You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma06/06/15

06/06/15

Written by  Newsroom

Akolola chimanga cha eni
Anyamata ena awiri kwa Kwataine m’boma la Ntcheu awakwidzinga atawagwira akukolola chimanga m’munda wa mwini.

10
June

Nkhaniyi ikuti alimi m’mudzi wina m’deralo akhala akudandaula kuti chimanga chikusowa m’minda yao. Nkulu wina yemwe m’munda wake munabedwanso anaganiza zolondela mundawo ndipo tsiku lina anangoti gululu ndi mbava ziwiri zikuba chimanga. Chifukwa choti ndiwa dzitho anakwanitsa kumbwandila anyamata onse awiri mpaka kuwanjata nkuwapititsa kwa anyakwawa. Nkhaniyi itafala m’mudzimo anthu anakondwa kwambiri pozindikila kuti mbala zomwe zakhala zikuba m’minda yao azigwira. Pakadali pano mbavazo azitengera ku polisi.


Ayimitsidwa mu mpingo kamba kamakani
Akhrisitu a mpingo wina ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre ayamba aimisa pa udindo mtsogoleri wao chifukwa chosafuna kumva za ena. Nkhaniyi ikuti kwa nthawi yaitali pakhala palibe mgwirizano weniweni pakati pa akhrisitu ndi mtsogoleri wao pa mpingopo. Akhrisituwo akamudzudzula mtsogoleri waoyo, akuti amalusa kwambiri ndipo amawauza kuti alibe mphamvu zomudzudzulira iye. Koma akhrisituwo atatopa ndi nkhaniyi anapita kukamang’ala kwa Prezidenti wa mpingowo yemwe anapempha nyakwawa ya m’deralo kuti iweruze nkhaniyo m’malo motsata malamulo a mpingo. Ngakhale nyakwawa inayitanila pa bwalo anthu onse omwe nkhaniyo ikuwakhudza, izi sizinaphule kanthu chifukwa choti ena anakana kufika pa bwalopo ponena kuti nkhani zaku mpingo saweruza pa bwalo la mfumu. Tsono poopa kuti mpingowo ungathe, akhrisitu akungana mpaka kuyamba ayimitsa mtsogoleri waoyo mu mpingo. Chimuyimitsile mtsogoleri waoyo, akhrisitu ambiri akuti ayambanso kusonkhana mu mpingowo monga kale. 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter