You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma13/05/15

13/05/15

Written by  Newsroom

Akolola chimanga cha eni
Mwamuna wina wapa mudzi wa Ndalama kwa Chitera m’boma la Chiradzulu yemwe wakwatira pa mudzi wa Malinga m’bomalo akuyenda wera-wera ngati wataya singano atamugwira akukolola chimanga m’munda mwa mbale wake.

14
May

Nkhaniyi ikuti mwamuna amamvetselera nkhongono kotero kuti kulima kumamuvuta kwambiri . Pamene anthu amakangalika ndi ntchito zaku munda iye amangokhalira kuyenda bawo. Kamba ka izi minda yonse yomwe mwamunayo ali nayo wachititsa lendi kwa anthu ena ndikutsala ndi kachikunda kamodzi kokha komwe amakalasapo. Pakadalipano, mwamunayo akungoyenda ngati munthu wozungulira mutu kamba koti abale ake onse akumukalasila makala a moto kamba ka khalidwe lake lakuba. Kamba ka izi mwamunayo kukacha akungokhalira kupemphetsa mowa wa ntonjani kwa mai wina yemwe amacheza mowawo pa mudzipo.


Abeledwa njinga akupemphera mu nzikiti
Mwamuna wina wapa mudzi wa Napawa kwa Bwananyambi m’boma la Mangochi akulilira ku utsi munthu wina atamubera njinga yake yakapalasi pamene amapemphera mu mzikiti wina m’deralo. Nkhaniyi ikuti, Lachisanu lapitali mwamuna wina anachoke ku mudzi kwao ndikupita kukapemphera pa mzikiti wapa mudzi wa Kaipa m’bomalo. Popita ku mzikitiko mwamunayo anakwera njinga yake yakapalasi, ndipo atafika anaiyedzeka pa mtengo wina kunja kwa mzikitiwo pomwenso panali njinga zakapalasa za anthu ena. Munthu wina yemwenso anadzizimbaitsa povala mkanjo analowa mu mzikitimo, koma mapemphero ali mkati mbalayo inatuluka msanga mu mzikitimo ndikuthamangira pomwe anthu anayerdzekapo njinga zawo ndipo anathamangira kutenga njinga ya mkuluyo kamba koti imaoneka kuti ndi yatsopano. Mwini njinga yobedwayo atatuluka mu mzikitimu anayesera kufufuza njinga yake pomwe anthu anayedzeka njinga zawo koma sanaipeze. Atafufuza kwa anthu ena anamuuza kuti anaona mkulu wina akuchoka mu mzikitimo mofulumira ndipo atakwera njingayo anaipalasa mwa ithyoke -ithyoke kuli kuthawa. Apa mwini njingayo misozi inalengeza m’maso ndipo nthawi yomweyo maso anafiira monga mkuta kudandaula njinga yake. Nkhaniyi anakaitula kwa akulu-akulu apa mzikitipo komanso nyakwawa ya mderalo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter