You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma29/04/15

29/04/15

Written by  Newsroom

Akunthidwa ataba mbewu ya tsabola
Anyamata awiri a mdera la Kalumba m’boma la Lilongwe achilapa atamenyedwa kolapitsa chifukwa cha kuba mbeu ya tsabola wa paplika kwa mlimi wina wa mderalo.

29
April

Nkhaniyi ikuti anyamatawa ndiapa chinzache cha ponda apa nane mpondepo koma ndi atsinzina mtole aku deralo. Kwa nthawi yayitali anthu mderalo akhala akuwadzudzula chifukwa cha khalidwe lao lotolatola zinthu zaweni, koma iwo akhala akutseka makutu ku malangizo a anthuwo. Paja amati chingauluke chidzatera , tsiku lina anagwirizana kuti akhaulitse mlimi wina wa paplika pomubera mbeuyo, koma mphuno salota agalu a mkuluyo ndi omwe anavumbulutsa zonse pothamangitsa anthuwo. Mwini nyumba naye anakuwa kuti AKUBA NTHANDIZENI , ndipo anthu anathandiza bamboyo kuthamangitsa anthuwo mpaka kuwagwira. Apa anawamenya mosawamvera chisoni mpaka kupita kuchipatala. Ngakhale zinali choncho anthuwo awalipitsabe chindapusa cha ndalama zokwana 4-thousand –kwacha kuti anthu ena aone polekera.

 


Akanidwa ukwati
Mkuluwina wa mudzi mwa Namitambo mdera la T/A Mpunga walira ching’ang’adza apongozi ake atamukana kuti sakufuna kuti akwatire mwanawawo.palipoti ati mkulu yemwe amatchuka ndi ntchito yobena ma CD anali mchikondi ndi msungwana wina yemwe amafuna kuti amangenaye banja, koma anachita jenkha pa nthawi yomwe amakaonekera kwa mkaziyo atapezanjonda ina yomwenso imafuna kukwatira mkaziyu zomwe zadzetsa mikangano pakati pa msungwanayu ndi mayi ake kamba koti iye akufuna mnyamata wokanidwayo kotelo kuti waopseza kuti angothawitsana ngati mayi akewo amenyetsa nkwangwa pamwala kuti sakumfuna mamuna wakeyo.

 

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter