You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma24/06/15

24/06/15

Written by  Newsroom

Amubwatika kuti amanga naye ukwati
Mai wina wa zaka 32 wapa mudzi wina m’boma la Phalombe akulira mosatonthozeka mnyamata wina wapa mudzi wa Magaleta kwa Mlauli m’boma la Neno atamubwatika kuti akumufuna ukwati ndikuti afike ku mudzi kwa mwamunayo.

24
June

Nkhaniyi ikuti mwamunayo yemwe ali ndi zaka 23 zakubadwa anaimbira nambala ya mkaziyo mwa ngozi. Ndipo akuyankhulana mwamunayo anauza mkaziyo kuti iye ali ndi golosale yodzaza ndipo ndi mwamuna yemwe akufuna mkazi woti amange naye banja. Ndipo anapitiriza kuuza mkaziyo kuti akumufuna kuti amange naye banja. Mkaziyo mosaganizira anakopeka ndi mauwa ndipo anauyatsa ulendo kuchokera kwao ku Phalombe kukafika kwa mwamunayo pa mudzi wa Magaleta. Ndipo atafika uku mkaziyo anafunsa ku nyumba kwa mwamunayo , komwe anthu ena anamulozera. Ndipo anadabwa kuona kuti mwamunayo ndi wokwatira komanso golosale yomwe amati ndi yake ndiya atate ake. Mkaziyo anamutengera ku bwalo la anyakwawa komwe atamupha ndi mafunso anafotokoza nkhani yonse. Anthu ambiri pa mudzipo akudabwa ndi zomwe mkaziyo wachita pothamangira mwamuna yemwe sakumudziwa bwino kuti amange naye banja.

 

Akoloredwa K30,000 pamowa
Mnyamata wina wapa mudzi wa Kanyama m’boma la Dedza walilira ku utsi anzake omwe amamwa nawo mowa m’bara ina pa boma la Dedza atamukolopola K30,000 kamba koledzera. Nkhaniyi ikuti, m’nyamatayo anapita kukagwira ntchito ku Kasosole m’dziko la Mocambique. Ndipo atagwira ntchito uku kwa kanthawi anabwelera kuno ku mudzi, ndipo anafikira kupapira mowa ndi anzake pa boma la Dedza asadafike ku mudzi kwao. Mnyamatayo atadakwa anafika pogona m’baramo ndipo anzake omwe amapapira nawo mowa limodzi anapeza mpata ndikumukolopola ndalama zonse zomwe anali nazo m’nthumba, pa nthawiyo nkuti ali mtulo tofa nato. Kutacha m’mawa m’nyamatayo atapisa mthumba lake la buluka anagwesa msozi uku akufunsa-funsa atsikana komanso anyamata wotumikira m’barayo ngati anamuonera ndalama zake. Anthuwo atanena kuti sanazione mnyamatayo anayamba kupemphetsa ndalama yoti akwelere bus kupita kwao pa mudzi ya Kanyama. Koma m’nyamatayo akupukusa mutu wopanda nyanga kamba koti pamene amapita ku Mocambique adabwereka ndalama ya m’nzake yokwana 5-thousand Kwacha.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter