You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma07/04/15

07/04/15

Written by  Newsroom

Anyamula maliro pa kaliyala
Mikoko yogona yapa mudzi wina ku Mtunthama mboma la Kasungu yaima mitu ndi zomwe wachita m’nyamata wina ponyamula malilo abambo ake pa kaliyala ya Njinga ya moto.Nkhani-yi ikuti m’nyamatayo ali ndi golosale ndipo masiku apitawa wakhala akuyenda ndi mkulu wina wa zitsamba pamene bambo ake amadwala mchipatala.

10
April

Nkhani yomwe inamveka kumeneko inali yoti m’nyamatayo akufuna geni yake ya golosale iyambe kuyenda bwino. Mosakhalitsa bamboo ake aja anamwalila ndipo nkhani inafika kumudzi. Anthu ali mkati mokambilana za momwe achitile kuti malilo afike pa khomo kuchoka kuchipala anthu anangodabwa malilo akufika pa njinga ya moto sing’anga ali pambuyo. Zimenezi akuti zaimitsa mitu mikoko yogona malinga nkuti nkoyamba zotere kuchitika kumeneko. Momwe anthu amatsitsa malilo pa njingayo akuti mwana wa malemuyo amaonetsa kuti sizikumukhudza mkomwe. Panopa amulipitsa 75-thousand Kwacha chifukwa chopeputsa mwambo wa malilo chonsecho kufuna kukhwimila golosale.


Apezeka ndi mfuti 
Apolisi ku Lilongwe agwira mwamuna wina wa zaka makumi atatu a Mackson Sato chifukwa chopezeka ndi mfuti popanda chilolezo. Mneneri wa apolisi m’dziko muno Mai Rhoda Manjolo wati Sato amugwira anthu ena atatsina khutu apolisi kupyolera mu ntchito yomwe ikudziwika kuti Mgwira mbava. Malinga ndi Mai Manjolo, Sato akuti amasatsa malonda amfutiyo ndipo atafufuza anapezadi Sato ali ndi chipolopolo chimodzi komanso mufti-yo. Sato anaulula kuti adapeza mfutiyo pamene adali msilikali wa gulu la Malawi Defence Force - MDF. Mai Manjolo ati Sato akaonekera ku khothi posachedwapa komwe akayankhe mlandu wopezeka ndi mfuti popanda chilolezo. Mackson Sato amachokera m’mudzi mwa Chitawira, m’dera la Mfumu Kuntaja m’boma la Blantyre.

Mbusa achita zachisembwere 
Apolisi mboma la Balaka atsekela mchitokosi mbusa wa Mpingo wina chifukwa chochita zachisembwere ndi mwana wachichepele mpaka kumupatsa pathupi. Mbusayo akuti adauza makolo a mtsiakana wina kuti akufuna azikamupemphelela poopa kuti mwina atha kudwala misala. Pachifukwa ichi makolowo adavomeleza ndipo adalola mwanayo kuti azikakhala kwa abusawo komwe akuti anayamba kumagona naye mowilikiza mpaka kumupatsa pathupi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter