01
November

01/11/17

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 6678 times

Mfumu ina igulisa mitengo ya kumanda

Anthu a kwa kalimanjira one kwa sub TA mkutumula, mboma la Ntcheu ati ndi okhumudwa ndi zomwe mfumu yawo ikuchita podula ndi kugulitsa mitengo ya kumanda mwa chisawawa.

31
October

31/10/17

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 5704 times

Ndeu ibuka pakati pa mwini mkazi ndi wa chibwenzi

Ndeu ya fumbi inabuka mdera la KACHECHE ku Mzimba pakati pa mwini mkazi ndi mwamuna wachibwenzi.

30
October

30/10/17

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 3673 times

Awapezelera ku malo ogona alendo

Mayi wina kwa Kamphata mboma a Lilongwe waona zakuda atamuyendetsa mbulanda pamene anamupeza ali ndi mwamuna wina ku malo ena ogona anthu apaulendo.

27
October

27/10/17

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 7217 times

Anyanyalira mwamuna ana atatu
Mai wina wapa mudzi wa Kambalame kwa Likoswe m’boma la Chiradzulu akumulozerana kamba konyanyalira mwamuna wake ana atatu. Nkhaniyi ikuti masiku apitawa mwamuna wina pa mudzipo anayambana ndi mkazi wake pa nkhani zodziwa awiriwo. Kamba ka izi awiriwo amagona zipinda zosiyana. Koma masiku apitawa mwamuna komanso mikoko yogona pa mudzipo anagwira pakamwa kuona kuti maiyo ndi woyembekezera. Atamupha ndi mafunso ndi pamene amaulula m’maso muli gwa! kuti pathupipo ndi pa kam’nyamata kena komwe ndi kavenda pa msika wapa Kanje m’bomalo. Mikoko yogona yati ubwenzi wa awiriwo unafumbira kamba koti maiyo naye amagulitsa malonda ake pa msikapo. Pakadalipano banja la awiriwo lathera ku bwalo la anyakwawa pamaso pa ankhoswe a mbali ziwirizo. Naye vendayo wati salola kusiyana naye maiyo kotero kuti wamuchitira lendi nyumba pa msika wapa Kanje pomwepo. Anthu ambiri pa mudzipo akumuseka maiyo posiyana ndi mwamuna wa msinkhu wake ndikukwatiwa ndi kam’nyamata.

 

Amangilidwa mumtengo pa maliro

Mwamuna wina wapa mudzi wa Ntepere kwa Likoswe m’boma lomwelo la Chiradzulu anam’mangilira ku mtengo mpaka mwambo wonse wa zovuta kutha atampezelera akupapira bibida maliro a mai wake ali m’nyumba. Watitumizira nkhaniyi wati mai wina amadwala pa mudzipo ndipo matendawo atakula mwa tsoka maiyo anatsamira mkono m’chipatala china momwe anamugoneka m’bomalo. Uthenga wa zovuta utakafika ku mudzi achibale anakanyamula thupi la malemuyo kupita nalo ku mudzi pokonzekera mwambo woika m’manda. Ndipo malirowo ali m’nyumba anthu ena anadabwa kupezelera mwamunayo yemwe ndi mwana woyamba wa maiyo akupapira bibida pamodzi ndi anzake.Anthuwo anakadandaula nkhaniyi kwa anyakwawa kudzanso mikoko yogona omwe analamula kuti akamududuluze ndikum’mangilira ku mtengo ku manda kufikira mwambo wonse watha. Pa nthawiyo mowa wonse unakungunuka ndipo anafiira maso monga mkuta. Ndipo palibe munthu ndi m’modzi yense yemwe anamumvera chisoni.

 

Apilikitsidwa kamba ka chimasomaso

Mkamwini wina amupitikitsa ku banja ku chikamwini pa mudzi wa Joshua m’boma la Balaka kamba ka chimaso-maso. Nkhaniyi ikuti mkazi wa mkamwiniyo anapita ku chipatala kukadikilira mwana wao wa mkazi yemwe amayembekezera. Mkamwiniyo malinga thonje lomwe wapha chaka chino aamaitanira m’nyumbamo akazi achibwenzi. Anthu ena augogodi anatumiza uthenga kwa mkazi wake ku chipatala yemwe atafika pakhomopo analusa mpaka kulamula mwamunayo kuti amange zovala zake azipita kwao. Pakadalipano mwamunayo wachokadi pakhomopo ndipo wapita kukagwira mwendo kwa mkazi wake woyamba. Naye mkazi woyambayo wanenetsa kuti mwamunayo akapitiriza khalidwe lake lachimaso-maso amupitikitsanso pakhomopo.

 

Athawitsana ndi mamuna

Mai wina wochita geni yogulitsa zitumbuwa pa msika wa Magomero m’dera la Mfumu Chilikumwendo m’boma la Dedza wathawitsana ndi mwamuna wa golosale. Nkhaniyi ikuti mkaziyo yemwe anali pa banja amachita geni yogulitsa zitumbuwa pa msikapo. Ndipo maso ali mwamba mkaziyo anagonekera khosi mwamuna wina wa golosale yemwenso ali ndi mkazi wake pofuna kudya nawo chuma. Makolo a mkaziyo ngakhale amadziwa bwino lomwe kuti ali ndi ana atatu ku banja kwake anamulolabe kulowelera mwamuna wopatayo. Pakadalipano mwamuna wa golosaleyo wachitira lenti nyumba mkaziyo. Mwamuna woyamba wa mkaziyo akupukusa mutu wopanda nyanga poganizira chikondi chomwe mkaziyo amaonetsa pa nthawi yomwe anali ndi chuma. Izi zikupherezera mwambi uja wakuti ukakhala pa msana pa njovu usamati kunja kulibe mame.Athyola mwendo wa galu

Mwamuna wina yemwe amachita bizinesi yakupha ndikugulitsa nyama ya mbuzi pa nyumba pake m’boma la Salima amulipitsa 1-thousand 500 Kwacha kamba kothyola mwendo wa galu yemwe amamuvutitsa pamene amasenda mbuzi yamalonda. Nkhaniyi ikuti wabizinesiyo tsiku lina monga mwa chizolowezi anakagula mbuzi ya malonda yomwe amasenda pa nyumba pake. Pa nthawi yomwe amasenda mbuziyo agalu anali nyomi pa malowo ndikumavutitsa wabizinesiyo. Ndipo potopa ndi zimenezi wabizinesiyo anatola mwala ndikugenda agaluwo ndipo anathyola mwendo m’modzi mwa agaluwo yemwe analira mokodola mbuyache. Mwini galuyo anafika pa malowo malinga ndi momwe analilira galuyo. Mwini galuyo atafika pa malowo analamula wabizinesiyo kuti amulipire ndalama zokwana 1-thousand 500-Kwacha kamba kothyola mwendo wa galu wake. Wabizinesiyo anakana kulipira ndalamazo ndipo mwini galuyo anakamutulira wabizinesiyo galu wothyoka mwendoyo kuti amugulire wa lunga. Nkhaniyi inakafika ku bwalo la anyakwawa lomwe linalamula wabizinesiyo kuti alipire.

Page 8 of 147

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter