You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma05/06/15

05/06/15

Written by  Newsroom

Akuchimuna akana kupita kuukwati
Makolo a mnyamata wina ku Misesa kwa Kapeni mboma la Blantyre amenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sadzapita ku ukwati wapa tchalitchi wa mwana wao wa mwamuna kumapeto a mwezi uno chifukwa choti akuchikazi akuyendetsa okha zokonzekera zonse za chisangalalo-cho.

05
June

Makolowo alankhula zimenezi atalandila kadi yowaitana ku ukwati wa mwana wao-yo pamene mwanayo sanawauze china chiri chonse. Nkhaniyi ikuti chiyambile pomwe mnyamatayo adagwilizira ukwatiwo akuchimuna akhala akuwasambwadza kuti ati ndi akapunthabuye kutanthauza kuti ndi amphawi. Zimenezi zakwiyitsa kwambiri akuchimuna ndipo ati akudikila tsiku la ukwati kuti akaone munthu yemwe akaimile pa ukwatiwo malinga nkuti iwo ndi anthu woitanidwa ngati alendo. Iwo ati makolo omwe adzawagule ndi ndalama kuti akaimile pa ukwatiwo akadziwikanso pa nthawiyo ndipo ali nchidwi chodziwa komwe akachokele. Koma makolo eni eni a mnyamatayo amenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sakakhala nawo.

 

 

Mkulu wina akumba manda amkazi wake yekha
Mikoko yogona ya m’mudzi wina ku Salima yadzudzula adzukulu okumba manda akumanda kumeneko chifukwa cholamula mkulu wina kuti akumbe yekha manda a mkazi wake misozi ili payi payi ili m’maso. Nkhani-yi ikuti mkulu wina kumeneko amachita bizinezi pamsika wina ndipo pa nthawiyo mkazi wake anamwalira. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi nthawi zambiri mudzimo mukachitika maliro mkulu-yo amatsanzika kuti iye sakhala nawo pa zovuta-zo ndipo akatelo amapita ku msika kumakachita bizinesi yake. Momwe mkuluyu amachita zimenezi adzukulu akuti amangomusiya kuti lidzakwana tsiku lomwe adzamukhaulitse. Mwa tsoka masiku apitawa mkazi wake anamwalila ndipo adzukulu m’malo mopita kumanda aliyense anangokhala kunyumba kwake ena kumacheza pa siwa pomwepo. Atawauza kuti apite kumanda anakanitsitsa mwa mtu wagalu kunena kuti sangayerekeze ndipo anaumiliza mkuluyo kuti akakumbe yekha manda ndipo anayamba kukumbadi mandawo misonzi ikutsikila m’masaya. Atafika mchiuno amuna ena akuti anamulandila ali wefu wefu. Mkuluyo akuti wanenetsa kuti sadzayambilanso ndipo wachimina. Koma nyakwawa zozungulila delalo zadzudzula zomwe anachita adzukulu-wo pa nkhaniyi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter