You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma01/05/15

01/05/15

Written by  Newsroom

Awapezelera nchimbudzi ali mchikondi
Banja lina kwa Chinyama mboma la Kasungu linatsala pangono kutha mwamuna atapezelela mkazi wake mchimbudzi ali mchikondi ndi chibwenzi.

05
May

Nkhani-yi ikuti mai-yo amagwila ntchito pa chigayo china mdera lomwe-lo. Ndipo akugwila ntchito yake anapalana ubwenzi ndi mkulu wina yemwe anapita mdera-lo kukachita bizinesi. Njonda ya bizinesi-yo akuti imakhala mnyumba yoyandikana ndi ya mai-yo. Ndipo tsiku lina awiri-wa akuti anagwilizana zochita chisembwere usiku wa tsiku-lo. Ndipo anthu atagona mai-yo akuti anatuluka mnyumba ngati akukataya madzi koma akupita kukakomana ndi chibwenzi-cho. Awiri-wo akuti anakomana mchimbudzi mwa njonda-yo. Mwamuna wa mai-yo ataona kuti mkazi wake watenga nthawi yaitali ali panja-po anada nkhawa ndipo anatsatila mkazi-yo. Atamufufuza ku chimbudzi cha banja-lo akuti sanamupeze. Apa mwamuna-yo pa modzi ndi anthu ena omwe anawadzutsa anapita kukayangana ku nyumba kwa njonda-yo. Koma kenaka anaganiza mwa changu ndipo atatsekula mchimbudzi mwa njonda-yo ndipo anapeza awiri-wo akuchita chisembwere. Ataona kuti madzi achita katondo njonda-yo akuti inathawa. Ndipo mwamuna ndi mkazi-yo anabwerela ku nyumba kwao. Koma njonda-yo inaganiza mwa changu kuti ikathawilatu mdera-lo ibetsa katundu wake. Apa inapita kwa mwini mkazi-yo modzichepetsa kukapepesa kamba ka ubwenzi-wo ndikulonjeza kuti ipereka chindapusa chili chonse chomwe mwini mkazi-yo anganene. Atadya mutu mwini mkazi-yo analamula mwamuna okuba-yo kuti apereke 10 thousand Kwacha. Mwamuna wa chibwenzi-yo anapereka ndalama-yo ndipo pakadali pano akukhala mwa ufulu monga kale.

 

Mayi wina agwidwa akuba chimanga
Mtsikana wina yemwe wakwatiwa kumene kwa Magwede mboma la Mchinji akubindikila mnyumba kamba ka manyazi atamugwila akuba chimanga. Nkhani-yi ikuti anthu mbiri mdera-lo akhala akukaikika kuti mtsikana-yo ndi otolatola. Mtsikana-yo akuti asanakwatiwe amaba mafuta odzola ndi sopo akapeza mpata mnyumba za anthu ena. Mtsikana-yo atakwatiwa anthu anayesa kuti asiya khalidwe lake la utsinzina mtole-lo. Koma poti wachake mgachake mtsikana-yo akuti amapitilizabe kuba. Masiku ochepa apita-wo mmawa mtsikana-yo akuti anapita kukaba chimanga mmunda mwa banja lina. Ali mmunda-mo eni munda anatulukila ndipo mtsikana-yo ataona kuti zinthu zavuta anathawa. Koma eni munda-wo anazindikila mtsikana-yo ndipo anamutsatila ku nyumba kwake. Atamfunsa nkhani-yi mtsikana-yo akuti anavomera kuti anapita ku munda-ko kukaba. Apa eni munda anauza mtsikana-yo kuti apereke chindapusa cha matumba atatu achimanga. Pakadali pano mtsikana-yo akubindikila mnyumba pomwe akulingalila komwe apeze ndalama yoti agulile matumba atatu a chimanga-wo kamba koti sanalime pomwe mwamuna wake wakhumudwa kwambiri ndi nkhani-yi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter