You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma30/04/15

30/04/15

Written by  Newsroom

Abeledwa K160,000 kwa mkazi waku Mozambique
Mwamuna wina ku Tsangano mboma la Ntcheu akulila usiku ndi usana mkazi waku Mozambique yemwe anakwatila atamukwangwanula pafupifupi K160,000 mkuthawila kwao.

05
May

Nkhani-yi ikuti mwamuna-yo anakwatila mkazi wa ku Mozambique zaka zingapo zapita-zo ndipo anabelekalana naye ana angapo. Mwamuna-yo yemwe akuti ndi mlimi wa mbatatesi amapeza phindu lambiri mpaka kumanga nyumba ya malata kwao. Izi zitatelo mkazi-yo akuti anayamba kuvutitsa mwamuna-yo kuti naye akamumangile nyumba kwao ku Mozambique. Koma mwamuna-yo akuti amangonyala nyaza . Mkazi-yo atatopa ndi kulonjelela za nyumba-yo akuti anaganiza zokhaulitsa mwamuna-yo. Tsiku lina mwamuna-yo akuti anagulitsa mbatatesi zake mpaka kupeza 160 Thousand Kwacha. Ndipo mai-yo yemwe amadziwa pomwe mkulu-yo amabisa ndalama zake akuti anangopita kukakokola-po ndalama zonse mkuubutsa wa kwao. Bambo-yo atazindikila izi akuti analira mokweza ngati mwana. Pakadali pano bambo-yo akuti akusowa mtengo ogwila kamba koti sangatsatile mkazi-yo kwao chifukwa anachita-ko chipongwe. Pakadali pano mkazi-yo akuti amafika pa khomo pake mozemba kudzatenga ana mmodzi mmodzi.


Atenegela kumowa ana malo mophika
Anthu ena akwa ChekuCheku mboma la Neno akukonza zokhaulitsa mkulu wina pamodzi ndi mkazi wake pomatengela ku mowa ana ake mmalo mowaphikila ku nyumba. Nkhani-yi ikuti mwamuna wa mbanja-mo ndi mbiya ng’ambe. Iye akamapita kubibida-ko akuti samasiya ndalama ya ndiwo pa khomo. Mkazi wa bambo-yo atatopa ndi khalidwe-lo akuti anayamba kutsatila mwamuna wake ku mowa komwe onse maledzera. Izi zitachitika kwa nthawi yaitali banja-lo akuti linayamba kumatenga ana ku mowa-ko ati ncholinga choti asamavutike ndi kuphikila ana-wo. Koma ana-wo omwe ndi achichepele akuti akamwa mowa-wo akumatukwana mudzi onse. Anthu ambiri akhala kudzudzula mai ndi bambo-yo za khalidwe lao lomwetsa ana mowa koma banja-lo silikusintha. Pakadali pano guli lina la anthu mdera-lo likukonza zokhaulitsa banja losaganiza za tsogolo la ana awo-lo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter