Ndiye poti chozemba chidakumana nchokwawa, patsikulo anatsanzikanso chimodzimodzi kuti akulawira kukatunga madzi koma chonsecho akukakumana ndi mlondayo.  
 

Tsono amayi ena anayi omwe analawira ku msika kwa Kanje anamuona mayiyo akuchita zadama ndi mkuluyo pa thengo.

Apatu sanalimbane nazo, koma kungotola miyala nkuyamba kuwagenda. Pamenepa awiriwo anavumbuluka ali mbulanda nkuthawa pamalopo, mwamunayo buluku liri m’manja.

Amayiwo atabwerako ku msikako anayamba kufalitsa nkhaniyi mpaka mwini mkaziyo inamupeza.  Pakadali pano banja la mayiyo lasokonekera pamene mlondayo akuyenda champeni, anyamata omwe ndi achibale a mwini mkaziyo,  atamuchenjeza kuti amukuntha  akakomana naye.Page 1 of 155

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter