You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma22/06/15

22/06/15

Written by  Newsroom

Akunthana kamba ka ganyu yowaza nkhuni
Anyamata awiri omwe amagwira maganyu pamsika omwe uli kuseri kwa Chipatala cha gulupu mu mzinda wa Blantyre anakunthana mpaka kung’ambirana zovala kamba kolimbirana ganyu yowaza nkhuni.

22
June

Msikawo womwe anthu amagulitsapo zinthu zosiyana-siyana wayandikana ndi nyumba yogona anthu wodikirira odwala pa chipatalacho. Tsiku lina ku m’mawa mayi wina yemwe amadikilira wodwala anaitana m’modzi mwa anyamatawo ndikupatsa ganyu yowaza nkhuni pa mtengo wa 200-Kwacha. Koma pa nthawiyo m’nyamata winayo anangokhala ndipo mwamuna wina wootcha chipisi ku malowo anauza m’nyamata wina yemwe anangokhalayo kuti amuwazire nkhuni pa mtengonso wa 200- kwacha. Koma m’nyamata wina yemwe anamupatsa ganyu poyambayo anakwiya ndi m’nzakeyo ndipo anauza mwini tchipisiyo kuti ganyuyo agwira ndi iyeyo pa mtengo wa 100-Kwacha yokha basi. Mnyamata winayo pomva mauwa sanaimve kotero kuti mkangano unabuka pakati pa awiriwo mpaka kung’ambirana zovala. Anthu ena achifundo analeletsa mkanganowo koma pa nthawiyo nkuti awiriwo akupumira mwamba komanso akutuluka magazi mphuno ndi mkamwa.


Alumbira kusokoneza mapemphero
Mkulu wina wa mpingo pa mudzi wa Kakhobwe kwa Mpando m’boma la Ntcheu wati asokoneza mapemphero pa mpingowo sabata ino. Nkhaniyi ikuti mkulu wa mpingowo adayamba aima kupemphera atasemphana maganizo ndi akhristu anzake pa nkhani zachitukuko pa mpingopo. Kamba ka mvula yamphamvu yomwe yakhala ikugwa mderalo miyezi yapitayi tchalitchicho chinagwa. Ndipo akhristu anagwirizana zomanga tchalitchi chocheperapo . Koma mkulu wa mpingoyo ananenetsa kuti sakugwirizana ndi maganizo womanga tchalitchi chaching’ono. Kamba ka izi mkuluyo anasiya kupemphera. Ndipo masiku apitawa mkulu wa mpingoyo anaganiza zobweleranso ku mpingo kwake. Atakafika uko komiti yapa mpingowo inauza mkuluyo kuti akayambirenso kalasi kamba koti adachoka mu mpingowo. Mkuluyo sanagwirizane ndi maganizowa kotero kuti waopsyeza kuti asokoneza mapemphero a sabata ino ngati anthuwo akulimbikira kuti mkuluyo akayambirenso kalasi. Nawo akhristu eni ake akonzekera kuti wina asasokoneze mapemphero awo sabata ino.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter