You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma23/06/15

23/06/15

Written by  Newsroom

Agwededza mudzi kamba ka chimasomaso
Mayi wina wapa mudzi wa Kamoto kwa Mabuka m’boma la Mulanje, wagwededza mudziwo ndi midzi ina yoyandikana kamba ka khalidwe lake lachimaso-maso.

24
June

Nkhaniyi ikuti maiyo yemwe ali ndi zaka pafupi-fupi makumiasanu komanso wakhala pa banja kwa zaka makumiatatu. Maiyo wakhala akudyetsa njomba mwamuna wake kwa zaka zambiri pomakhala ndi zibwenzi za m’nseri . Mwamuna wa maiyo anatumiza mkazi wake yo ku mudzi kuti azikalima ndikumpatsa ndalama zolimitsira ku munda. Ali ku mudziko maiyo anatailira pomayenda mwa nseri ndi amuna ena . Makolo komanso achibale a mwamunayo atsina khutu waoyo pomufotokozera zomwe amachita mkazi wakeyo ku mudzi. Mwamunayo atafufuza wapeza umboni wotsimikiza kuti mkaziyo akumudyetsadi njomba ndipo wakakatula malata pa nyumba yomwe wamangira mkaziyo. Pakadalipano , mkaziyo akubindikira mnyumba kamba ka manyazi ndi nkhaniyi.

 

 

Athetsa banja la mwana wawo
Makolo ena kwa Dauya m’boma lomwelo la Dedza athetsa banja la mwana wao wa mkazi posakondwa ndi momwe mwana wao amakhalira mokondwa ndi mwamuna wake. Malinga ndi yemwe watitumizira nkhaniyi mpongozi wa mwamuna samasangalala ndi momwe mkamwini wao amakhalira mokondwa ndi mkazi wake yemwe ndi mwana wao pakhomopo. Makolowo anapempha ana awowo kuti aleke kugula nyama ndikumamwa tiyi pakhomo paopo. Makolowo ngakhale ali ndi ziwetu komanso pakhomo pawo ndipa mwana alirenji iwo sakupha chiwetu kuti atsuke mkamwa komanso sakumwa tiyi pakhomo paopo. Malinga ndi momwe mkamwiniyo amakhalira ndi mkazi wake pakhomopo anapangana zoti asamuke ndikukakhala ku malo ena pa mudzi pomwepo.

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter