You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma21/06/15

21/06/15

Written by  Newsroom

Aphuluphuthidwa mpaka kukomoka
Mnyamata wina wa mtauniship ya Ndirande mu mzinda wa Blantyre amukuntha mpaka kukomoka atamupezerela akuba kompyuta mu ofesi ina ku Limbe mu mzinda wa Blantyre.

22
June

Chomwe chinachitika ndi chakuti atate ake a mnyamatayo omwe amakhala mtauniship ya Ndirande ku Blantyre anachita lenti ma ofesi ena ku Limbe komwe amagwirako ntchito zawo, ndipo pa zifukwa zina anatseka maofesiwo koma sanachotse wina mwa katundu wao. Kamba kozisaka m’nyamatayo anaganiza zokaba compyuta ku ofesi ya atate akewo, ndipo anasiya makolo ake akugona usiku ndikuzembetsa makiyi amu ofesiyo ndipo atatsekula anaba kompyuta. Koma mwatsoka akutuluka mu ofesiyo anangoti gululu ndi mlonda yemwe amayang’anila pa malopo, ndipo atamufunsa anangoti kakasi kusowa choyankha. Mlondayo anaimba wenzulo kuitana anzake kuti amuthandize kuthana ndi wakubayo, ngakhale m’nyamatayo analephera kulongosola kuti ofesiyo ndi ya atate ake ndipo amutuma . Koma alondawo sanamve izi kotero kuti anamukuntha ndi zibonga mpaka kusamba magazi. Pamenepa atate ake amafika pa malowo nkuti m’nyamatayo atamuvulaza kwambiri. Pakadali pano mnyamatayo akubula mchitokosi cha apolisi momwe amutsekera kudikira tsiku lokaonekera ku khothi kukayankha mlandu pa nkhaniyi.

 

 

Abindikila nyumba kamba ka manyazi
Mwamuna wina wapa mudzi wa Chikapa kwa Santhe m’boma la Kasungu akubindikira m’nyumba kamba ka manyazi atamugwira m’nyumba ya mwini ndikumulipitsa K50,000. Mwamunayo yemwe ndi mlimi wa fodya wakhala akudololoka ndi mkazi wa mwini ngakhale iye ali pa banja. Mlimiyo wakhala akuvutitsa mkazi wa m’nzake woyandikana naye nyumba kuti akumufuna ubwenzi wa nseri. Koma mkaziyo amakana ndipo wakhala akufotokozera mwamuna wake za nkhaniyi. Mwamuna wa mkazi yemwe amafunidwa ubwenziyo yemwe ali ndi njinga ya moto anagwirizana ndi mkazi wake kuti amulole mwamuna wakubayo kuti afike ku nyumbako. Ndipo tsiku lina n’kachisisila mwini mkaziyo analiza njinga yake ya moto kunamizira kupita ku sitolo zaku Mtunthama. Ndipo sanayende mtundu wautali anakasiya njingayo kwa mnzake nkuyenda pansi kubwelera ku nyumbako. Mkaziyo anaimbira foni mlimiyo kumuitana kuti afike ku nyumbako kamba koti mwamuna wake wachoka. Mlimiyo anali ndi chitsimikizo choti mkaziyo akunena zoona kamba koti wamva ndikuona mwamunayo akuchoka ku nyumbako pa njinga ya moto kamba koti anthuwo ndi woyandikana nyumba, osadziwa kuti mwamunayo anabwelera pansi. Atafika m’nyumbamo mwamuna wakubayo anayamba kucheza ndi mkaziyo nkhani zachikondi. Nthawi yomweyo mwini nyumbayo anachoka ku chipinda chomwe anabisala ndikukankha chitseko chakuchipinda komwe anakapezelera mwamuna wakubayo. Mwini nyumbayo analamula mwamuna wakubayo kuti alipire 50-thousand Kwacha ndipo anatuma munthu wina kukatenga ndalamayo kwa mkazi wake. Zitatero anamusiya koma atamuchenjeza kuti akadzachitanso adzamukhaulitsa.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter