You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma04/06/15

04/06/15

Written by  Newsroom

Mtsikana oyendayenda atibulidwa pamaliro
Mtsikana wina oyendayenda m’mudzi wa Kapichi m’boma la Thyolo amutibula mpaka kukomoka pa mwambo wamaliro.

04
June

Chinachitika ndi choti mkulu wina anamwalira ndipo abusa analengeza kuti mwambo onse ukachitikira ku tchalichi . Koma ali ku tchalichiko anthu anakhumudwa kuona amai ena awiri atagwetsana pansi uku akumenyena koospya ngakhale kuti mwambo wa misawo umapitilila. Zikumveka kuti m’modzi mwa amai-wo mwamuna wake ali ku John. Koma asanapite ku njako anali pa chibwenzi ndi mai oyendayendayo yemwe anafika pa mwambo wa malirowo. Kenaka mwamunayo anatumizira Foni ya m’manja mkazi wa chibwenziyo koma pali chinthuzi chake. Tsono pa tsikuli la malirolo mkazi mwini mwamunayo nail nao pa mwambo wa malirowo. Koma mkazi oyenda yendayo anayamba kulankhula mwathamo kuti ngakhale mwamunayo ali kunja koma iyeyo ali mgulu la anthu omwe akudya nao chumacho ndipo umboni wake ndi foni yomwe ali nao, yomwe ili ndi chinthuzi chake cha mwamunayo. Nthawi yomweyo mkangano unabuka mpaka mkazi mwini mwamunayo analanda foniyo ndikumutibula mkazi wa chibwenziyo. Anthu ena anatengera mtsikana wachibwenziyo ku chipatala komwe sakupeza bwino chifukwa anavulala kwambiri.


Amuyatsika mabelo afodya 40
Mlimi wina kwa Wimbe m’boma la Kasungu manja ali ku nkhongo mkazi wake wa m’ng’ono atamutethera mabelo makumi anai omwe amati akagulitse ku msika wa fodya. Nkhaniyi ikuti mlimiyo anali ndi akazi awiri. Mwadzidzidzi mkazi wamkuluyo anapita kumudzi komwe kunali mwambo wa chiliza. Pamenepa mwamunayo anayitana mkazi wa mng’onoyo ku mundako kuti akatahndize nao ntchito zina. Koma mwamunayo aku kosamba pa foni ya mkuluyo panabwera uthenga chikondi wa mkazi wina yemwe amapempha chinthandizo cha ndalama zoti zithandizire mwana yemwe wangobadya kumene ku chipatala. Izi zinakwiyitsa mkazi wamng’onoyo ndi atamufunsa mkuluyo anangoti kakasi kusowa choyankha .Ndipo mwamunayo atachoka kupita ku msika mkaziyo anangoyatsa belo limodzi la fodya ndipo motowo unafalikira mpaka fodya yense kuyakha. Pamene amabwera anthu kudzathandiza anapeza zonse zili phulutsa lokhalokha. Mwamunayo atafika analira mosalekeza mpaka kukomoka . M’mene zimachitika izi mkazi wang’onoyo atathawa ndipo sakuoneka komwe ali .

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter