You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma28/04/15

28/04/15

Written by  Newsroom

Njoka ituluka mu ntondo wa chigayo
Anthu ena ogwira ntchito yagaitsa pa ntchini ku Mtunthama m’boma la Kasungu aona malodza njoka itatuluka mu mtondo wa chigayocho, iwo ali mkati ndi ntchito yao yothandiza anthu.

28
April

Nkhaniyi ikuti azibambowo omwe akhala akugwira ntchito pa ntchiniwo kwa nthawi yayitali tsiku lina anaona malodza pamene anaona njoka ya mamba ikutuluka mu mtondo wa chigayocho koma ili ndi tsitsi kumutu kwake. Mwa zina mwini chigayocho atamva za nkhaniyi anathawa m’mudzimo koma anthu omwe anaona izi akukhalira kukomokakomoka akakumbukira za chilombocho ndipo wina mwa anthuwo amugoneka ku chipatala chifukwa chakukomoka. Malipoti ati anthu ozungulira ntchiniwo agwirizana zoti asamakagayenso pa chigayocho. Mikoko yogona ya m’mudzimo yati ikhala pansi ndi mwini chigayocho kuti afotokoze bwino za nkhaniyi.

 

 

Zodabwisa zichitika mkulu wina atangomwalira
Anthu a mdera la T/A Chimwala m’boma la Mangochi ndiwozizwa kwambiri pa zomwe zinachitika mderalo m’mene bambo wina atamwalira kumene. Nkhaniyi ikuti bambo wina yemwe anali mvula za kale anamwalira mderalo mosadziwika bwino, koma chodabwitsa nchakuti atangomwalira kumene kunayamba mphepo ya mphamvu. Izi zili choncho anthu ena anabwera akuthamanga kudzanena kuti mtengo wina wa m’munda wa mkuluyo unapikuka okha popanda chifukwa chenicheni. Anthu ena mderalo ati sakukayika kuti mkuluyo kutheka kuti anali okhwima pamene ena akuti chifukwa chakuti mzimu wao ndi wamphamvu chifukwa chakumwalira mwadzidzi kuti ena anachita kuwatchera.

 


Banja litha kamba kosinthasintha amuna
Mayi wina wodziwika ndi kukangalika ndi nkhani zopemphera kwa Mkwepu ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre, manja ali ku nkhongo , mwamuna wake atathetsa banja chifukwa cha khalidwe lake losintha amuna. Nkhaniyi ikuti mayiyo yemwe ndiwa ana atatu, anali pa banja ndi mwamuna wina yemwe pakadali pano ali kunja kwa dziko lino. Poti amati wachake ngwachake mayiyo anapalana ubwenzi ndi mnyamata wina wachichepere yemwe amakhala ku Ndilande mu mzinda womweo wa Balntyre , ndipo ubwenzi wao utafumbila , masiku ena amakagona ku Ndirande komweko ponamiza anthu pamudzipo kuti akupita kumudzi. Pali mau oti anthu sabisilana nkhani, anthu ena omwe ngakufuna kwabwino anatsina khutu akubanja kwa bambo wakunjayo ndipo atafufuza anapeza umboni wokwana kuti mayiyo anali pa chikondi ndi mnyamata wachichepereyo. Koyamba anachenjeza mayiyo koma iye sanafune kuva ndipo anapitilirabe ndi khalidwe lake lachisembwere. Anthuwo atatopa ndi khalidwe la mayiyo anadziwitsa mwana waoyo ndipo iye anaimbira foni mayiyo kuti aone kolowera, kuthandauza kuti banja latha. Mayiyo koma ananenetsa kuti anthu ena osamufunila zabwino amuchotsetsa pa banja ndipo ati iye amalalata mopanda manyazi sasiya kudalira kwa ambuye ndipo pakadali pano wapiti kwao ku Zomba.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter